Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NYIMBO 3

Ndinu Mphamvu Zathu, Chiyembekezo Chathu Komanso Timakudalirani

Ndinu Mphamvu Zathu, Chiyembekezo Chathu Komanso Timakudalirani

(Miyambo 14:26)

 1. 1. O, Yehova mwatiphunzitsa

  za moyo wosatha.

  Zimatikhudzadi mtima

  n’kuphunzitsa ena.

  Nthawi zina timada nkhawa

  chifukwa cha mavuto.

  Chiyembekezo chathunso

  chimatha kuchepa.

  (KOLASI)

  Inu Mulungu ndinu

  mphamvu yathu.

  Inde mumatithandiza.

  Mwalimbitsa,

  chiyembekezo chathu

  timadalira inuyo.

 2.  2. Yehova muzitikumbutsa

  tisamaiwale,

  Zoti mumatithandiza

  kutumikirabe.

  Tikakumbukira mfundoyi

  sitimaopa kanthu.

  Koma timalimba mtima

  pophunzitsa anthu.

  (KOLASI)

  Inu Mulungu ndinu

  mphamvu yathu.

  Inde mumatithandiza.

  Mwalimbitsa,

  chiyembekezo chathu

  timadalira inuyo.