JAY CAMPBELL | MBIRI YA MOYO WANGA
Anandichotsa Pafumbi N’kundikweza Pamwamba
Pomwe ndinkakula, ndinali mtsikana wamanyazi kwambiri. Ndinkakonda kumangokhala m’nyumba kuti ndisaonane ndi anthu ndipo nthawi zambiri ndinkadziona ngati wachabechabe. Sindinkakonda kuonekera kumaso kwa anthu komanso ndinkaopa kuti sangandione ngati munthu wofunika. Dikirani ndikufotokozereni za moyo wanga.
Ndinali mwana wathanzi ndithu. Koma tsiku lina cha mu August 1967, ndili ndi chaka chimodzi ndi miyezi 6, ndinatentha thupi. Mmene kumacha mawa lake, ndinadzuka miyendo yanga ili yofooka. Madokotala a mumzinda wa Freetown ku Sierra Leone komwe tinkakhala, anandipeza ndi poliyo. Matendawa amakhala opatsirana ndipo amapha ziwalo komanso amakonda kugwira ana osapitirira zaka 5. Ngakhale kuti madokotala ankandipangitsa mafizo, sizinaphule kanthu. Pang’onopang’ono miyendo yanga inafookeratu moti sindinkathanso kuyenda. Chifukwa cha chilemachi, nthawi zambiri bambo anga ankakonda kundinena kuti, ‘ngakhale pa mwana siufika.’ Ndinkangodziona kuti si ine kanthu n’komwe chifukwa ndinkadalira kukwawa kuti ndiyende.
Kukula Kwanga Konse, Ndinkangokhalira Kukwawa
Ndinkakhala ndi mayi anga ndipo nyumba yathu inali yoyandikana ndi nyumba za mabanja ena omwenso anali osauka. Ngakhale kuti anthu ena ankandikonda, koma ndinkafunitsitsanso kuti bambo anga azindikonda. Anthu ena ankanena kuti vuto langa si matenda enieni koma nkhani yaufiti. Anthu ena ankauza mayi anga kuti akangondisiya ku nyumba yosamalira ana olumala. Iwo ankanena kuti zimenezi zikanawathandiza kutula chimtolo chondisamalira. Mayi anga anakana zimenezi ndipo ankandisamalira mwakhama.
Chifukwa choti sindikanatha kuimirira kapena kuyenda, ndinkangokwawa basi. Nthawi zambiri ndinkavulala komanso kusupukasupuka chifukwa chodzikwakwaza pansi. Kuti ndisavulale, ndinkavala zovala zokhuthala kwambiri. Ndinkavala masilipasi m’manja kuti ndisasupuke. Patapita nthawi, ndinapeza zipangizo zopangidwa ndi matabwa zomwe ndinkavala kuti ndisavulale m’manja. Kuti ndisunthe, ndinkagwira pansi nkudzikhwekhwerezera kutsogolo. Pochita zimenezi, msana unkandipweteka kwambiri. Ndinkafunika kuchita zimenezi mobwerezabwereza kuti ndisunthe. Zimenezi zinkachititsa kuti ndizimva kupweteka mikono ndi m’mapewa. Sindinkachokachoka pakhomo chifukwa kuti ndiyende chinali chintchito. Sindinkapita kusukulu komanso kukasewera ndi anzanga. Nthawi zambiri ndinkada nkhawa kuti ndidzakwanitsa bwanji kukhala ndekha ngati mayi anga atamwalira.
Ndinkapemphera kwa Mulungu kuti andithandize kuti ndisadzakhale munthu wopemphapempha. Ndinkaona kuti ngati nditakhala pa ubwenzi ndi Mulungu komanso kumamutumikira m’njira imene amafuna, adzandithandiza kupeza zinthu zofunikira. Ngakhale kuti ndinkavutika kuyenda, tsiku lina mu 1981, ndinapita kutchalitchi chomwe chinali m’mbali mwa msewu womwe tinkakhala. Sindinamasuke chifukwa cha momwe anthu ankandiyang’anira. M’busa wa kutchalitchiko sanandilandire n’komwe ndipo anadzudzula mayi anga chifukwa chondilola kukhala pampando womwe ena anali atalipira kale. Ndinaganiza zoti ndisadzapitekonso.
Mmene Ndinadziwira Atate Wanga Wakumwamba
M’mawa wa tsiku lina mu 1984 ndili ndi zaka 18, mwachizolowezi ndinapita kukakhala pawindo la m’chipinda cham’mwamba. Ndikakhala pawindopo ndinkaona zinthu zosiyanasiyana zomwe anthu ankachita tsiku ndi tsiku. Koma kenako ndinaganiza zopita m’chipinda chapansi chomwe nthawi zambiri simunkapezeka anthu. Nditafika ndinakumana ndi amuna awiri omwe ankalalikira khomo ndi khomo. Anandiuza za tsogolo labwino pomwe sindidzakhalanso ndi vuto lomwe ndikulimbana naloli. Anandiwerengera Yesaya 33:24 ndi Chivumbulutso 21:3, 4. Kenako anandipatsa kabuku kokongola kakuti Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! ndipo anandilonjeza kuti adzabweranso kuti adzandiphunzitse zambiri.
