Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NYIMBO 125

“Odala ndi Anthu Achifundo”

Sankhani Zoti Mumvetsere
“Odala ndi Anthu Achifundo”
ONANI

(Mateyu 5:7)

 1. 1. Yehova ndi wachifundo,

  Amasonyeza chifundo.

  Iye ndi wokoma mtima

  Amatisamaliradi.

  Ochimwa omwe alapa,

  Adzamva pemphero lawo.

  Amadziwa ndife fumbi,

  Amatikomera mtima.

 2. 2. Tikachimwa n’kupemphera,

  M’lungu amakhululuka,

  Yesu anatiphunzitsa

  Mmene tingapempherere:

  ‘Mukhululuke zolakwa,

  Za ena takhululuka.’

  Tisasungenso zifukwa,

  Mtendere tidzaupeza.

 3. 3. Tikapatsa ena mphatso,

  Tizisonyeza chifundo.

  Tisamafune kutchuka,

  Koma kungowathandiza.

  M’lungu yemwe amaona,

  Adzakubwezeranidi.

  Achifundo n’ngachimwemwe,

  M’lungu amawakondanso.

(Onaninso Mat. 6:2-4, 12-14.)