Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 17

“Ndikufuna”

“Ndikufuna”

(Luka 5:13)

  1. 1. Khristu anatisonyeza

    Chikondi chachikuludi

    Pobwera padziko

    Kudzaphunzitsa

    M’mawu komanso m’zochita.

    Ankakonda anthu onse,

    Ankachiritsa odwala,

    Ankathandiza anthu mwakhama.

    Ananena: “Ndikufuna.”

  2. 2. Tikufuna kum’tsanzira

    M’zonse zomwe timachita.

    Timasonyezatu

    Kukoma mtima

    Tikalalikira anthu.

    Anzathu akavutika

    Tiwathandize mwamsanga

    Ndipo amasiye akapempha

    Tizinena: “Ndikufuna.”