Pa ulendo wachiwiri, anandiuza kuti adzabwera ndi mmishonale wina dzina lake Pauline amene anali atangobwera kumene. Anabweradi naye ndipo ine ndi Pauline tinayamba kugwirizana kwambiri ngati mayi ndi mwana wake wamkazi. Mayi anga anandilimbikitsa kuti ndipitirize kuphunzira ndi Pauline yemwe anasonyeza kuti anali munthu wodzipereka, woleza mtima, wokoma mtima komanso yemwe ankafunitsitsa kudziwa mmene zinthu zinalili pa moyo wanga. Iye anandiphunzitsa kuwerenga. Pang’onopang’ono pogwiritsa ntchito Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, anandithandiza kudziwa za Atate wa chikondi amene ndinkafunitsitsa kumudziwa.
Pauline, mmishonale amene anandiphunzitsa Baibulo
Zomwe ndinaphunzira m’Baibulo zinandithandiza kukhala wosangalala kwambiri. Tsiku lina ndinapempha Pauline ngati zinali zotheka kuti ndikapezeke nawo pamsonkhano wa Mboni za Yehova wotchedwa Phunziro la Buku la Mpingo, a womwe unkachitikira pa nyumba ya Wamboni wina pafupi kwambiri ndi pomwe tinkakhala. Pauline anavomera ndipo Lachiwiri la wiki yotsatira, anabwera n’kundidikira kuti ndikonzeke kuti tipitire limodzi kumsonkhanoko. Munthu wina anandiuza kuti ndimuuze Pauline kuti andilipirire galimoto. Koma ndinamuuza kuti “Ayi ndiyenda pogwiritsa ntchito matabwa anga.”
Ponyamuka, mayi anga ndi maneba athu ankangondiyang’anitsitsa mondidera nkhawa. Pomwe ndinkachoka pakhomopo, anthu ena anayamba kukalipira Pauline kuti, “Ukuchita kumukakamiza.”
Mokoma mtima Pauline anandifunsa kuti, “Jay, ukwanitsadi koma?” Ndinamuuza kuti, “Inde, ndi zomwe ndasankha.” Inali nthawi yoti ndisonyeze kuti ndikudalira Yehova. (Miyambo 3:5, 6) Anthuwo ankangondiyang’anitsitsa ndipo nditafika pageti sanalankhulenso kanthu. Nditangotuluka kumpandako onse anayamba kundichemerera.
Ndinasangalala kwambiri ndi msonkhanowo ndipo ndinatsitsimulidwa kwambiri. Ndinalandiridwa mwansangala. Aliyense ankandiona kuti ndine munthu wofunika ndipo ndinali womasuka. Choncho ndinayamba kusonkhana nthawi zonse. Patapita nthawi yochepa, ndinamufunsanso ngati ndingathe kukasonkhana nawo ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova komwe kunkasonkhana anthu ambiri. Ndinali pa umphawi wadzaoneni. Ndinali ndi madiresi awiri okha komanso peya imodzi yokha ya masilipasi. Ngakhale zinali choncho sindinaganizepo kuti abale ndi alongo angandinyoze ndipo ndi mmene zinalilidi.
Kuti ukafike ku Nyumba ya Ufumu, unkafunika kuyenda wapansi nkukafika kumapeto kwa msewu. Kenako n’kukakwera galimoto yopita mmunsi mwenimweni mwa phiri momwe munali Nyumba ya Ufumuyo. Kumeneko abale ankandinyamula m’manja kukafika pa holo.
Nditalawa n’kuona ubwino wa Yehova ndinaganiza zopanga Yehova kukhala malo anga othawirako. Ndinatsimikiza zoyamba kupezeka pamisonkhano nthawi zonse. (Salmo 34:8) Nyengo yamvula ikafika, nthawi zambiri ndinkafika pamisonkhano nditanyowa komanso ndili matope okhaokha. Ndikafika pa Nyumba ya Ufumu ndinkafunika kusintha kaye zovala. Komabe ndinkaona kuti sindinataye nthawi yanga pachabe.
Mu Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 1985, munalembedwa nkhani yanga. Mlongo wina wa ku Switzerland dzina lake Josette atawerenga nkhaniyi, anakhudzidwa kwambiri moti ananditumizira njinga yamatayala atatu ya maphedulo opalasa ndi manja. Njingayi inalinso ndi matigadi abwino komanso tinyale towala takumbuyo. Nditalandira njingayi, ndinkatha kupanga maulendo popanda nkhawa iliyonse. Ana ankayisirira kwambiri njingayi ndipo ankandiuza kuti amasangalala kwambiri akandiona ndikuyendetsa. Sindinkafunikiranso kukwawa n’kumadziona ngati wachabechabe. Tsopano ndinakwezedwa pamwamba ndipo ndinayamba kumva ngati ndine mfumukazi. Anthu nawonso ankandilemekeza komanso kundiona kuti ndine wofunika.
