Pitani ku nkhani yake

Gulu Lonse la Abale

Zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, Akhristu analamulidwa kuti azikonda “gulu lonse la abale.” Kodi a Mboni za Yehova akuchita zotani pomvera lamulo limeneli? Vidiyoyi ikusonyeza njira zitatu zimene tikusonyezera chikondi pa gulu lonse la abale: 1) ntchito yolalikira, 2) kuthandiza anthu amene akuvutika, ndi 3) kusonkhana pamodzi n’kumalambira Yehova Mulungu.