Mavidiyo Othandiza Muutumiki

Mavidiyo othandiza kuyamba kukambirana ndi anthu nkhani za Baibulo.

Vidiyo Yothandiza Pogawira Kabuku Kakuti Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala

Mabanja ali pamavuto aakulu. Baibulo limapereka malangizo othandiza kuti banja likhale losangalala.

Kodi Mungakonde Kumva Uthenga Wabwino?

Baibulo lili ndi ‘uthenga wabwino wa zinthu zabwino,’ monga mmene lemba la Yesaya 52:7 limanenera. Uthenga wabwino umenewu ungakuthandizeni kuti mukhale ndi banja labwino, mupeze anzanu abwino ocheza nawo komanso kuti mukhale ndi mtendere wa mumtima.

Kodi Anthu Amene Anamwalira Adzakhalanso ndi Moyo?

Baibulo limanena kuti n’zotheka kudzakumananso ndi achibale komanso anzathu amene anamwalira akadzaukitsidwa padziko lapansi pompano.

Kodi a Mboni za Yehova ndi Anthu Otani?

Anthu ambiri amafuna atadziwa kuti a Mboni za Yehova ndi anthu otani. Onerani vidiyoyi kuti akuuzeni okha zimene amakhulupirira.