Moyo Wanga Unasinthiratu
Sizinandivute kuti ndipite patsogolo mwauzimu chifukwa ndinkakhala kale moyo wosalira zambiri komanso ndinali ndi makhalidwe abwino. Ndinkatha kulowa mu utumiki mosavuta chifukwa cha njinga ija ndipo pa 9 August 1986, ndinabatizidwa. Nditabatidzidwa, moyo wanga unasinthiratu ndipo ndinkamva bwino kwambiri kuposa kale lonse. Ndinayamba kukhala ndi mtendere wamumtima komanso wosangalala. Ndinayamba kudziona kuti ndine munthu wofunika, sindinkadzikayikiranso chifukwa tsopano ndinapeza Bambo wondikonda komanso ndinakhala pa ubale ndi anthu omwe amandikonda kuchokera mumtima.
Nditafufuza zomwe ndingachite kuti ndimubwezere Yehova pa zomwe anandichitira, ndinaganiza zochita upainiya wokhazikika. Komabe ndinkakayikira ngati ndingaukwanitsedi. (Salmo 116:12) Nditapemphera ndinaganiza zoti ndiyeserere. Ndinayamba upainiya pa 1 January 1988, ndipo ndakhala ndikuchita utumikiwu mpaka pano. Ndapeza madalitso ambiri chifukwa cha utumikiwu. Ndili ndi abale ndi alongo omwe amandithandiza kuti mwezi uliwonse ndizikwanitsa utumiki wanga. Ndaonanso mmene Yehova wandithandizira pogwiritsa ntchito mzimu wake woyera.—Salmo 89:21.
Monga mpainiya, tsopano ndinkatha kupita kulikonse mosavuta. Ngakhale kuti miyendo yanga inali yofookabe, ndinayambako kumva kukhudza chinachake chikandigunda. Patapita nthawi, ndinapita pachipatala china chake chongotsegulidwa kumene kuti mwina azikandipangitsa mafizo. Komabe, nesi wa pachipatalacho anandiuza kuti ndisavutike n’komwe chifukwa sipapita nthawi yaitali ndimwalira. Nesi mnzake anavomerezana naye ndipo zimenezi zinandifoola kwambiri. Nditabwerera kunyumba, ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize kulimbana ndi maganizo ofooketsawa komanso kuti papezekebe njira ina yopangira mafizo.
Utumiki womwe ndinkachita unakhala ngati njira ina yabwino kwambiri yopangira mafizo chifukwa unkandithandiza kuti ndiziwongola thupi. Patapita zaka zingapo, mmodzi wa manesi aja akudutsa pa Nyumba ya Ufumu, anandiona. Anadabwa kwambiri kundiona kuti ndidakali moyo.
Ngakhale kuti ndine wolumala, ndimayesetsa kutumikira Yehova mwakhama. Abale amandiyamikira chifukwa cha khama langa komanso kufika pamisonkhano mwamsanga. Ndimachita zimenezi chifukwa zimandipatsa mpata wocheza ndi abale ndi alongo komanso kuwasonyeza kuti ndimachita nawo chidwi.
Ndaona kuti Yehova ndi wabwino ndipo wandidalitsa m’njira zambiri. Ndimasangalala kuti ndinathandizapo anthu atatu mpaka kufika pobatizidwa. Mmodzi wa iwo ndi Amelia yemwe analowa nawo kalasi ya nambala 137 ya Giliyadi. Kwa maulendo angapo tsopano, ndakhala ndikulowa nawo Sukulu ya Utumiki Waupainiya. Yehova wandithandiza kwambiri kukhala wosangalala komanso kudziona kuti ndine wofunika. Tsopano anthu amandilemekeza ndipo ndimadziona kuti ndine wofunika. Ndapeza mabwenzi abwino m’gulu la Yehova osati ku Freetown kokha komwe ndimakhala kapena m’dziko la Sierra Leone lokha, koma padziko lonse.
Tsopano patha zaka 40 kuchokera pomwe ndinaphunzira za lonjezo la Mulungu la dziko latsopano, momwe simudzapezeka munthu aliyense wolumala. Lonjezo limeneli limandilimbikitsa kwambiri ndipo ndikufunitsitsa kudzaliona likukwaniritsidwa. Ndipo ndipitiriza kuyembekezera chifukwa ndikudziwa kuti Mulungu wathu Yehova, adzakwaniritsa zomwe anatilonjeza. (Mika 7:7) Yehova wandidalitsa chifukwa sindinafooke ngakhale kuti ndinkakumana ndi mavuto ambiri. Iye wandithandiza kulimbana ndi mavuto komanso mayesero osiyanasiyana. Wakhala akundithandiza pa nthawi yeniyeni yomwe ndinkafunikira thandizolo. Ndine wosangalala kwambiri chifukwa anandinachotsa pafumbi pomwe ndinkakwawa, n’kundikweza pamwamba pomwe sindinkayembekezera n’komwe.
a Panopo amati Phunziro la Baibulo la Mpingo.