Mavidiyo Othandiza Kumvetsa Mabuku a M’Baibulo

Mfundo zothandiza kumvetsa buku lililonse la m’Baibulo.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Genesis

Buku la Genesis lili ndi mfundo zofunika zokhudza mmene anthu analengedwera komanso mmene mavuto ndi imfa zinayambira.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Ekisodo

Mulungu anapulumutsa Aisiraeli ku ukapolo ku Iguputo komanso kuwathandiza kuti akhale mtundu wodzipereka kwa iye.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Ezara

Yehova anakwaniritsa lonjezo lake pomasula anthu ake ku ukapolo ku Babulo komanso pobwezeretsa kulambira koona ku Yerusalemu.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Nehemiya

Buku la Nehemiya lili ndi mfundo zothandiza anthu onse amene akutumikira Yehova masiku ano.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Esitere

Zinthu zimene zinachitika pa nthawi ya Esitere zikhoza kulimbitsa chikhulupiriro chanu chakuti Yehova Mulungu ali ndi mphamvu yopulumutsa anthu ake akakumana ndi mavuto.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Yobu

Anthu onse amene amakonda Yehova adzakumana ndi mayesero. Nkhani ya Yobu imatithandiza kudziwa kuti tikhoza kupitiriza kukhala okhulupirika ndiponso kukhala kumbali ya Yehova.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Masalimo

Buku la Masalimo limasonyeza kuti Yehova ndi woyenera kulamulira. Limathandiza ndiponso kulimbikitsa anthu amene amamukonda komanso limasonyeza zimene Ufumu wa Mulungu udzachite posintha zinthu padzikoli.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Miyambo

Pezani malangizo ochokera kwa Mulungu othandiza pa zochitika zosiyanasiyana monga bizinezi komanso mfundo zothandiza mabanja

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Mlaliki

M’bukuli, mfumu Solomo anasiyanitsa zinthu zomwe ndi zofunika kwambiri pa moyo wathu ndi zinthu zimene zimasemphana ndi zomwe Mulungu amafuna.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Nyimbo ya Solomo

Kodi N’chifukwa chiyani bukuli limafotokoza chikondi chenicheni chimene Msulami anasonyeza kwa m’busayo kuti “lawi la Ya”?

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Yesaya

Buku la Yesaya lili ndi maulosi olondola omwe angatithandize kuti tizikhulupirira kwambiri Yehova amene ndi Wokwaniritsa malonjezo komanso yemwe ndi Mulungu wa chipulumutso chathu.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Yeremiya

Yeremiya anachita utumiki wake mokhulupirika ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto. Onani mmene chitsanzo chake chingathandizire Akhristu masiku ano.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Maliro

Linalembedwa ndi mneneri Yeremiya, buku la Maliro limafotokoza uthenga wachisoni wokhudza kuwonongedwa kwa Yerusalemu komanso kuti kulapa kumachititsa kuti Mulungu atichitire chifundo.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Ezekieli

Ezekieli anadzichepetsa n’kuchita ntchito iliyonse imene Yehova anamuuza kuti achite, ngakhale kuti zinali zovuta. Chitsanzo chake n’chothandiza kwambiri kwa ife masiku ano.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Danieli

Danieli ndi a anzake anakhalabe okhulupirika kwa Yehova pa mayesero onse amene anakumana nawo. Chitsanzo chawo komanso kukwaniritsidwa kwa maulosi a m’bukuli zimatithandiza ifenso m’masiku otsiriza ano.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Hoseya

Zimene Hoseya analosera zimatiphunzitsa zambiri ponena za mmene Yehova amasonyezera chifundo kwa anthu omwe alapa komanso zimene amafuna kuti tizichita tikamamulambira.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Yoweli

Mneneri Yoweli analosera zinthu zomwe zidzachitike pa “tsiku la Yehova” komanso ananena zimene munthu angachite kuti adzapulumuke patsikuli. Ulosi wakewu ndi wofunika kwambiri masiku ano.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Amosi

Yehova anagwiritsa ntchito munthu wodzichepetsayu kuti agwire ntchito yofunika kwambiri. Kodi tingaphunzire chiyani kwa Amosi?

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Obadiya

Buku la Obadiya ndi lalifupi kwambiri m’Malemba Achiheberi. Bukuli lili ndi uthenga wopereka chiyembekezo komanso limasonyeza kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Yona

Mneneri Yona analandira chilango chimene Yehova anamupatsa. Bukuli limasonyeza zimene anachita atapatsidwa chilangocho, mmene anachitira utumiki wake komanso mmene Yehova anamuthandizira kudziwa kufunika kokhala wachifundo komanso wokoma mtima. Zimene Yona anakumana nazo zingakuthandizeni kwambiri.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Mika

Ulosi wopezeka m’buku la Mika umatitsimikizira kuti zimene Yehova amayembekezera kwa ife ndi zoti tingazikwanitse komanso zothandiza.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Nahumu

Ulosiwu umatithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri zimene Yehova amanena komanso kuti amatonthoza anthu omwe akufunafuna mtendere ndiponso chipulumutso kudzera mu Ufumu wake.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Habakuku

Sitikayikira kuti Yehova amadziwa nthawi yabwino komanso njira yabwino yopulumutsira anthu ake.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Zefaniya

N’chifukwa chiyani tiyenera kumapewa maganizo akuti tsiku la Yehova silidzafika?

