Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

KODI ZOPEREKA ZANU ZIMAGWIRITSIDWA NTCHITO BWANJI?

Tchanelo cha JW Setilaiti Chimaoneka Kumene Kulibe Intaneti

Tchanelo cha JW Setilaiti Chimaoneka Kumene Kulibe Intaneti

APRIL 1, 2021

 Mwezi uliwonse timayembekezera mwachidwi mapulogalamu auzimu komanso mavidiyo omwe amatulutsidwa pa JW Broadcasting. Komabe abale ambiri a ku Africa sangakwanitse kupeza mapulogalamuwa pa intaneti. Chifukwa chiyani?

 M’madera ambiri a ku Africa intaneti imavuta. Komanso kumene imapezekako imachedwa, kapena ndi yodula kwambiri. Mwachitsanzo, pa nthawi ina woyang’anira dera wina wa ku Madagascar anapanga dawunilodi pulogalamu ina ya mwezi ndi mwezi ya JW Broadcasting pamalo ena a intaneti. Anatchajidwa ndalama zokwana madola 16 zimene ndi zochuluka kwambiri kuposa zimene anthu ena amapeza pa wiki. *

 Ngakhale pali mavuto onsewa, tsopano abale ambiri ku Africa akhoza kumasangalala ndi pulogalamu ya JW Broadcasting popanda kugwiritsa ntchito intaneti. Kodi zimenezi zimatheka bwanji?

 Kungoyambira mu 2017, pulogalamu ya JW Broadcasting yakhala ikupezeka pa tchanelo cha setilaiti m’madera akum’mwera kwa Sahara ku Africa. Tchanelochi chimaulutsidwa kwaulere kwa maola 24 pa tsiku, masiku 7 pa wiki komanso m’zilankhulo 16.

Mu 2018, abale ku Mozambique akuchuna dishi kuti azitha kuonera tchanelo cha Mboni za Yehova ku Nyumba ya Ufumu

 A Mboni za Yehova amalipira kampani ina youlutsa zinthu pa TV kuti iziulutsa mapulogalamu athu pa setilaiti. Setilaiti imene imagwiritsidwa ntchitoyi, imafika kumayiko 35 akum’mwera kwa Sahara ku Africa. Kampaniyi timailipira ndalama zoposa madola 12,000 pa mwezi. Nthawi zina, timafunika kupereka ndalama zina zowonjezera ngati pakufunika tchanelo china choti paulutsidwe mapulogalamu ena apadera omwe akuchitika. Zimenezi zimathandiza kuti anthu ambiri asangalale ndi misonkhano kapenanso mapulogalamu apadera omwe amachitika kukabwera abale ochokera kulikulu.

Mu 2018, abale ndi alongo a ku Malawi a m’Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga akuonera pulogalamu yauzimu pa tchanelo cha Mboni za Yehova

 Anthu ambiri, kuphatikizapo omwe si a Mboni, amaonera tchanelo cha Mboni za Yehova m’nyumba mwawo. Komabe abale ndi alongo ena sangakwanitse kugula zinthu zomwe zimafunika kuti azitha kuonera tchanelochi. Ndiye pofuna kuwathandiza, m’Nyumba za Ufumu zoposa 3,670 munaikidwa zipangizo za setilaiti n’cholinga choti abale ndi alongo azitha kuonera pulogalamu ya JW Broadcasting. Mtengo wa zipangizozi kuphatikizapo thiransipoti, umakwana pafupifupi madola 70 ngati Nyumba ya Ufumuyo ili kale ndi TV kapena pulojekita. Koma ngati palibe, mtengo wonse ukhoza kukwana madola pafupifupi 530.

 Abale ndi alongo athu amasangalala kwambiri ndi tchanelochi. Mkulu mumpingo wina wa ku Cameroon ananena kuti: “Banja lathu limanona zinthu zimenezi ngati mana m’chipululu.” M’bale wina wa ku Nigeria, dzina lake Odebode, ananena kuti: “M’banja mwathu timaonera tchanelochi katatu pa wiki. Ana anga amasangalala kwambiri nthawi imeneyi ikafika. Ndipo nthawi zina tikamaonera zinthu zina, amapempha kuti tiike tchanelochi.” Rose, yemwe amakhalanso ku Nigeria, ananena kuti: “Ndine wosangalala kuti panopa sindioneranso nkhani ngati kale. Koma m’malomwake, ndimakonda kuonera tchanelo cha Mboni za Yehova. Ndikamaonera nkhani, sindinkachedwa kukhumudwa ndi zimene ndaonazo ndipo zinkandikweza BP. Koma JW Broadcasting ndi yolimbikitsa kwambiri komanso yokhazika mtima pansi. Ndi tchanelo chimene ndimachikonda kwambiri. Amenewatu ndi madalitso ochokera kwa Yehova.”

Banja la ku Malawi likuonera vidiyo ya ana pa tchanelo chathu

 Woyang’anira dera wina wa ku Mozambique ananena kuti Nyumba za Ufumu m’dera lake munaikidwa zipangizo za setilaiti. Abale ndi alongo a m’mipingoyi amafika kumisonkhano kutatsala ola limodzi kapena kuposa kuti aonere JW Broadcasting.

Mu 2018 abale ndi alongo amumpingo wina wa ku Ethiopia anatha kuonera pulogalamu ya JW Broadcasting popanda kugwiritsa ntchito intaneti

 Pamsonkhano wamayiko wa 2019 wa ku Johannesburg ku South Africa, nkhani zikuluzikulu, kuphatikizapo zomwe zinakambidwa ndi m’bale wa m’Bungwe Lolamulira, zinaulutsidwa patchanelochi m’madera enanso 9. Sphumelele, yemwe ndi wa m’dipatimenti ya Local Broadcasting ku South Africa, ananena kuti: “M’mbuyomu tikanafunika kuulutsa nkhanizi kudzera pa intaneti. Koma zimenezi zimafunika kukhala ndi intaneti yodalirika komanso ndalama zambiri. Koma tchanelo cha Mboni za Yehova chinali chodalirika komanso chotchipa.”

 Tikukuthokozani chifukwa cha mtima wanu wopatsa popereka ndalama zothandiza pa ntchito yapadziko lonse. Ndalamazi zimathandiza abale ndi alongo ambiri a ku Africa kuti azitha kuonera JW Broadcasting mosavuta pogwiritsa ntchito setilaiti. Timayamikira kwambiri ndalama zanu zimene mumapereka pogwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana kudzera pa donate.jw.org.

^ Madola onse amene atchulidwa munkhaniyi ndi a ku United States.