Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Pokonza malo ojambulira vidiyo ya sewero la m’Baibulo ku situdiyo ya ku Mt. Ebo, anagwiritsa ntchito mchenga woposa makilogalamu 27,500.

KODI ZOPEREKA ZANU ZIMAGWIRITSIDWA NTCHITO BWANJI?

Ntchito Yokonza Mavidiyo a Msonkhano Wachigawo wa 2020 Wakuti “Kondwerani Nthawi Zonse”

Ntchito Yokonza Mavidiyo a Msonkhano Wachigawo wa 2020 Wakuti “Kondwerani Nthawi Zonse”

AUGUST 10, 2020

 Mavidiyo a pamisonkhano yathu yachigawo amakhala ogwira mtima ndipo amatithandiza kumvetsa zimene Baibulo limaphunzitsa. Msonkhano Wachigawo wa 2020 wakuti, “Kondwerani Nthawi Zonse,” uli ndi mavidiyo 114 komanso nkhani 43 zokambidwa ndi abale a m’Bungwe Lolamulira komanso abale amene amawathandiza. Kodi munayamba mwaganizirapo ntchito imene imakhalapo komanso ndalama zimene zimafunika kuti mavidiyowa akonzedwe?

 Abale ndi alongo pafupifupi 900 padziko lonse, anadzipereka pogwiritsa ntchito nthawi komanso luso lawo pokonza pulogalamuyi. Ntchitoyi inatenga zaka zoposa ziwiri, ndipo abale ndi alongowa anathera maola pafupifupi 100,000 pogwira ntchitoyi. Zimenezi zikuphatikizapo maola 70,000 omwe anagwiritsa ntchito pokonza vidiyo ya Nehemiya ya maminitsi 76 ya mutu wakuti, “Chimwemwe Chimene Yehova Amapereka Ndicho Malo Anu Achitetezo.”

 Monga mmene mwaonera, panafunika ndalama zambiri posamalira abale ndi alongo odziperekawa. Panafunikanso ndalama zambiri zokonzera malo komanso zogulira zipangizo zofunika pa ntchitoyi.

 M’bale Jared Gossman, yemwe amatumikira m’Dipatimenti Yojambula Mavidiyo, ananena kuti: “Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa ya Bungwe Lolamulira imafuna kuti m’mavidiyowa muzioneka malo osiyanasiyana komanso anthu azikhalidwe zosiyanasiyana. Izi zili choncho chifukwa gulu lathu ndi lapadziko lonse, ndipo timafuna zimenezi zizionekera m’mavidiyowa. Ndiye kuti zimenezi zitheke, panali magulu 24 m’mayiko osiyanasiyana 11, omwe anathandiza pogwira ntchitoyi. Kuti anthuwa agwirire ntchito limodzi, panafunika ndalama zambiri, kukonzekera bwino komanso kuchita zinthu mogwirizana.”

 Pokonza mavidiyo athu ambiri pamafunika zipangizo zapadera komanso kuika zinthu m’njira yoti zigwirizane ndi zochitika za m’vidiyo imene ikujambulidwa. Mwachitsanzo, mbali zosiyanasiyana za mu vidiyo ya Nehemiya yakuti, “Chimwemwe Chimene Yehova Amapereka Ndicho Malo Anu Achitetezo,” anazijambulira mu situdiyo ya ku Mt. Ebo yomwe ili kufupi ndi ku Patterson ku America. Pofuna kugwiritsa ntchito bwino ndalama zimene abale amapereka, koma tikuyesetsa kuti zochitika za mu vidiyoyi zioneke mmene zinkaonekera panthawiyo, abale anakonza mpanda wooneka ngati mpanda wakale wa Yerusalemu pogwiritsa ntchito matabwa opepuka. Panelo iliyonse ya mpandawu inkakhala yaitali mamita 6, ndipo ankaipaka penti komanso kuikutira ndi zinthu zina n’cholinga choti izioneka ngati khoma lamiyala. Makomawa ankatha kuwasuntha n’cholinga choti athe kujambula mbali zosiyanasiyana za vidiyoyi. Izi zinathandiza kuti pasakhale zipangizo zambiri zokonzera malo ena ojambulirako mbali zina za seweroli. Ngakhale zili choncho, ndalama pafupifupi madola 100,000 ndi zimene zinagwiritsidwa ntchito pokonza mbali zosiyanasiyana za vidiyo ya Nehemiya yokha. *

 Kudziwa zimenezi kukutipangitsa kuti tiziyamikira kwambiri pulogalamu ya msonkhano wachigawo wa chaka chino. Tikukhulupirira kuti khama limene abale ndi alongo anali nalo pokonza pulogalamu ya msonkhanowu, lithandiza kuti anthu padziko lonse alemekeze Yehova. Tikukuyamikirani chifukwa chopereka mowolowa manja ndalama zothandizira pa ntchito yapadziko lonse kudzera pa donate.jw.org komanso pogwiritsa ntchito njira zina.

^ Vidiyo ya Nehemiya yakuti, “Chimwemwe Chimene Yehova Amapereka Ndicho Malo Anu Achitetezo,” inajambulidwa mliri wa COVID-19 usanayambe. Choncho pa nthawiyo sipankafunika kukhala motalikirana.