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Hagai

Bukuli likusonyeza kufunika koika zinthu zokhudza kulambira Mulungu pamalo oyamba m’moyo wathu.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Zekariya

Masomphenya komanso maulosi ambiri ankalimbikitsa anthu akale. Maulosi amenewa amatitsimikizira kuti Yehova angatithandize ndipo sangatisiye tokha.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Malaki

Bukuli lili ndi ulosi womwe umasonyeza kuti Yehova sasintha mfundo zimene amayendera, ndi wachifundo komanso wachikondi.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Mateyu

Onerani vidiyoyi kuti mudziwe mfundo zina zokhudza bukuli, lomwe ndi buku loyamba la Uthenga Wabwino.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Luka

Kodi ndi zinthu ziti zomwe zinalembedwa m’buku la Luka zomwe sizinalembedwe m’mabuku ena a Uthenga Wabwino?

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Yohane

Buku la Yohane limafotokoza mmene Yesu anasonyezera chikondi chake kwa anthu, chitsanzo chake chabwino cha kudzichepetsa komanso udindo wake wapadera wokhala Mesiya ndiponso Mfumu yam’tsogolo ya Ufumu wa Mulungu.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Machitidwe a Atumwi

Akhristu oyambirira anagwira mwakhama ntchito yolalikira kuti apange ophunzira kuchokera m’mitundu yonse. Buku la m’Baibulo la Machitidwe lingakuthandizeni kuti muzichita khama kugwira ntchito yolalikira.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Aroma

M’bukuli muli malangizo ouziridwa okhudza mmene Yehova amasonyezera kuti alibe tsankho komanso kufunika kokhulupirira Yesu Khristu.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la 1 Akorinto

Kalata ya Paulo ili ndi malangizo ouziridwa pa nkhani yochita zinthu mogwirizana, kupewa chiwerewere, kusonyeza chikondi komanso kukhulupirira kuti anthu adzaukitsidwa.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la 2 Akorinto

Yehova ndi “Tate wachifundo chachikulu ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse,” ndipo amalimbikitsa komanso kuthandiza atumiki ake.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Agalatiya

Malangizo a m’kalata ya Paulo yopita kwa Akhristu a ku Galatiya ndi othandizabe masiku ano. Angathandize Akhristu onse kuti apitirizebe kukhala okhulupirika.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Aefeso

Kalatayi ikusonyeza kuti Mulungu ali ndi cholinga choti adzabweretse mtendere komanso mgwirizano kudzera mwa Yesu Khristu.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Afilipi

Tikamapirira mayesero, timalimbikitsa ena kuti nawonso akhale ndi chikhulupiriro cholimba.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Akolose

Yehova angasangalale nafe ngati timagwiritsa ntchito zimene timaphunzira, timakhululukira ena komanso ngati timazindikira udindo komanso ulemerero umene Yesu ali nawo.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la 1 Atesalonika

Tiyenera kukhala maso, ‘kutsimikizira zinthu zonse,’ ‘kupemphera mosalekeza’ komanso kulimbikitsana.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la 1 Timoteyo

Mtumwi Paulo analemba kalata ya 1 Timoteyo pofuna kufotokoza dongosolo lomwe mpingo uyenera kuyendera. Anachenjezanso Timoteyo zokhudza ziphunzitso zonyenga ndiponso kuopsa kwa kukonda ndalama.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la 2 Timoteyo

Paulo analimbikitsa Timoteyo kuti azikwaniritsa utumiki wake.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Tito

M’kalata yomwe Paulo analembera Tito, anafotokoza za mavuto omwe anali mumpingo wa Kerete komanso anatchula zimene munthu ankayenera kukwanitsa kuti akhale mkulu mumpingo.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Filimoni

Kalata yaifupi koma yamphamvuyi ili ndi malangizo othandiza pa nkhani ya kudzichepetsa, kukoma mtima komanso kukhululuka.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Aheberi

Akhristu amalambira Mulungu m’njira yabwino kwambiri kusiyana ndi mmene Ayuda ankachitira pogwiritsa ntchito kachisi komanso nsembe zanyama.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Yakobo

Yakobo anagwiritsa ntchito mafanizo pophunzitsa mfundo zofunika kwambiri kwa Akhristu.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la 1 Petulo

M’kalata yake yoyambayi, Petulo anatilimbikitsa kuti tizichita khama potumikira Mulungu ndipo tizimutulira nkhawa zathu zonse.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la 2 Petulo

M’kalata yake yachiwiri, Petulo anatilimbikitsa kuti tiyenera kupitirizabe kukhala okhulupirika pamene tikuyembekezera kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la 1 Yohane

Kalata ya Yohane imatichenjeza za okana Khristu ndipo imatithandiza kudziwa zinthu zomwe tiyenera kuzikonda komanso zomwe sitiyenera kuzikonda.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la 2 Yohane

Kalata yachiwiri ya Yohane imatilimbikitsa kuyendabe m’choonadi komanso kukhala osamala ndi anthu achinyengo.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la 3 Yohane

Buku la 3 Yohane limasonyeza kufunika koti Akhristu azichereza ena.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Yuda

Yuda anathandiza Akhristu kuzindikira njira zachinyengo zomwe anthu ampatuko ankafuna kulowetsa mumpingo n’cholinga chofuna kusokoneza anthu.

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Chivumbulutso

M’buku la Chivumbulutso muli masomphenya omwe amasonyeza zimene Ufumu wa Mulungu udzachite pofuna kukwaniritsa cholinga chimene Mulungu anali nacho kwa anthu ndi dziko lapansili.