Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NYIMBO 127

Mtundu wa Munthu Amene Ndiyenera Kukhala

Sankhani Zoti Mumvetsere
Mtundu wa Munthu Amene Ndiyenera Kukhala
ONANI

(2 Petulo 3:11)

 1. 1. Ndipereke chani, kwa inu M’lungu

  Pokuthokozani, chifukwa cha moyo?

  Mawu anuwa, amandiunikira;

  Ndithandizeni kuti ndidzifufuze.

  (VESI LOKOMETSERA)

  Ndalonjeza kutumikira inu,

  Mofunitsitsa ndi moyo wanga wonse.

  Ndasankhatu ndekha kutumikira;

  Ndifuna kusangalatsa inu.

  M’lungu n’thandizeni kudzifufuza,

  Ndikhaletu munthu amene mufuna.

  Odalirika, mudzawasamalira;

  Nane ndifuna kusangalatsa inu.