Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NYIMBO 33

Umutulire Yehova Nkhawa Zako

Sankhani Zoti Mumvetsere
Umutulire Yehova Nkhawa Zako
ONANI

(Salimo 55)

 1. 1. Chonde ndimveni Yehova,

  Musandinyalanyaze.

  Imvani ululu wanga;

  Chonde mundithandize.

  (KOLASI)

  Tulira Yehova nkhawa;

  Iye adzakupulumutsa.

  Amateteza ndipo ndi

  wokhulupirikanso.

 2. 2. N’kanakhala ndi mapiko,

  Ndikanaulukadi,

  Kuti ndibisale,

  ondichitira zoipawo.

  (KOLASI)

  Tulira Yehova nkhawa;

  Iye adzakupulumutsa.

  Amateteza ndipo ndi

  wokhulupirikanso.

 3. 3. M’lungu akatitonthoza,

  Timapeza mtendere.

  Adzatithandiza kuti

  tipirire mavuto.

  (KOLASI)

  Tulira Yehova nkhawa;

  Iye adzakupulumutsa.

  Amateteza ndipo ndi

  wokhulupirikanso.

(Onaninso Sal. 22:5; 31:1-24.)