NYIMBO 105
“Mulungu Ndiye Chikondi”
1. Mulungu ndiye chikondi, wati:
‘Yendani nane.’
Tikonde M’lungu ndi anthu,
Tizichita zabwino.
Tidzasangalala ndithu;
Tidzapezanso moyo.
Tizisonyeza chikondi;
Ngati cha Yesu Khristu.
2. Tikakonda choonadi,
Tidzachita zabwino.
Tikalakwitsa n’kufo’ka;
M’lungu amatidzutsa.
Chikondi chilibe nsanje;
Ndipo chimapirira.
Choncho tizikonda ’nzathu;
Tidzadalitsidwadi.
3. Musalole kuti mkwiyo;
Ukutsogolereni.
Khulupirirani M’lungu;
Adzakuphunzitsani:
Kukonda M’lungu ndi anthu,
N’chikondi chenicheni.
Tizisonyeza anzathu
Chikondi cha Mulungu.
(Onaninso Maliko 12:30, 31; 1 Akor. 12:31–13:8; 1 Yoh. 3:23.)