Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NYIMBO 104

Mzimu Woyera Ndi Mphatso Yochokera kwa Mulungu

Mzimu Woyera Ndi Mphatso Yochokera kwa Mulungu

(Luka 11:13)

 1. 1. Yehova ’Tate ndinu wamkulu,

  Kuposadi mitima yathu.

  Pamavuto mutithandizetu,

  Mzimu wanu utilimbikitse.

 2. 2. Ndife ochimwa, operewera;

  Nthawi zina timalakwitsa.

  Tikupempha mutipatse mzimu.

  Nthawi zonse utitsogolere.

 3. 3. Tikafooka, tikakhumudwa,

  Mzimu udzatilimbikitsa.

  M’tipatse mphamvu tisafooke;

  Tigawireni mzimu woyera.