Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NYIMBO 4

“Yehova Ndi M’busa Wanga”

“Yehova Ndi M’busa Wanga”

(Salimo 23)

 1. 1. Yehova ndi M’busa wanga;

  Adzanditsogolera.

  Amadziwa zofuna zanga;

  Zomwe ndifunikadi.

  Andipititsa kumsipu,

  Malo otetezeka.

  Mwachikondi chakedi chosatha

  Mtendere wandipatsa.

  Mwachikondi chake chosatha

  Mtendere wandipatsa.

 2. 2. Njira zanu ndi zabwino,

  Zonse n’zachilungamo.

  Zochita zanga nthawi zonse

  Zikulemekezeni.

  Poyenda m’zigwa za mdima,

  Mumandilimbikitsa,

  Sindidzaopatu chilichonse,

  Chifukwa muli nane.

  Sindidzaopa chilichonse,

  Chifukwa muli nane.

 3.  3. M’lungu ndinu M’busa wanga;

  Ndidzakutsatirani.

  Mumandilimbikitsa zedi;

  Zonse mumandipatsa.

  Poti ndinudi wamoyo,

  Ndimakudalirani.

  Kukoma mtima kwanu kosatha

  Muzindisonyezabe.

  Kukoma mtimatu kosatha

  Muzindisonyezabe.

(Onaninso Sal. 28:9; 80:1.)