Kumbukirani Mkazi wa Loti

Chenjezo lomwe Yesu anapereka zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, lidakali lamphamvu ndipo ndi lofunika kwambiri. Onerani vidiyoyi kuti muone zimene a Brian Park ndi akazi awo anachita kuti ateteze banja lawo ku zinthu zomwe zikanasokoneza ubwenzi wawo ndi Yehova.

Kumbukirani Mkazi wa Loti​—Mbali Yoyamba

Onerani vidiyoyi kuti muone mavuto omwe banja lina lachikhristu linakumana nawo chifukwa choganiza kuti likhoza kumatumikira Yehova kwinaku likufunafunanso chuma.

Kumbukirani Mkazi wa Loti—Mbali Yachiwiri

Kodi ndi zinthu ziti zomwe zikhoza kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova komanso kutichititsa kutengera makhalidwe oipa a anthu a m’dzikoli?

Kumbukirani Mkazi wa Loti—Mbali Yachitatu

Yesu ananena za mkazi wa Loti ngati chenjezo kwa ife. Mkazi wa Loti akanatha kupewa tsoka lomwe linamugwera. Nkhaniyi ikutiphunzitsa kuti pali zimene ifenso tingachite kuti tipewe tsokali.