Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

KODI ZOPEREKA ZANU ZIMAGWIRITSIDWA NTCHITO BWANJI?

Amishonale Amapita “Kumalekezero a Dziko Lapansi”

Amishonale Amapita “Kumalekezero a Dziko Lapansi”

JUNE 1, 2021

 Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Mudzakhala mboni zanga . . . kumalekezero a dziko lapansi.” (Machitidwe 1:8) Masiku ano, a Mboni za Yehova akugwira ntchito imeneyi mwakhama. Koma kuli malo ena, ngakhale kumizinda ina, kumene anthu ambiri sanalalikiridwe mokwanira. Ndipo kumayiko ena kuli a Mboni ochepa. (Mateyu 9:37, 38) Ndiye kodi tikutani kuti tikwanitse kulalikira kwa anthu ambiri?

 Kuti timvere lamulo la Yesulo, Komiti ya Utumiki ya Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova imatumiza amishonale kuti akathandize kumalo kumene kukufunika olalikira ambiri. Panopa kuli amishonale othandiza pa ntchito yolalikira okwana 3,090 padziko lonse. * Ambiri a iwo anapita kusukulu ina yophunzitsa Baibulo ngati Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu. Amishonale amadzipereka kuti achoke kwawo n’kupita kudziko lina. Iwo amakhala anthu amene aphunzitsidwa bwino, akumana ndi zinthu zambiri pa moyo wawo komanso ndi olimba mwauzimu. Choncho amathandiza kwambiri pofalitsa uthenga wabwino komanso amapereka chitsanzo chabwino kwa Akhristu atsopano.

Amishonale amathandiza polalikira uthenga wabwino kumene kukufunika a Mboni ambiri

Kuthandiza Amishonale Kuti Azithandiza Ena

 Ku ofesi ya nthambi iliyonse, abale a mu Ofesi Yoyang’anira Atumiki a ku Filudi, yomwe ili m’Dipatimenti ya Utumiki, amagwira ntchito ndi a m’Komiti ya Nthambi pothandiza amishonalewo. Amawathandiza kukhala ndi nyumba, chithandizo chakuchipatala komanso kangachepe kowathandiza kupeza zofunika pa moyo. Mu chaka chautumiki cha 2020, a Mboni za Yehova anagwiritsa ntchito ndalama zokwana madola 27 miliyoni a ku United States posamalira amishonale. Chifukwa chothandizidwa chonchi, amishonale amatha kugwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zawo zambiri polalikira komanso polimbikitsa mpingo wawo.

Amishonale amathandiza kulimbitsa mipingo

 Kodi amishonale athandiza bwanji pa ntchito yolalikira? M’bale Frank Madsen, yemwe ali m’Komiti ya Nthambi ya ku Malawi, anati: “Chifukwa choti amishonale ndi olimba mtima komanso aluso, amathandiza anthu amumpingo wawo kuti azilalikira m’magawo ovuta monga kunyumba zokhala ndi mipanda kapena kumene amalankhula chilankhulo china. Amishonale amaperekanso chitsanzo chabwino pochita khama kuti aphunzire chilankhulo ndi chikhalidwe cha kumene akutumikira. Komanso amalimbikitsa achinyamata kuti achite utumiki wa nthawi zonse. Timathokoza Yehova chifukwa cha amishonalewa.”

 M’bale wina amene ali m’Komiti ya Nthambi yakudziko lina anati: “Amishonale amapereka umboni woti anthu a Yehova ndi ogwirizana padziko lonse. Ngakhale anthu amene si Mboni amazindikira kuti mfundo za m’Baibulo zatithandiza kukhala ogwirizana ngakhale kuti timachokera m’zikhalidwe zosiyanasiyana.”

 Kodi amishonale amathandiza bwanji anthu amumpingo kumene akutumikira? M’bale wina wa ku Timor-Leste dzina lake Paulo amayamikira kwambiri amishonale amumpingo wake. Iye anati: “Kwathu n’kotentha kwambiri koma amishonalewo amalalikirabe nthawi zonse ngakhale kuti amachokera kumadera ozizira. Nthawi zonse amapezeka m’mawa pamisonkhano yokonzekera utumiki. Ndimawaonanso pafupipafupi akupita pa maulendo obwereza masana kuli kotentha kwambiri komanso madzulo. Iwo athandiza anthu ambiri, ngati ineyo, kuti aphunzire choonadi. Amagwiritsa ntchito moyo wawo wonse potumikira Yehova mwakhama komanso mosangalala. Zimenezi zimalimbikitsa onse mumpingo kuti azichita zambiri potumikira Yehova.”

 Mpainiya wokhazikika wina ku Malawi dzina lake Ketti anafotokoza mmene banja lina la amishonale linamuthandizira. Iye anati: “Pamene banja lina la amishonale linafika mumpingo wathu, wa Mboni ndinali ndekha m’banja lathu. Koma banjali linkandithandiza kwambiri ndipo linayamba kugwirizana ndi banja lathu. Chitsanzo chawo chabwino chinathandiza ana anga kuona kuti kutumikira Yehova kumathandiza anthu kuti akhale ndi moyo wabwino komanso wosangalala. Chifukwa cholimbikitsidwa ndi amishonalewo, panopa ana anga atatu ndi apainiya okhazikika ndipo mwamuna wanga wayamba kufika kumisonkhano.”

 Kodi ndalama zimene zimagwiritsidwa ntchito posamalira amishonale zimachokera kuti? Zimachokera pa ndalama zimene anthu amapereka pothandiza ntchito yapadziko lonse. Ndalama zambiri zimaperekedwa m’njira zofotokozedwa pa donate.jw.org. Timathokoza kwambiri zimene anthu amapereka mowolowa manja.

^ Amishonalewa amatumizidwa kumipingo kumene kukufunika anthu ambiri ogwira ntchito yolalikira. Kuli amishonale enanso 1,001 omwe amagwira ntchito yadera.