Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Esitere Anali Wolimba Mtima

Esitere Anali Wolimba Mtima

Pangani Dawunilodi:

 1. 1. Anali wamasiye

  Komanso kapolo.

  Anaphunzira za M’lungu

  Kwa Moredekai.

  Zinthu zinasintha,

  N’kukhala mfumukazi.

  Sanakane, anamvera.

  Nane ndimvere.

  (KOLASI)

  Esitere anali

  Mkazi wolimba mtima.

  Anamveratu Yehova.

  N’chitsanzo chabwino.

  Anadalira M’lungu,

  Anadalitsidwanso.

  Nane ndim’tsanzira,

  Ndidzilimba mtima.

 2. 2. Mfumu inkamukonda,

  Anali wabwino.

  Anali waulemu,

  Anali wanzeru.

  Anatetezatu,

  Mtundu wake usaphedwe.

  Sanakane, anamvera.

  Nane ndimvere.

  (KOLASI)

  Esitere anali

  Mkazi wolimba mtima.

  Anamveratu Yehova.

  N’chitsanzo chabwino.

  Anadalira M’lungu,

  Anadalitsidwanso.

  Nane ndim’tsanzira

  Ndidzilimba mtima. Mukhale wolimba mtima ngati Esitere.