Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NYIMBO 117

Ubwino wa Yehova

Sankhani Zoti Mumvetsere
Ubwino wa Yehova
ONANI

(2 Mbiri 6:41)

 1. 1. Yehova, M’lungu wabwino,

  Mumatidalitsadi.

  Ndinu wokhulupirika,

  Wabwino m’zinthu zonse.

  Mumasonyeza chifundo,

  Kwa anthu ochimwafe.

  Tilambire inu nokha,

  Tikutumikireni.

 2. 2. Taona ubwino wanu

  Mwa atumiki anu;

  Khalidwe lawo labwino

  Ndi kulalikiranso.

  Mwatipatsa mawu anu,

  Ndi abusa abwino.

  Mutipatse mzimu wanu,

  Zabwino tizichita.

 3. 3. Tikachitirako ena

  Zabwino m’tidalitse.

  Tikhale okoma mtima

  Kwa munthu aliyense.

  M’mabanja ndi mumipingo,

  Ndiponso kulikonse,

  M’tithandize kuchitira

  Anthu onse zabwino.