Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

KODI ZOPEREKA ZANU ZIMAGWIRITSIDWA NTCHITO BWANJI?

Ntchito Yomanga Inayenda Bwino Mliri Usanayambe

Ntchito Yomanga Inayenda Bwino Mliri Usanayambe

1 NOVEMBER, 2020

 Chaka chilichonse, anthu masauzande ambirimbiri akumabatizidwa. Choncho, tikufunikira kuwonjezera malo olambirira. Kuti zimenezi zitheke, Madipatimenti Oona za Mapulani ndi Zomangamanga padziko lonse anakonza zoti m’chaka cha 2020, malo olambirira oposa 2,700 amangidwe kapena kukonzedwa. *

 N’zomvetsa chisoni kuti mliri wa COVID-19 unasokoneza ntchito imeneyi. Komiti Yoona za Ntchito Yofalitsa Mabuku ya Bungwe Lolamulira inaimitsa kaye mapulojekiti ambiri padziko lonse pomvera malamulo a boma komanso pofuna kuteteza abale ndi alongo ku mliriwu. Komabe, mliriwu usanayambe, malo olambirira oposa 1,700 anali atamangidwa kale ndiponso kukonzedwa m’chaka chautumiki cha 2020. Kuwonjezera pamenepa, ntchito yokonzanso maofesi a nthambi opitirira 100 inali itamalizidwa. Taonani mmene mapulojekiti awiri omwe anamalizidwa athandizira abale athu.

 Ofesi ya nthambi ya Cameroon. Ofesi ya nthambi yakale yomwe inali ku Douala inali yaing’ono kwambiri ndipo zinthu zambiri zinkafunika kukonzedwa. Komiti Yoona za Ntchito Yofalitsa Mabuku inaganizira zokonza nthambiyi koma kuti zimenezi zitheke pankafunika ndalama zambiri. Komitiyi inafufuzanso ngati pankangofunika kumanga pamalo ena atsopano kapena kugula maofesi ena n’kuwakonza, koma zonsezi sizinagwire.

 Ndiyeno abale anamva zoti kumpoto kwa Douala boma likufuna kumanga msewu womwe utadutse pafupi ndi malo athu ochitirako msonkhano. Msewu umenewu ukanathandiza kuti zikhale zosavuta kufika pamalowa komanso kubweretsa zinthu zofunikira. Apa zinangokhala ngati yankho lapezeka. Ndiyeno Bungwe Lolamulira linavomereza kuti ofesi ya nthambi yatsopano imangidwe mbali ina ya Malo a Msonkhanowo.

Abale ndi alongo akugwira nawo ntchito yomanga ofesi ya nthambi yatsopano ya Cameroon

 A Mboni za Yehova anagwira ntchitoyi limodzi ndi makontilakita ndipo zimenezi zinathandiza kuti ntchitoyi iyende msanga komanso asawononge ndalama zambiri. Ndalama zonse zomwe zinagwiritsidwa ntchito zinali zopitirira madola 2 miliyoni a ku U.S.A. Komabe ndalamazi n’zochepa poyerekezera ndi mmene ankaganizira poyamba. Banja la Beteli linasamukira kumalo atsopanowa mliri wa COVID-19 utangotsala pang’ono kuyamba.

Ntchito yomanga ofesi ya nthambi ya Cameroon inatha mliri wa COVID-19 usanayambe

 Atumiki a pa Beteli ku Cameroon akusangalala kwambiri ndi malo okhala komanso ogwirira ntchito abwino kwambiri ndipo akuona kuti nthambi yatsopanoyi ndi madalitso ochokera kwa Yehova. Banja lina linanena kuti, “Tikufunitsitsa kumagwira ntchito mwakhama ndiponso kuti tisamaone mphatso imeneyi mopepuka.”

Abale ndi alongo akugwira ntchito mu ofesi yawo yatsopano mliriwu usanayambe

 Ofesi ya Omasulira Mabuku ya Tojolabal ku Mexico. Kwa zaka zambiri, omasulira Chitojolabala anali ku nthambi ya Central America yomwe ili kufupi ndi ku Mexico. Komabe, Chitojolabala chimalankhulidwa kwambiri ku Altamirano ndi ku Las Margaritas, womwe ndi mtunda wa makilomita pafupifupi 1,000 kuchokera mumzinda wa Mexico. Zimenezi zinkachititsa kuti omasulirawa azivutika kumasulira mmene anthu akulankhulira chifukwa ankakhala kutali ndi kumene chinenerochi chimalankhulidwa. Zinkakhalanso zovuta kuti ofesi ya nthambi ipeze abale ndi alongo oyenerera amene angathandize kumasulira ndi kujambula zinthu za m’Chitojolabala.

