Kugwiritsa Ntchito Mfundo za M’Baibulo

Mawu a Mulungu amatithandiza kuti tiziganiza komanso kuchita zinthu mogwirizana ndi mfundo zake. Onani zitsanzo zingapo zokuthandizani kumvetsa mmene nzeru za m’Baibulo zimakhalira zothandiza.

Mukhoza Kupeza Mabwenzi Kulikonse

Tinalengedwa kuti tizikhala ndi anzathu. Ndiye kodi ndi mfundo ziti za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni kuti musankhe mwanzeru anthu oti akhale anzanu?

Yehova Mulungu Adzakuthandizani

Suchita kufunika kuti ukhale wangwiro kuti uthe kutumikira Mulungu. Amafuna kuti zikuyendere bwino ndipo adzakuthandiza sangakusiye.

Mukamamvera Uphungu Mudzakhala Anzeru

Muziganizira kwambiri za uphunguwo osati za munthu wokupatsani uphunguyo. Malangizo anzeru omwe timapatsidwa ndi akulu Achikhristu amasonyeza kuti Yehova amatikonda.