Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NYIMBO 145

Mulungu Watilonjeza Paradaiso

Sankhani Zoti Mumvetsere
Mulungu Watilonjeza Paradaiso
ONANI

(Luka 23:43)

 1. 1. M’lungu wathu watilonjeza,

  Paradaiso mwa Khristuyo,

  Adzachotsa uchimo, imfa,

  Misozi ndi zopweteka.

  (KOLASI)

  Paradaiso adzafika.

  Ndipo tikhulupirire.

  Khristu adzakwaniritsa,

  Chifuniro cha Mulungu.

 2. 2. Cholinga cha Mulungu n’choti,

  Yesu aukitse anthu.

  Paja Yesu analonjeza,

  ‘Udzakhala m’Paradaiso.’

  (KOLASI)

  Paradaiso adzafika.

  Ndipo tikhulupirire.

  Khristu adzakwaniritsa,

  Chifuniro cha Mulungu.

 3. 3. Yesu Mfumu, analonjeza,

  Paradaiso padzikoli.

  Tithokoze Atate wathu,

  Kuchokera mumtimamu.

  (KOLASI)

  Paradaiso adzafika.

  Ndipo tikhulupirire.

  Khristu adzakwaniritsa,

  Chifuniro cha Mulungu.