Abale ndi alongo akuthandiza nawo pomanga ofesi ya omasulira

 Pa zifukwa zimenezi, Komiti Yoona za Ntchito Yolemba Mabuku ya Bungwe Lolamulira inafuna kuti omasulira Chitojolabala asamukire kudera lomwe chinenerochi chimalankhulidwa. Kuti zimenezi zitheke, ofesi ya nthambi inaganiza zogula ndi kukonza nyumba inayake. Kuchita zimenezi kunali kotsikirako mtengo poyerekezera ndi kumanga kapenanso kuchita lendi ma ofesi.

 Womasulira wina anafotokoza mmene wapindulira chifukwa chosamukira kuderali. Iye anati: “Kwa zaka 10 zomwe ndakhala ndikugwira ntchito yomasulira kunthambi, ndinali ndisanakumaneko ndi banja lolankhula chinenero changa. Koma panopa ofesi yathu ili mwenimweni m’dera la anthu olankhula Chitojolabala. Ndimacheza ndi anthu olankhula Chitojolabala tsiku lililonse. Zimenezi zandithandiza kuti ndiphunzire mawu ambiri atsopano komanso kuti ndizigwira bwino kwambiri ntchito yanga.”

Ofesi ya omasulira chinenero cha Chitojolabala isanakonzedwe komanso itakonzedwa

Mapulojekiti a M’chaka cha Utumiki cha 2021

 Pali mapulani oti ngati n’kotheka m’chaka chautumiki cha 2021, ma Ofesi a Omasulira Mabuku okwana 75 amangidwe kapena kukonzedwanso kuphatikizaponso nyumba zosiyanasiyana za maphunziro a Baibulo. Ntchitoyi ikuphatikizapo kumanga nthambi zikuluzikulu 8 kuphatikizapo pulojekiti yatsopano ya kulikulu la padziko lonse yomwe ikuchitika ku Ramapo, New York ndiponso kusamutsa ofesi ya nthambi ya Argentina ndi Italy. Kuwonjezera pamenepa, pali Nyumba za Ufumu zoposa 1,000 zomwe zikufunika kumangidwa, malo olambirira oposa 6,000 omwe sakuyenera kugwiritsidwa ntchito ndipo akufunika kumangidwanso komanso Nyumba za Ufumu 4,000 zikufunika kukonzedwa.

 Kodi ndalama zogwirira ntchito yonseyi zimachokera kuti? M’bale Lázaro González wa m’Komiti ya Nthambi ya Central America anayankha funsoli pamene ankafotokoza zokhudza Ofesi ya Omasulira Mabuku ya Chitojolabala. Iye anati: “M’gawo la nthambi yathu timapeza zinthu movutikira. Ndiye popanda kuthandizidwa ndi abale padziko lonse, sizikanatheka kumanga ofesi ya omasulira mabuku m’Chitojolabala. Ndalama zimene abale padziko lonse amapereka n’zimene zathandiza kuti omasulirawa asamukire m’madera amene zinenero zawo zimalankhulidwa. Tikuthokoza kwambiri abale ndi alongo padziko lonse chifukwa chothandiza mowolowa manja.” Kunena zoona, ntchito zomangamangazi zikutheka chifukwa cha zopereka zanu ndipo tikukuthokozani kwambiri pothandiza pa ntchito yapadziko lonse. Ambiri amapereka kudzera pa donate.jw.org.

^ Madipatimenti Oona za Mapulani ndi Zomangamanga amakonza mapulani komanso kugwira ntchito yomanga Nyumba za Ufumu m’magawo a nthambi zawo. Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga Padziko Lonse, yomwe ili kulikulu lathu lapadziko lonse, imasankha ntchito zomangamanga zomwe zikufunika kugwiridwa poyamba ndiponso imatsogolera pa ntchitozi padziko lonse.