Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NYIMBO 126

Khalani Maso, Limbani M’chikhulupiriro, Khalani Amphamvu

Sankhani Zoti Mumvetsere
Khalani Maso, Limbani M’chikhulupiriro, Khalani Amphamvu
ONANI

(1 Akorinto 16:13)

 1. 1. Khala maso, upirire,

  Ukhalebe wamphamvu.

  Ukhale wolimba mtima,

  Udzapambana ndithu.

  Timvera lamulo la Yesu;

  Tikhalebe kumbali yake.

  (KOLASI)

  Khala maso, khala wamphamvu!

  Limba mpaka mapeto!

 2. 2. Khala maso, usagone,

  Wokonzeka kumvera.

  Uzimvera malangizo

  Ochokera kwa Yesu.

  Mvera malangizo a ’kulu,

  Oteteza nkhosa, n’cho’nadi.

  (KOLASI)

  Khala maso, khala wamphamvu!

  Limba mpaka mapeto!

 3.  3. Khala maso, m’gwirizane

  Poteteza uthenga.

  Ngakhale uzitsutsidwa,

  Uzilalikirabe.

  Tamanda M’lungu mwachimwemwe.

  Tsiku lake layandikira!

  (KOLASI)

  Khala maso, khala wamphamvu!

  Limba mpaka mapeto!