Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI SAYANSI INGALOWE M’MALO MWA BAIBULO?

Kodi Sayansi Imatithandiza Bwanji?

Kodi Sayansi Imatithandiza Bwanji?

Buku lina lotanthauzira mawu limanena kuti sayansi ndi “kufufuza zachilengedwe komanso zinthu zina pofuna kudziwa mmene zimachitikira. Pofufuzapo amayeza zinthu, kuyeserera komanso kuona zotsatira zake.” Komatu kuchita zimenezi ndi ntchito yaikulu ndi yotopetsa zedi, chifukwa nthawi zambiri pamatenga nthawi yaitali akugwira ntchitoyi. Ndipotu nthawi zina sapeza n’komwe yankho la zimene akufufuzazo. Komabe nthawi zambiri amapeza zimene akufuna kudziwazo ndipo zimakhala zothandiza kwa anthufe. Taonani zitsanzo izi.

Kampani ina ya ku Europe inaphatikiza mapulasitiki ndi zinthu zina n’kupanga zosefera madzi. Zosefera madzizi zimathandiza kuti anthu azimwa madzi aukhondo, makamaka pakachitika mavuto ogwa mwadzidzidzi. Mwachitsanzo, zinathandiza kwambiri pa nthawi ya chivomerezi chomwe chinachitika ku Haiti mu 2010.

Asayansi apanga chipangizo china chothandiza kudziwa mapu a dziko lonse chotchedwa GPS. Chipangizochi chimagwiritsa ntchito setilaiti ndipo chimathandiza munthu kudziwa kumene akupita. Poyamba asilikali ndi amene ankagwiritsa ntchito GPS. Koma masiku ano imagwiritsidwanso ntchito ndi oyendetsa galimoto, oyendetsa ndege, oyenda panyanja, alenje komanso okwera mapiri. Izi zikusonyeza kuti asayansi anagwira ntchito yotamandika popanga chipangizochi chifukwa n’chothandiza kwambiri.

Ambirife timagwiritsa ntchito foni, kompyuta kapena Intaneti. Ena akafuna kupita kwinakwake amakwera ndege. Palinso anthu ambiri omwe anachira kapena kukhala ndi moyo wathanzi chifukwa cha mankhwala enaake. Zonsezi zikusonyeza kuti zimene asayansi apanga, zimatithandiza m’njira zosiyanasiyana.

KODI SAYANSI YAFIKA PATI MASIKU ANO?

Asayansi akufufuza chilengedwechi kuti adziwe zambiri. Ena akuyesetsa kufufuza zambiri zokhudza maatomu. Pomwe ena akufufuza zomwe zinachitika zaka mabiliyoni apitawo n’cholinga choti adziwe kuti zinthu zamoyo zinachokera kuti. Asayansi enanso afika kutali kwambiri m’mlengalenga ndipo amaona kuti Mulungu yemwe amatchulidwa m’Baibulo akanakhala kuti alipodi, bwenzi atamupeza.

Wolemba mabuku wina dzina lake Amir D. Aczel ananena kuti “asayansi komanso afilosofi ena atafufuza kwambiri, anayamba kukayikira zoti Mulungu alipo.” Mwachitsanzo, wasayansi wina wotchuka padziko lonse ananena kuti: “Popeza sitinapeze umboni uliwonse wosonyeza kuti kuli Mulungu yemwe analenga zinthu, m’pomveka kuganiza kuti Mulunguyo kulibe.” Ena amaganiza kuti si zoona kuti kuli Mulungu wotchulidwa m’Baibulo ndipo nkhani zonena za zimene Mulungu ankachita, n’zongofuna kupusitsa anthu. Amaonanso kuti amene amakhulupirira zimenezi amangokhulupirira zamatsenga. *

 Komabe, kodi panopa asayansi akudziwa zonse zokhudza chilengedwechi moti zonse zomwe anganene zingakhale zolondola? Ayi. N’zoona kuti sayansi yapita patsogolo kwambiri, komabe asayansi ambiri amadziwa kuti padakali zinthu zambiri zomwe sakuzidziwa komanso zoti sangathe kuzidziwa. Wasayansi wina, dzina lake Steven Weinberg, anati: “Ngakhale titayesetsa bwanji, sitidzadziwa zonse.” Pulofesa wina, dzina lake Martin Rees, ananenanso kuti: “Pali zinthu zambiri zimene anthufe sitingathe kuzimvetsa.” Apa mfundo ndi yakuti, ngakhale kuti sayansi yapita patsogolo, asayansi sangatithandize kudziwa zonse. Taonani zitsanzo zotsatirazi.

