Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NYIMBO 118

“Tiwonjezereni Chikhulupiriro”

“Tiwonjezereni Chikhulupiriro”

(Luka 17:5)

 1. 1. Yehova ndifedi anthu ochimwa,

  Zoipa zimadzadza mumtima.

  Pali tchimo lomwe limatikola​—

  Kusowa kwa chikhulupiriro.

  (KOLASI)

  M’tionjezere chikhulupiriro.

  Tikupempha kwa inu Yehova.

  Mwa chifundo chanu m’tionjezere,

  Tikulemekezeni mu zonse.

 2. 2. N’zosatheka kukusangalatsani.

  Ngati sitimakhulupirira.

  Chikhulupiriro chimateteza.

  Ndipo chimatilimbitsa mtima.

  (KOLASI)

  M’tionjezere chikhulupiriro.

  Tikupempha kwa inu Yehova.

  Mwa chifundo chanu m’tionjezere,

  Tikulemekezeni mu zonse.