Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

KODI ZOPEREKA ZANU ZIMAGWIRITSIDWA NTCHITO BWANJI?

Zimene Ena Ali Nazo Zimathandizira pa Zimene Ena Akusowa

Zimene Ena Ali Nazo Zimathandizira pa Zimene Ena Akusowa

1 OCTOBER 2020

 A Mboni za Yehova amagwira ntchito yophunzitsa anthu Baibulo komanso yothandiza anthu m’mayiko oposa 200. Komabe, mayiko 35 okha ndi amene amapeza zopereka zokwanira kugwiritsa ntchito m’dziko lawo. Nanga bwanji mayiko amene amapeza ndalama zochepa? Kodi amapeza kuti ndalama zogwiritsa ntchito m’dziko lawo?

 Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova limafufuza kuti lidziwe zinthu zomwe abale ndi alongo padziko lonse akufunikira kuti apitirize kulambira Yehova komanso kugwira ntchito yolalikira. Ndipo limaonetsetsa kuti zopereka zikugwiritsidwa ntchito moyenera. Mwachitsanzo, ngati ofesi ya nthambi ina yapeza ndalama zochuluka kuposa zomwe zikufunikira kugwiritsa ntchito, imatumiza ndalama zotsalazo ku ofesi ya nthambi ina yomwe yapeza zochepa. N’zimenenso Akhristu am’nthawi ya atumwi ankachita. Iwo ankathandizana “kuti pakhale kufanana.” (2 Akorinto 8:14) Anagwiritsa ntchito zinthu zochuluka zomwe anali nazo kuti athandize Akhristu anzawo omwe anali ndi zochepa.

 Kodi abale ndi alongo athu amamva bwanji akalandira zopereka kuchokera kumaofesi a nthambi amayiko ena? Mwachitsanzo, anthu ambiri omwe amakhala ku Tanzania amagwiritsa ntchito ndalama zosakwana MK1600 (Malawi Kwacha) pa tsiku. Ngakhale zili choncho, abale ndi alongo anakwanitsa kukonzanso Nyumba ya Ufumu yampingo wa Mafinga pogwiritsa ntchito ndalama zimene abale ndi alongo am’mayiko ena anapereka. Mpingowo unati: “Chiwerengero cha osonkhana chawonjezereka kwambiri kungochokera pamene Nyumba ya Ufumu yathu inakonzedwanso. Tikuyamikira kwambiri gulu la Yehova komanso abale ndi alongo padziko lonse chifukwa chopereka mowolowa manja, zomwe zathandiza kuti tikhale ndi malo abwino olambirira.”

 Mliri wa COVID-19 wachititsa kuti abale ndi alongo ena ku Sri Lanka akumane ndi vuto losowa chakudya. Mmodzi mwa anthu omwe anakhudzidwa ndi vutoli ndi a Imara Fernando ndi mwana wawo Enosh. Iwo anayamikira kwambiri atalandira thandizo kuchokera kwa abale ndi alongo am’mayiko ena ndipo analemba kuti: “Tikuthokoza abale ndi alongo posonyeza kuti amatikonda pa nthawi yovutayi. Ndife osangalala kukhala m’banja lapadziko lonse limeneli ndipo tipitiriza kupempherera abale ndi alongo athu onse kuti Yehova awathandize m’masiku otsiriza ano.”

A Imara Fernando ndi mwana wawo, Enosh

 Abale ndi alongo amayesetsa kugawira ena zimene ali nazo posatengera kumene amakhala. Mwachitsanzo, Enosh anakonza kabokosi ka zopereka kuti azisungiramo ndalama zothandizira mabanja osowa. Nawonso a Guadalupe Álvarez anasonyeza mtima wowolowa manja. Iwo amakhala ku Mexico komwe anthu ambiri amalandira ndalama zochepa pamwezi kapena akagwira ganyu. Ngakhale zili choncho, a Álvarez amapereka zomwe angakwanitse. Iwo analemba kuti: “Ndikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa cha zinthu zabwino zimene amandichitira komanso chikondi chake chosatha. Ndikudziwa kuti zopereka zanga ziphatikizidwa ndi zina ndipo zithandiza abale ndi alongo amene akufunikira thandizo.”

 Abale am’maofesi a nthambi omwe amatumiza ndalama kumayiko amene akufunika thandizo, amakhala osangalala. M’bale Anthony Carvalho yemwe amatumikira m’Komiti ya Nthambi ku Brazil, anati: “Kwa zaka zambiri takhala tikulandira ndalama zogwiritsira ntchito m’dziko lathu kuchokera kumayiko ena. Chifukwa cha thandizoli, tinaona kusintha kwakukulu. Koma panopa tinayamba kupeza ndalama zokwanira ndipo tikumakwanitsa kuthandizanso ena. Abale ndi alongo athu a ku Brazil amaona kuti ntchito yolalikira padziko lonse ndi yofunika kwambiri ndipo amasonyeza mtima wodzimana poyesetsa kuthandiza ena monga ophunzira a Yesu.”

 Kodi a Mboni za Yehova angathandize bwanji abale ndi alongo anzawo omwe akufunika thandizo? Iwo angachite zimenezi popereka ndalama zawo m’mabokosi a zopereka kumpingo, m’malo motumiza paokha kumaofesi a nthambi am’mayiko ena. Angaponye ndalama m’bokosi lolembedwa kuti, “Ntchito Yapadziko Lonse” kapena kudzera pa donate.jw.org. Timayamikira kwambiri zopereka zimenezi.