  • Asayansi samvetsa zimene zimachitika mkati mwa selo. Sakudziwa bwinobwino kuti maselo amagwiritsa ntchito bwanji mphamvu zimene amapeza kuchokera ku dzuwa, zakudya ndi zinthu zina. Sakudziwanso kuti maselowa amapanga bwanji mapuloteni komanso kuti amachulukana bwanji.

  • Mphamvu yokoka ya dziko lapansi imathandiza kwambiri. Komatu asayansi sadziwa bwinobwino mmene mphamvuyi imagwirira ntchito. Mwachitsanzo, sadziwa kuti mphamvuyi imatikokera bwanji pansi tikadumpha m’mwamba. Sadziwanso mmene mphamvuyi imathandizira kuti mwezi uzizungulira dziko lapansili.

  • Asayansi ena amaganiza kuti 95 peresenti ya zinthu zakuthambo ndi zinthu zosaoneka ndipo ngakhale atagwiritsa ntchito zipangizo zawo sangathe kuzitulukira. Asayansiwa sadziwanso mmene zinthu zimenezi zimagwirira ntchito.

Wasayansi winanso wotchuka anati: “Zinthu zimene timadziwa ndi zochepa kwambiri poyerekeza ndi zimene sitidziwa. Choncho wasayansi sayenera kumangokhutira ndi zomwe amadziwa. Ineyo ndimaona kuti ukamafufuza zambiri za sayansi, m’pamene umaonanso kuti pali zambiri zomwe sudziwa.”

Ndiyeno ngati mumaona kuti sayansi yangotsala pang’ono kulowa m’malo mwa Baibulo kapena kupangitsa anthu kuti asamakhulupirire Mulungu, mungachite bwino kuganizira mfundo iyi: Ngati akatswiri asayansi omwe ali ndi zipangizo zamphamvu kwambiri sakudziwabe zonse zokhudza chilengedwechi, kodi ndi bwino kufulumira kuganiza kuti Mulungu kulibe chifukwa choti asayansi sanapeze umboni woti alipo? Mpake kuti buku lina limanena kuti, “ngakhale kuti sayansi yapita patsogolo kwambiri, zimene tikudziwa panopa sizikusiyana kwenikweni ndi zimene akatswiri ofufuza zakuthambo akale, monga a ku Babulo, ankadziwa zaka 4,000 zapitazo. Zikuoneka kuti padakali zambiri zimene sitikuzidziwa.”—Encyclopedia Britannica.

A Mboni za Yehova amadziwa kuti aliyense ali ndi ufulu wosankha zimene akufuna kukhulupirira pa nkhaniyi. Amachita zimenezi chifukwa amatsatira mfundo ya m’Baibulo yakuti: “Anthu onse adziwe kuti ndinu ololera.” (Afilipi 4:5) Komabe, tikukupemphani kuti muone kugwirizana kwa zimene asayansi apeza ndi zimene Baibulo limanena pa nkhani zasayansi.

^ ndime 9 Anthu ena sakhulupirira Baibulo chifukwa cha zimene matchalitchi ena amaphunzitsa. Matchalitchiwa amaphunzitsa kuti dziko lapansili ndiye pakati pa chilengedwe chonse komanso kuti Mulungu analenga dzikoli m’masiku 6 enieni a maola 24.—Onani bokosi lakuti, “ Baibulo Silitsutsana Ndi Mfundo Zolondola Zasayansi.”