Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ophunzira a Sukulu ya Giliyadi ali m’kalasi pa nthawi ya maphunziro awo mu 2017

KODI ZOPEREKA ZANU ZIMAGWIRITSIDWA NTCHITO BWANJI?

Mmene Sukulu ya Giliyadi Imathandizira Padziko Lonse

Mmene Sukulu ya Giliyadi Imathandizira Padziko Lonse

1 DECEMBER 2020

 Chaka chilichonse abale ndi alongo omwe ali mu utumiki wanthawi zonse padziko lonse amaitanidwa kuti akalowe Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo yomwe imachitikira ku Likulu la Maphunziro la Watchtower ku Patterson, New York. * Ophunzirawa amaphunzira zimene angachite kuti azichita bwino mautumiki awo osiyanasiyana amene amapatsidwa m’gulu la Yehova. Maphunzirowa amawathandiza kuti akalimbikitse ndi kuthandiza kuti zinthu ziziyenda bwino m’mipingo komanso m’maofesi a nthambi padziko lonse.

 Anthu amene amalowa sukulu ya Giliyadi amachokera m’mayiko osiyanasiyana. Mwachitsanzo, kalasi ya nambala 147 yomwe inachitika mu 2019, inali ndi ophunzira 56 omwe anachokera m’mayiko 29. Omwe amalowa sukuluyi amakhala akuchita kale utumiki wanthawi zonse monga kutumikira pa Beteli, kuyang’anira dera, umishonale kapena upainiya wapadera.

 Pamatenga nthawi yaitali kuti akonzekere sukuluyi. Mwachitsanzo Dipatimenti Yoona za Maulendo ku Likulu Lathu imagulira matikiti a ndege abale ndi alongo omwe aitanidwa kusukuluyi. Pa avereji, wophunzira aliyense wa kalasi nambala 147 ankafunika ndalama zokwana madola 1,075 a ku America kuti ayendere kupita ku Patterson ndi kubwerera kwawo. Ophunzira omwe anachokera ku Solomon Islands anakwera ndege 4 kuti akafike ku Patterson ndipo pobwerera kwawo anakwera ndege zitatu, zomwe zikutanthauza kuti anayenda mtunda wa makilomita 35,400. Wophunzira aliyense amene anachokera m’dzikoli anamulipirira tikiti ya ndalama zokwana madola 2,300 a ku America. Pofuna kuti asawononge ndalama zambiri Dipatimenti Yoona za Maulendo ku Likulu Lathu imagwiritsa ntchito pulogalamu inayake yapakompyuta pofufuza matikiti otsika mtengo. Ngakhale pamene asungitsa kale matikiti, pulogalamuyi imapitirizabe kufufuza kwa milungu kapenanso miyezi ingapo kuti aone ngati pali matikiti otsikirako mtengo. Dipatimentiyi imagwiritsanso ntchito mapointi amene abale ndi alongo ena apereka ku gulu lathu kuti agulire matikiti.

 Ophunzira ambiri amafunikira viza monga chilolezo cholowera m’dziko la United States. Zikatere Dipatimenti ya Zamalamulo ku Likulu Lathu imathandiza ophunzirawa kuti atenge viza. Pa avereji, pamafunika ndalama zokwana madola 510 a ku America kuti wophunzira apatsidwe viza komanso ziphaso zoyenerera.

 Kodi tonsefe timapindula bwanji ndi zimene ophunzirawa amaphunzira ku Giliyadi? M’bale Hendra Gunawan ndi mkulu mumpingo wina ku Southeast Asia. M’baleyu ali mumpingo umodzi ndi banja lina lomwe linamaliza maphunziro a Giliyadi. Iye akuti: “Poyamba mumpingo wathu munalibe mpainiya wokhazikika aliyense. Koma banjali litabwera kuchokera kusukulu, mzimu wawo wodzipereka ndiponso khama lawo pa ntchito yolalikira zinathandiza abale ndi alongo ambiri moti nawonso anayamba kuchita upainiya. Patapita nthawi, mlongo wina wamumpingo wathu analowa Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu.”

 M’bale Sergio Panjaitan amatumikira pa Beteli ku Southeast Asia limodzi ndi abale ndi alongo ena omwe anamaliza maphunziro a Giliyadi. Iye akuti: “Sukuluyi sikuti inangopindulitsa iwowo basi koma ikuthandizanso ifeyo. Anaphunzira zinthu zambiri. Koma m’malo modziona kuti ndi ofunika kwambiri kuposa ifeyo, amafotokozera ena zimene anaphunzira. Zimenezi zimatilimbikitsa ndipo nafenso timalimbikitsa ena.”

 Kodi gulu lathu limatenga kuti ndalama zoyendetsera sukuluyi? Ndalama zake zimachokera ku zopereka za ntchito yapadziko lonse ndipo abale ndi alongo ambiri amapereka pogwiritsa ntchito donate.jw.org. Tikukuthokozani chifukwa cha zopereka zanu chifukwa zimathandizira kuti abale ndi alongo ochokera padziko lonse azilowa nawo sukuluyi.

^ Dipatimenti Yoyang’anira Sukulu Zophunzitsa Atumiki a Mulungu ndi imene imakonza maphunzirowa motsogoleredwa ndi Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa ya Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Alangizi ochokera m’dipatimentiyi ndi amene amaphunzitsa sukuluyi limodzi ndi alangizi ena kuphatikizapo abale a m’Bungwe Lolamulira.