Khalani Bwenzi la Yehova—Imbani Limodzi Nafe
Nyimbozi, zomwe ndi zoti ana aziimba nawo komanso ndi za mavidiyo a makatuni, zikhoza kuwathandiza kuti aloweze mawu a nyimbo za Ufumu.
Inu Ndinu Yehova (Nyimbo 2)
Tamandani dzina lokwezeka la Yehova poimba nyimboyi.
Chilengedwe Chimatamanda Mulungu (Nyimbo 11)
Mungaphunzire zambiri zokhudza Yehova poona zimene analenga.
“Ndikufuna” (Nyimbo 17)
Kodi mungathandize bwanji anthu amene akuvutika?
Munapereka Mwana Wanu Wobadwa Yekha (Nyimbo 20)
Nyimbo imene imathandiza mabanja kuti aziyamikira chikondi chimene Yehova ndi Yesu anasonyeza popereka dipo.
Munachitira Ine Amene (Nyimbo 26)
Yehova ndi Yesu amasangalala akakuona ukugwira ntchito yolalikira komanso ntchito zina.
Tikhale pa Ubwenzi ndi Yehova (Nyimbo 106)
Kodi mukufuna mutakhala mnzake wa Mulungu? Mawu a m’nyimboyi angakuthandizeni kudziwa mmene mungachitire zimenezi.
Mulungu Adzakulimbitsa (Nyimbo 38)
Yehova angakuthandize kuti ukhale wolimba ndiponso kuti uchite zabwino.
Tikuyamikani Yehova (Nyimbo 2)
N’chifukwa chiyani mumamuthokoza Yehova? Mukamaimba mawu a m’nyimboyi, muziwerenga zifukwa zimene mungathokozere Mulungu.
Inuyo Panokha Muzikonda Kwambiri Choonadi (Nyimbo 56)
Kodi mumakonda kwambiri choonadi?
Kufufuza Anthu Okonda Mtendere (Nyimbo 58)
Mvetserani nyimbo yokoma yomwe ithandize ana kukonda anthu amitundu yonse komanso kupeza mabwenzi a Yehova padziko lonse lapansi.
“Lalikira Mawu” (Nyimbo 92)
Kodi mwakonzeka kuimba nyimbo yokhudza kulalikira mawu a Mulungu?
Fufuzani Anthu Oyenerera (Nyimbo 70)
Kodi tingamutsanzire bwanji Yesu pa nkhani yofufuza anthu oyenerera?
Tithandizeni Kukhala Olimba Mtima (Nyimbo 137)
Yehova akhoza kukuthandizani muzilimba mtima polalikira za dzina lake.
“Talawani Ndipo Muone Kuti Yehova Ndi Wabwino” (Nyimbo 95)
Phunzirani mawu a m’nyimboyi, kenako muimbe limodzi ndi munthu amene akuchita utumiki wa nthawi zonse.
Moyo wa Mpainiya (Nyimbo 140)
Uziganizira zodzachita upainiya ndipo Yehova adzakudalitsa kwambiri.
Nyimbo 83—“Kunyumba ndi Nyumba” (Nyimbo 83)
Inunso mungathandize nawo kulengeza za uthenga wa Ufumu!
Timadzipereka (Nyimbo 84)
Pali njira zosiyanasiyana zimene mungathandizire anthu ena.
Khalani Omvera Kuti Mulandire Madalitso (Nyimbo 120)
Imbani limodzi ndi Sofiya ndi Kalebe kuti mudziwe chifukwa chake kumvera kumapangitsa munthu kukhala osangalala.
Dalitsani Msonkhano Wathu (Nyimbo Nambala 20)
Muimbe nawo nyimboyi ndipo onani zimene anzanu ena amachita kuti azisonkhana ndi Akhristu anzawo nthawi zonse.
Buku la Mulungu—Ndi Chuma (Nyimbo 96)
Timaphunzira zambiri zokhudza Yehova komanso tsogolo lathu tikamawerenga mawu a Mulungu
Tigwire Ntchito Mogwirizana (Nyimbo Nambala 53)
Onani mmene abale athu amachitira zinthu mogwirizana pamsonkhano wa mayiko.
“Mulungu Ndiye Chikondi” (Nyimbo 105)
Tingatsanzire Yehova pokonda abale ndi alongo athu.
Tili ndi Zifukwa Zambiri Zokhalira Osangalala (Nyimbo 111)
Kodi ndi zinthu ziti zimakuchititsani kukhala osangalala?
Muzikhululuka (Nyimbo 130)
Muzitsanzira Yehova pokhululukira ena ndi mtima wonse.
Lambirani Yehova Mudakali Achinyamata (Nyimbo 133)
Kumbukirani Mlengi wanu Wamkulu mudakali achinyamata.
Ana Ndi Mphatso Yochokera kwa Mulungu (Nyimbo 88)
Kodi mumadziwa kuti ana ndi mphatso ya mtengo wapatali yochokera kwa Mulungu? Lowezani mawu a nyimboyi kuti muziimba nawo.
Yehova Akutipempha Mokoma Mtima Kuti: “Mwana Wanga, Khala Wanzeru” (Nyimbo 89)
Kodi mudzayesetsa kusangalatsa mtima wa Yehova? Onerani vidiyoyi kuti mudziwe mmene mungachitire zimenezi.
Yerekezerani Kuti Muli M’dziko Latsopano (Nyimbo 139)
Nyimbo yabwino kwambiri imene ingakuthandizeni kudziona muli m’paradaiso m’tsogolo ndipo Mulungu atasintha zinthu zonse kukhala zatsopano.
Moyo Ndi Wodabwitsa (Nyimbo 141)
Yeserani kuimba nyimboyi maulendo angapo kuti mukaiyimbe bwinobwino ku Nyumba ya Ufumu.
Yang’ananibe Pamphoto! (Nyimbo 24)
Mukamaimba nyimboyi, ganizirani za mmene moyo udzakhalire m’Paradaiso.
Nyimbo Yotamanda Yehova Chifukwa Wapambana (Nyimbo 132)
Tsanzirani Mose ndi Aisiraeli poimba nyimbo yotamanda Yehova.

