Zimene Ena Amanena Zokhudza Mmene Moyo Unayambira

Anthu osiyanasiyana akufotokoza zimene zinawachititsa kuti ayambe kukhulupirira kuti kuli winawake amene analenga zinthu zonse.

Monica Richardson: Dokotala Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

Akaona zimene zimachitika kuti mwana abadwe ankadzifunsa ngati zimangochitika zokha kapena ngati pali winawake amene anakonza kuti zizichitika choncho. Kodi pamapeto pake anapeza zotani pa ntchito yawo ngati dokotala?

Massimo Tistarelli: Katswiri Wopanga Maloboti Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

Zomwe ankapeza pa ntchito yawo monga wasayansi zinawachititsa kuti ayambe kukayikira ngati zamoyo zinachitadi kusintha kuchokera ku zinthu zina.

Petr Muzny: Pulofesa wa Zamalamulo Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

Pulofesa Petr Muzny anabadwa pa nthawi ya ulamuliro wachikomyunizimu. Pa nthawiyo zinkaoneka zopanda nzeru kunena kuti dzikoli linalengedwa ndi Mulungu. Kodi n’chiyani chomwe chinamuchititsa kuti asinthe maganizo?

Irène Hof Laurenceau: Dokotala Woona za Mafupa Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

Ntchito yomwe ankagwira yoikirira miyendo yochita kupanga, inachititsa kuti ayambe kukayikira zomwe ankakhulupirirazi.

Mwina Mungakondenso Kudziwa Izi

BAIBULO KOMANSO SAYANSI

Zokhudza Mmene Moyo Unayambira

Asayansi, madokotala komanso akatswiri ena akufotokoza maganizo awo a mmene moyo unayambira atayerekezera zimene anapeza ndi zimene Baibulo limanena.