Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NYIMBO 44

Pemphero la Munthu Wovutika

Sankhani Zoti Mumvetsere
Pemphero la Munthu Wovutika
ONANI

(Salimo 4:1)

 1. 1. Yehova ndipempha:

  “Imvani pemphero langa.”

  Zilonda zanga zakula;

  sizipola msanga.

  Kuvutika ndi maganizo

  kwandifoola.

  Ndichitireni chifundo M’lungu

  wotonthoza.

  (KOLASI)

  Ndidzutseni; ndipirire.

  Nkhawa zanga zichotseni.

  Pamavuto n’thandizeni.

  Yehova ndilimbitseni.

 2. 2. Ndikafo’ka Mawu anu

  amanditonthoza,

  Amafotokoza mfundo

  zondigwira mtima.

  Ndidziwe kuti chikondi chanu

  n’chachikulu.

  Ndikumbukire kuti

  n’choposa mtima wanga.

  (KOLASI)

  Ndidzutseni; ndipirire.

  Nkhawa zanga zichotseni.

  Pamavuto n’thandizeni.

  Yehova ndilimbitseni.