Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

KODI ZOPEREKA ZANU ZIMAGWIRITSIDWA NTCHITO BWANJI?

Laibulale Yokwanira M’dzanja Limodzi

Laibulale Yokwanira M’dzanja Limodzi

SEPTEMBER 1, 2021

 “Kale, sitinkaganiza n’komwe kuti tingamalandire chakudya chauzimu pazipangizo zamakono.” Kodi mukugwirizana ndi mawuwa? Anali m’nkhani yolimbikitsa imene Geoffrey Jackson anakamba mu Lipoti la Bungwe Lolamulira la Nambala 6 la 2020. Iye ananenanso kuti: “Koma panopa tingamadzifunse kuti, ‘Kodi tingathe bwanji kupirira nthawi yovutayi popanda zinthu ngati JW Library. Kwa zaka zambiri, Yehova wakhala akutikonzekeretsa nthawi yovuta ngati imeneyi.”

 Kodi Yehova wakhala akutikonzekeretsa bwanji? Kodi pulogalamu ya JW Library inapangidwa bwanji, nanga amafunika kuchita chiyani kuti pulogalamuyi izigwira bwino ntchito?

N’kuyamba Kupanga Pulogalamu Ngati Imeneyi

 Mu May 2013, Bungwe Lolamulira linapempha Dipatimenti ya MEPS ku likulu lapadziko lonse kuti ipange pulogalamu yoti anthu azikhala ndi Baibulo la Dziko Latsopano pazipangizo zawo. M’bale Paul Willies, yemwe amagwira ntchito mu dipatimentiyi, ananena kuti: “Tinali tisanatulutsepo pulogalamu iliyonse yogwiritsa ntchito pazipangizo m’masitolo a mapulogalamu. Koma tinapanga timu ya anthu, kusiya kugwira ntchito zina komanso kugwirizana ndi madipatimenti ena kuti tipange pulogalamu imeneyi. Tinkapemphera pafupipafupi ndipo Yehova anatithandiza kutulutsa pulogalamuyi patangopita miyezi 5, pamsonkhano wa pa chaka.”

 Kenako tinayamba ntchito yokonza pulogalamuyi kuti ikhale laibulale yeniyeni yokhala ndi mabuku ambiri komanso yopezeka m’zilankhulo zina. Pofika mu January 2015, ambiri a mabuku athu a Chingelezi anali akupezeka papulogalamuyi. Ndipo patangopita miyezi 6, anthu ankatha kupanga dawunilodi mabukuwo m’zilankhulo zina zambirimbiri.

 Kuchokera nthawi imeneyo, abale athu asintha pulogalamuyi m’njira zambiri. Iwo awonjezera mavidiyo, akonza zoti anthu azipeza zinthu zonse zokhudza misonkhano yampingo akangodina batani imodzi komanso zoti azipeza pamavesi a m’Baibulo malifalensi ake onse opezeka mu Buku Lofufuzira Nkhani.

Kukonza Laibulaleyi

 JW Library imagwiritsidwa ntchito pazipangizo zokwana 8 miliyoni tsiku lililonse komanso pazipangizo 15 miliyoni mwezi uliwonse. Kodi n’chiyani chimathandiza kuti pulogalamuyi izigwirabe bwino ntchito pazipangizo zonsezi? M’bale Willies anafotokoza kuti: “Mapulogalamu apazipangizo samaliza kukonzedwa. Nthawi zonse tiyenera kuwonjezera zinthu zothandiza kuti anthu azigwiritsa ntchito pulogalamuyi mosavuta. Makampani opanga mapulogalamu ochititsa kuti zipangizo zizigwira ntchito amasinthasintha mapulogalamu awo moti tiyenera kusinthanso pulogalamu yathuyi kuti izigwirabe ntchito pazipangizo. Tiyenera kusinthanso zinthu popeza kuti mabuku ndi zinthu zina zopezeka pa JW Library zikuchulukirachulukirabe. Kuphatikiza pamodzi zilankhulo zonse, panopa pali mabuku okwana 200,000 ndiponso mavidiyo ndi zinthu zongomvetsera zokwana 600,000 zomwe zikupezeka pa JW Library.

 Kuti tizikonzabe pulogalamuyi, timafunika zambiri osati makompyuta basi. Timafunikanso kugula malaisensi a mapulogalamu osiyanasiyana. Laisensi ina timagula chaka chilichonse pa ndalama zokwana madola 1,500 a ku United States. Komanso Dipatimenti ya MEPS imagwiritsa ntchito ndalama zokwana madola 10,000 a ku United States chaka chilichonse kuti agule zinthu kumakampani osiyanasiyana zomwe zimathandiza kuti pulogalamu yathuyi izigwirabe bwino ntchito pa makompyuta, matabuleti ndi mafoni atsopano.

