Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

KODI ZOPEREKA ZANU ZIMAGWIRITSIDWA NTCHITO BWANJI?

Kuonera Kapena Kumvetsera Msonkhano

Kuonera Kapena Kumvetsera Msonkhano

AUGUST 1, 2021

 Msonkhano wachigawo wa chaka cha 2020 unali wapadera kwambiri. Unali msonkhano woyamba kujambulidwa n’kuikidwa pa intaneti kuti anthu padziko lonse auonere. Koma abale ndi alongo ambiri ku Malawi ndi ku Mozambique anaonera kapena kumvetsera msonkhanowu popanda kugwiritsa ntchito intaneti. Kodi zimenezi zinatheka bwanji?

 A m’Komiti ya Ogwirizanitsa komanso a m’Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa ya Bungwe Lolamulira anavomereza kuti ku Malawi ndi ku Mozambique msonkhano uulutsidwe pa TV ndi pa wailesi. Koma n’chifukwa chiyani anavomereza zimenezi? Ku Malawi, mtengo wa intaneti ndi wodula kwambiri kuposa kumayiko ambiri moti ndi a Mboni ochepa okha amene angakwanitse kuigwiritsa ntchito. M’bale William Chumbi, yemwe ali m’Komiti ya Nthambi ku Malawi, anati: “Kugwiritsa ntchito wailesi ndi TV kunali njira yokhayo imene tikanaperekera chakudya chauzimu chimenechi kwa abale ndi alongo.” M’bale Luka Sibeko, yemwe alinso m’Komiti ya Nthambi ku Malawi, anawonjezera kuti: “Zikanakhala kuti n’zosatheka kuulutsa msonkhanowu pa TV ndi pa wailesi, ndi abale ochepa okha m’dziko lathu amene akanatha kumvetsera msonkhanowu.” Nakonso ku Mozambique, ndi abale ochepa okha omwe akanatha kupeza chipangizo chamakono kapena kugwiritsa ntchito intaneti.

Kukonzekera

 Chifukwa cha mliri wa COVID-19, masiteshoni ena a TV ndi a wailesi anali atayamba kale kuulutsa misonkhano yampingo. * Abale athu anapempha masiteshoniwa kuti awapatse nthawi yowonjezereka youlutsira msonkhano wachigawo.

 Koma ku Malawi, abale anakumana ndi vuto. Nthawi zambiri, masiteshoni amangolola kuti anthu aulutse zinthu zawo kwa ola limodzi basi. Masiteshoniwo amaopa kuti akalola anthu kukhala ndi nthawi yaitali kuposa ola, amene akumvetsera angasiye kukhala ndi chidwi. Koma abale athu anafotokoza kuti ntchito yathu imathandiza kwambiri anthu. Ngakhale pa nthawi ya mliriyi, tikuthandiza anthu kuti azimvabe uthenga wabwino wochokera m’Baibulo, womwe ungawathandize kukhala nzika zabwino komanso kukhala ndi mabanja osangalala. Atamva zimenezi, masiteshoniwa analola kuti abale akhale ndi nthawi yowonjezereka.

 Ku Malawi, msonkhano unaulutsidwa ndi siteshoni imodzi ya TV ndi imodzi ya wailesi. Masiteshoni onse awiriwa amaulutsa nkhani m’dziko lonse la Malawi ndipo anthu mamiliyoni angapo amatha kumvetsera. Ku Mozambique, msonkhano unaulutsidwa ndi siteshoni imodzi ya TV ndi masiteshoni 85 a wailesi.

 M’mayiko onse awiriwa, analipira ndalama zokwana madola 28,227 * poulutsa msonkhano pa TV komanso ndalama zokwana pafupifupi madola 20,000 pouulutsa pa wailesi. Analipira ndalama zosiyanasiyana kuti aulutse msonkhano pa wailesi. Mwachitsanzo, kusiteshoni ina yaing’ono analipira madola 15 pomwe kusiteshoni ina yaikulu youlutsa nkhani m’dziko lonse analipira madola 2,777.

