Khalani Bwenzi la Yehova—Zochita
Izi ndi zochita zosiyanasiyana zomwe zaikidwa pamodzi pofuna kuti muzisangalala ndi ana anu.
Thandizani Kalebe Kukonza M’nyumba
Pangani dawunilodi kapena sindikizani tsambali ndipo muthandizeni Kalebe kupeza zidole zake 5 zomwe akufunika kuchotsa m’nyumba.
Muzipemphera Nthawi Iliyonse: Nyimbo ndi Mawu Ake
Pangani dawunilodi mawu a nyimbo yomwe mungathe kusindikiza. Ana adzaikonda nyimbo yosavuta kuphunzirayi.
Kodi Kalebe Akuwerenga Buku Lanji?
Onerani vidiyo yakuti, “Kuba N’koipa.” Kenako sindikizani tsambali ndipo mulikongoletse ndi chekeni.
Pangani Chikwama cha mu Utumiki
Kodi mumafunika kutenga chiyani popita kolalikira? Tsambali lingakuthandizeni kuti muzitenga chikwama popita mu utumiki.
Kukonzekera Kupita Kolalikira
Kodi mungasankhe zovala zimene Kalebe ndi Sofiya akufunika kuvala pokalalikira?
Panga Galimoto ya Kalebe
Sindikiza, dula ndi kulumikiza galimoto ya Kalebe.
Lowezani Salimo 83:18
N’chifukwa chiyani Yehova amatchedwa kuti “Wam’mwambamwamba wolamulira dziko lonse lapansi”?
Kodi Uyenera Kuchita Chiyani?
Onerani vidiyo yakuti “Uzikhululuka ndi Mtima Wonse” kenako sindikizani tsambali ndipo mukongoletse chithunzi cholondola.
Lowezani Salimo 133:1
Tikasonkhana, Yehova amatidalitsa potithandiza kuti tikhale ogwirizana komanso a mtendere.
Timapepala Tazithunzi Tofunika Kusunga!
Mungagwiritsire ntchito timapepalati kudziwa malo omwe mumawerenga m’mabuku anu!
Kodi Zithunzizi Zikusiyana Pati?: Zochita Zokhudza Misonkhano
Yerekezerani zithunzizi. Kodi chingakuthandizeni ndi chiyani kuti muzimvetsera kwambiri nthawi ya misonkhano?
Kodi Yehova Angakuthandize Bwanji Kuti Ukhale Wolimba Mtima?
Yehova angakuthandize ngati mmene anathandizira kamtsikana ka ku Isiraeli.
Kuyerekezera: Moyo Wapanopa ndi Wam’tsogolo
Kodi ndi malonjezo ati a m’Baibulo omwe adzakwaniritsidwe m’Paradaiso?
Thandizani Anthu Ambiri Pogwiritsa Ntchito Pulogalamu Yothandiza Kuphunzira Chinenero pa JW
Phunzirani mawu a m’chinenero china kuti muzithandiza anthu kuphunzira zokhudza Yehova.
Muzikonda Anthu Onse
Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti amakonda anthu onse?
Lowezani Mabuku a M’Baibulo (Gawo 1)
Gwiritsani ntchito makadi a mabuku a m’Baibulo kuti akuthandizeni kuloweza mabuku a Chiheberi, kuyambira Genesis mpaka Yesaya.
Lowezani Mabuku a M’Baibulo (Gawo 2)
Gwiritsani ntchito makadiwa kuti akuthandizeni kuloweza mabuku a Malemba a Chiheberi, kuyambira Yeremiya mpaka Malaki.
Kunena Zoona Kuli Ngati Kumanga Mlatho
N’chifukwa chiyani kunena zoona kungathandize kuti muzigwirizana kwambiri ndi anzanu?
Kodi Ungatani Kuti Ukhale Woleza Mtima?
Kodi ndi njira zina ziti zimene ungasonyezere kuti ndiwe woleza mtima?
Dongosolo la Banja Limene Yehova Anakhazikitsa
Kodi m’Baibulo mungapezemo mabanja a ndani?
Imbirani Yehova Nyimbo
Dulani zithunzizi ndi kuziika malo amodzi potsatira malangizo ndipo kenako imbirani Yehova komanso loweza nyimbo ya mutu wakuti “Dzina Lanu Ndinu Yehova.”
Dzina la Yehova
Kodi dzina la Mulungu limapezeka maulendo angati m’Baibulo?
Yehova Anapanga Zinthu Zokongola
Kodi ndi zinthu zingati zimene Yehova analenga zomwe mungathe kuzipeza m’chithunzicho?
Tizilalikira kwa Anthu a Mitundu Yonse
Kodi uthenga wa Ufumu uyenera kulalikidwa kwa ndani?
Pezani Anzanu Enieni
N’chifukwa chiyani ndi bwino kukhala ndi anzanu omwe ndi achikulire?
Lolani Kuti Yehova Akuphunzitseni
Mulungu angakuphunzitseni kuti mukhale olimba ndiponso amphamvu.
Tchati Chosonyeza Moyo wa Yesu
Werengani malemba a m’Baibulo ndipo agwirizanitseni ndi chithunzi chogwirizana ndi lemba lililonse.
Inuyo Panokha Muzikonda Kwambiri Choonadi
Kodi ndi zinthu ziti zimene mungachite zomwe zingakuthandizeni kuti muzikonda kwambiri choonadi?
Mmene Tingasonyezere Chikondi Kwa Ena
Kodi tingatsanzire bwanji Yesu pa nkhani yosonyeza ena chikondi?
Yerekezera Kuti Uli M’Paradaiso
Kodi ndi chinthu chiti chimene ukuchiyembekezera kwambiri m’Paradaiso?