Kupanga Dawunilodi Zinthu Kumathandiza Kuti Tisawononge Ndalama Zambiri

 JW Library yathandiza kuti tisamagwiritse ntchito ndalama zambiri posindikiza mabuku, kuwamata komanso kuwatumiza. Mwachitsanzo, taganizirani za kabuku kakuti Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku. Tinasindikiza timabuku ta Kuphunzira Malemba ta 2013 tokwana 12 miliyoni. Koma tinasindikiza timabuku ta 2020 tokwana 5 miliyoni basi, ngakhale kuti kunali ofalitsa pafupifupi 700,000 padziko lonse oposa amene analipo mu 2013. N’chifukwa chiyani zinali choncho? Masiku ano, abale ndi alongo ambiri amawerenga lemba la tsiku pa JW Library. *

“Ndi Yamtengo Wapatali Kwambiri”

 JW Library imathandiza anthu amene amaigwiritsa ntchito m’njira zambiri. Mlongo wina wa ku Canada, dzina lake Geneviève, amaona kuti pulogalamuyi yamuthandiza kuti aziphunzira Baibulo pafupipafupi. Iye anati: “Kunena zoona, zikanakhala kuti ndizifunika kutulutsa chimulu cha mabuku kuti ndiphunzire, bwenzi ndisakuphunzira Baibulo tsiku lililonse m’mawa. Koma chifukwa cha pulogalamuyi, ndimangotenga tabuleti yanga ndipo zonse zofunika zili pompo. Kuphunzira Baibulo nthawi zonse kwalimbitsa chikhulupiriro changa komanso ubwenzi wanga ndi Yehova.”

Geneviève

 Pulogalamu ya JW Library yathandiza kwambiri pa nthawi ya mliri wa COVID-19. Mlongo wina wa ku United States dzina lake Charlyn anati: “Chifukwa choti mliri wa COVID-19 wafalikira padziko lonse, sindinalandire mabuku athu atsopano osindikizidwa kwa nthawi yoposa chaka. Koma JW Library yandithandiza kumalandira chakudya chauzimu ndipo ndimathokoza Yehova chifukwa chotisonyeza chikondi potipatsa pulogalamu imeneyi.”

 Mlongo wina wa ku Philippines dzina lake Faye ananena zimene anthu ambiri akuganiza. Iye anati: “Ndikutha kukhalabe pa ubwenzi wolimba ndi Yehova pongogwiritsa ntchito pulogalamu yodabwitsa imeneyi. Ndimaiwerenga tsiku lililonse ndikangodzuka. Ndimaimvetsera ndikamagwira ntchito zapakhomo. Ndimaigwiritsa ntchito pokonzekera misonkhano. Ndimaigwiritsanso ntchito pokonzekera phunziro langa la Baibulo. Ndimaonera mavidiyo papulogalamuyi ndikapeza mpata. Ndimawerenga nkhani kapena Baibulo papulogalamuyi ndikamadikira pamzere. Kunena zoona, ndi yamtengo wapatali kwambiri.”

 Pulogalamu ya JW Library yathandizanso kwambiri mu utumiki. Mwachitsanzo, mlongo wina ku Cameroon ankafuna kugwiritsa ntchito lemba limene anali ataona mlongo wina akugwiritsa ntchito milungu ingapo yapitayo. Koma sankakumbukira kumene angapeze lembali. Iye ananena kuti: “Mwamwayi, ndinakumbukira mawu ena amulembali. Ndiye ndinatsegula pulogalamuyi n’kufufuza mawuwo. Nthawi yomweyo, ndinapeza lembalo. Chifukwa chogwiritsa ntchito pulogalamuyi, ndimatha kupeza malemba ambiri amene nthawi zina ndimawaiwala.”

 Ndalama zimene mumapereka mokoma mtima pogwiritsa ntchito njira zimene zafotokozedwa pa donate.jw.org zatithandiza kupanga, kukonza ndi kusintha pulogalamu ya JW Library n’cholinga choti abale ndi alongo apadziko lonse azitha kuigwiritsa ntchito. Timakuthokozani kwambiri chifukwa cha mtima wanu wopatsa.

Zimene Tapanga pa JW Library

  1. October 2013—Pulogalamuyi inatulutsidwa ndipo inali ndi Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso m’Chingelezi

  2. January 2015—Mabuku ena anayamba kupezeka papulogalamuyi, kenako mabuku a m’zilankhulo zina zambirimbiri anayambanso kupezeka

  3. November 2015—Zinatheka kuchekenira mawu

  4. May 2016—Tinaikapo batani la Misonkhano

  5. May 2017—Zinatheka kulemba notsi

  6. December 2017—Baibulo Lophunzirira linayamba kupezeka m’Chingelezi

  7. March 2019—Zinatheka kupanga dawunilodi mabuku omvetsera, kuonera mavidiyo popanda kupanga dawunilodi komanso kupeza malifalensi a mu Buku Lofufuzira Nkhani

  8. January 2021—Buku lakuti Mungakhale ndi Moyo Mpaka Kalekale linayamba kupezeka

^ Ndalama yochepa imawonongedwa nthawi iliyonse imene munthu wapanga dawunilodi zinthu pa JW Library. Mwachitsanzo, chaka chatha tinagwiritsa ntchito ndalama zoposa madola 1.5 miliyoni a ku United States polola anthu kupanga dawunilodi zinthu komanso kungoonera kapena kumvetsera zinthu pa jw.org ndi pa JW Library. Komabe ndalama zimene timagwiritsa ntchito kuti zinthu zizipangidwa dawunilodi n’zochepa kwambiri poyerekezera ndi zimene tingagwiritse ntchito popanga ndi kutumiza mabuku, ma CD komanso ma DVD.