 Abale athu anayesetsa kuti asawononge ndalama zimene anthu amapereka. Mwachitsanzo, ku Malawi, anakambirana ndi akumasiteshoniwa kuti awatsitsire mtengo moti kusiteshoni ina anatsitsa mtengo wake ndi 30 peresenti. Zimenezi zinathandiza kuti abale asunge ndalama zokwana madola 1,711. Ku Mozambique, masiteshoni ena anatsitsa mtengo chifukwa choti tili ndi mbiri yabwino yakuti ndife anthu oona mtima komanso timalipira pa nthawi yake.

Mawu Othokoza

 Abale athu anathokoza kwambiri kuti anatha kuonera msonkhano pa TV kapena kuumvetsera pa wailesi. M’bale wina dzina lake Patrick, yemwe ndi mkulu ku Malawi, anati: “Tikuthokoza kwambiri abale a m’Bungwe Lolamulira chifukwa chotiganizira m’nthawi ya mliriyi.” M’bale wina wa ku Malawi dzina lake Isaac ananena kuti: “Tilibe zipangizo zina zamakono choncho tikuthokoza kwambiri kuti gulu la Yehova linalola kuti timvetsere msonkhano pa wailesi. Chifukwa cha zimenezi, banja langa lonse linatha kumvetsera msonkhano. Tinaona kuti zimenezi ndi umboni wakuti Yehova amakonda anthu ake.”

 Msonkhano wa 2020 unali woyamba umene wofalitsa wina wa ku Mozambique anamvetsera. Iye anati: “Zonse zimene achita kuti tionere msonkhano pa TV zandikumbutsa kuti Yehova ndi Mulungu wamphamvuyonse. Mliri sunamulepheretse kutipatsa chakudya chauzimu moti anandipatsa chakudyachi ndili m’nyumba yanga momwemu. Ndinaona umboni wa chikondi chimene anthu a Yehova ali nacho. Sindikukayikira ngakhale pang’ono kuti chipembedzochi ndi choona.”

 M’bale wina dzina lake Wyson, yemwe ndi mkulu, ananena kuti: “Ndikufuna kuthokoza kwambiri mmene kapolo wokhulupirika watisamalirira pa nthawi ya mliriyi. Kuno kumayiko osauka, ambirife tikuvutika ndi mavuto azachuma koma kulola kuti msonkhano uulutsidwe pa wailesi ndi pa TV kunatithandiza kumvetsera komanso kupindula ndi msonkhanowu.”

 A m’Komiti ya Ogwirizanitsa komanso a m’Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa avomerezanso kuti msonkhano wachigawo wa 2021 uulutsidwe pa TV ndi pa wailesi kumadera ena. Kodi timapeza bwanji ndalama zolipirira zimenezi? Ndalama zake zimachokera pa zimene anthu amapereka pothandiza ntchito yapadziko lonse. Zambiri mwa ndalamazi zimaperekedwa pogwiritsa ntchito njira zopezeka pa donate.jw.org. Tikukuthokozani kwambiri chifukwa chopereka ndi mtima wonse.

^ Chakumayambiriro kwa chaka cha 2020, Komiti ya Ogwirizanitsa inavomereza kuti misonkhano yampingo iziulutsidwa pa TV ndi pa wailesi m’madera ena pa nthawi ya mliri wa COVID-19. Inavomereza zimenezi pofuna kuthandiza anthu amene sangapange misonkhano pogwiritsa ntchito foni kapena intaneti chifukwa choti zinthuzi sizipezeka kwawo kapena ndi zodula kwambiri moti sangakwanitse. Koma kumadera kumene anthu amatha kulumikizana ndi mpingo wawo pogwiritsa ntchito intaneti sayenera kugwiritsa ntchito njira imeneyi.

^ Madola onse otchulidwa munkhaniyi ndi a ku United States.