Uzipilira Ena Akakuchitira Nkhanza
Kodi tizitani ena akatichitira zinthu zankhanza?
Kuphunzira za Mabwenzi a Yehova
Gwiritsani ntchito zoti muchitezi kuti muyambe kuphunzira Baibulo panokha.
Uzidzichepetsa
Phunzirani zokhudza kudzichepetsa kuchokera kwa anthu osiyanasiyana otchulidwa m’Baibulo.
Tili ndi Zifukwa Zambiri Zokhalira Osangalala
Kodi ndi nyama iti yomwe ukufunitsitsa kudzasewera nayo m’dziko latsopano la Mulungu?
Kupilira Imfa ya Munthu Yemwe Munkamukonda
Kodi n’chiyani chomwe chingatithandize kukhalabe osangalala pamene munthu yemwe tinkamukonda wamwalira?
Kunyumba ndi Nyumba
Kodi ndi zinthu ziti zomwe ukufuna kugwiritsa ntchito muutumiki?
Uzipempherera Ena
Kodi ndi anthu ati omwe ungawapempherere?
Uzikonda Nyumba ya Yehova
Uziyesetsa kuchita zinthu zomwe zingathandize kuti nyumba ya Mulungu izikhala yoyera nthawi zonse
Ndakonzekera Kuchita Zambiri
Yehova amafuna kuti tizikhala ndi zolinga zauzimu. Kodi iweyo uli ndi zolinga zotani?
Lambirani Yehova Mudakali Achinyamata
Mungasonyeze bwanji kuti ndinu oyamikira?
Yehova ndi Mnzanga Wapamtima
Mulungu analenga zomera ndiponso zinyama kuti anthufe tizisangalala chifukwa chakuti iye ndi Mnzathu
Uzichita Zinthu Bwino Muutumiki
Mungatani kuti muchita zinthu zabwino muutumiki?
Muzikhululuka
N’chiyani chingakuthandizeni kuti muzikhululukira ena?
Nyimbo Yofotokoza Mavidiyo ndi Zinthu Zina za Khalani Bwenzi la Yehova
Kodi ukukumbukira zina mwa zinthu zimene Kalebe ndi Sofiya aphunzira m’Baibulo?
“Ndikufuna”
Yesu amakonda kuthandiza ena. Ungatani kuti nawenso uzichita ngati Yesu?
Timakonda Kulambira kwa Pabanja
Kodi banja lanu lingachite zotani kuti muzisangalala kwambiri ndi kulambira kwa pabanja?
Muzigwiritsa Ntchito Nthawi Mwanzeru
Kodi lemba la Aefeso 5:15, 16 lingakuthandizeni bwanji kugwiritsa ntchito nthawi mwanzeru?
Ntchito Zodabwitsa za Mulungu
Kodi ungatchule nyama zingati?
Ili ndi Banja Lathu
Dziwani zokhudza banja lanu!
Kodi Mumamva Bwanji?
Kodi ungatani kuti uzilalikira mwakhama?
Zikomo Kuti Ndinu Mnzanga
Anzathu enieni amatithandiza kuti tizikonda Yehova.
Uzikhala Wokhulupirika
Yehova amakonda anthu okhulupirika.
Uzikonda Mnzako
Kodi Sofiya angasonyeze bwanji chikondi ndiponso kukoma mtima?
Munapereka Mwana Wanu Wobadwa Yekha
Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti iye ndi amene anayamba kutikonda?
Uzipirira Ngati Nowa
Phunzirani zimene mungachite kuti muzipirira ngati mmene Nowa anachitira.
Esitere Anali Wolimba Mtima
Phunzira zimene ungachite kuti ukhale wolimba mtima ngati Esitere.
Yerekezerani Kuti Muli M’dziko Latsopano
Kodi mungadziyerekezere muli m’dziko latsopano?
Chikondi cha Mulungu
Tingasonyeze bwanji kuti timakonda ena ngati mene Yehova amachitira?
Yehova Amakhululuka
Yehova amakhala wokonzeka kutikhululukira nthawi zonse.
Kodi Tiyenera Kukondwerera Mabefide?
Onani chifukwa chake sitikondwerera mabefide.
Buku la Mulungu Ndi Chuma
Baibulo ndi mphatso yochokera kwa Yehova.
Mariya—Anali Wodzichepetsa ndi Wololera
Mofanana ndi Mariya, nafenso tingathe kukhalabe okhulupirika kwa Yehova kaya tikumane ndi zotani.
Tipitirizabe Kupirira
Tingathe kupirira mavuto tikamaganizira zinthu zabwino zomwe tikuyembekezera m’tsogolo.
Rute Anali Bwenzi Lenileni
Ungafanane ndi Rute pokhala bwenzi lenileni.
Davide Ndi Chitsanzo Chabwino kwa Ana
Davide ali mnyamata anayamba kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ndipo ubwenziwo unkamuthandiza pa moyo wake wonse.
Kodi Yehova Amayankha Mapemphero?
Nthawi zina Yehova amayankha mapemphero m’njira yomwe sitinkayembekezera.
Muzipemphera kwa Yehova Tsiku Lililonse
Timafunika kuchita khama kuti tikhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova, koma kuchita zimenezi n’kothandiza kwambiri
Munachitira Ine Amene
Atumiki a Yehova amasangalala kuchita chilichonse pofuna kuthandiza odzodzedwa.
N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kumvera Mulungu Ngakhale Sitimamuona?
Onani zinthu zokongola zimene Mulungu analenga. Zimatithandiza kukumbukira kuti iye aliko ngakhale kuti sitingathe kumuona.
Fufuzani Anthu Oyenerera
Kufufuza anthu oyenerera si kutaya nthawi.
Uzisangalatsa Yehova
Mukhoza kumachita zinthu zoyenera n’kusangalatsa Yehova.