Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NYIMBO 119

Tiyenera Kukhala Ndi Chikhulupiriro

Tiyenera Kukhala Ndi Chikhulupiriro

(Aheberi 10:38, 39)

 1. 1. Kale Mulungu ankalankhula

  Kudzera mwa aneneri.

  Lero kudzera mwa Mwana wake,

  Akuti, ‘lapanitu.’

  (KOLASI)

  Kodi chikhulupiriro

  Chathu ndi cholimba ndithu?

  Chikakhala chenicheni,

  M’pamene tingadzapulumuke.

 2. 2. Mosangalala timvera Yesu,

  Tilalikira Ufumu.

  Tilengezabe molimba mtima;

  Anthu amve uthenga.

  (KOLASI)

  Kodi chikhulupiriro

  Chathu ndi cholimba ndithu?

  Chikakhala chenicheni,

  M’pamene tingadzapulumuke.

 3. 3. Talimbatu m’chikhulupiriro;

  Sitidzabwerera m’mbuyo.

  Tidziwa Yehova M’lungu wathu

  Adzatipulumutsa.

  (KOLASI)

  Kodi chikhulupiriro

  Chathu ndi cholimba ndithu?

  Chikakhala chenicheni,

  M’pamene tingadzapulumuke.