Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NYIMBO 58

Kufufuza Anthu Okonda Mtendere

Sankhani Zoti Mumvetsere
Kufufuza Anthu Okonda Mtendere
ONANI

(Luka 10:6)

 1. 1. Yesu anatilamula kuti

  tiuze anthu uthenga.

  Amve mawu a Yehova.

  Ankakonda nkhosa za Mulungu.

  Ankazifufuza

  mwakhama tsiku lonse.

  Nyumba ndi nyumba, mumsewu

  Timauza aliyense,

  Kuti posachedwa mavuto atha.

  (KOLASI)

  Tifufuze

  okonda mtendere m’dzikoli.

  Tiwapeze

  Ofuna kupulumutsidwa.

  Tifufuze

  Paliponse.

 2.  2. Tifufuzabe anthu mwa khama.

  Alipo ambiri

  omwe tingathe kuwathandiza.

  Poti timawakonda kwambiri,

  Tibwererekonso

  Tikawalimbikitse.

  M’matauni, ndi m’midzinso,

  Tikapeza omvetsera,

  Timasangalala powaphunzitsa.

  (KOLASI)

  Tifufuze

  okonda mtendere m’dzikoli.

  Tiwapeze

  Ofuna kupulumutsidwa.

  Tifufuze

  Paliponse.