NKHANI YA PACHIKUTO | KODI UFUMU WA MULUNGU UDZAKUCHITIRANI CHIYANI?
Yesu Amaona Kuti Ufumu wa Mulungu Ndi Wofunika Kwambiri
Yesu ali padziko lapansi, anaphunzitsa otsatira ake zinthu zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, anawaphunzitsa mmene angapempherere, zimene angachite kuti azisangalatsa Mulungu ndiponso zimene angachite kuti akhale osangalala. (Mateyu 6:5-13; Maliko 12:17; Luka 11:28) Koma nkhani imene sinkachoka pakamwa pake inali yokhudza Ufumu wa Mulungu.—Luka 6:45.
Monga taonera m’nkhani yoyamba ija, ntchito yaikulu imene Yesu ankagwira inali ‘yolalikira ndi kulengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu.’ (Luka 8:1) Iye anagwira ntchitoyi modzipereka kwambiri ndipo ankayenda mitunda italiitali m’madera onse a m’dziko la Isiraeli. Anachita zonsezi n’cholinga chofuna kuphunzitsa anthu za Ufumu wa Mulungu. Zimene Yesu anachita pa utumiki wake zinalembedwa m’Mauthenga Abwino, ndipo m’mabuku amenewa nkhani yonena za Ufumu wa Mulungu yatchulidwa koposa ka 100. Pa maulendo 100 amenewa, ambiri ndi mawu a Yesu. Koma n’kuthekanso kuti Yesu anatchula za Ufumu kambiri kuposa pamenepa.—Yohane 21:25.
N’chifukwa chiyani Yesu ankaona kuti Ufumu wa Mulungu ndi wofunika kwambiri? Chifukwa ankadziwa kuti Mulungu anasankha iyeyo kuti akhale Mfumu ya Ufumu umenewu. (Yesaya 9:6; Luka 22:28-30) Komatu sikuti maganizo a Yesu anali pa kufuna kulamulira kapena kutchuka. (Mateyu 11:29; Maliko 10:17, 18) Akamalengeza za Ufumu, sikuti ankangoganizira phindu limene iyeyo angapeze. Koma ankaganizira kwambiri mmene Ufumuwu udzathandizire kuti dzina la Atate wake wakumwamba liyeretsedwe komanso zimene Ufumuwu udzachitire otsatira ake.
UFUMUWU UDZAYERETSA DZINA LA ATATE WAKE
Yesu amakonda kwambiri Atate wake wakumwamba. (Miyambo 8:30; Yohane 14:31) Amawakonda chifukwa Atate wakewo ali ndi makhalidwe abwino kwambiri monga chikondi, chifundo komanso chilungamo. (Deuteronomo 32:4; Yesaya 49:15; 1 Yohane 4:8) Choncho Yesu sasangalala akamamva mabodza amene anthu amanena okhudza Atate wake. Ena mwa mabodzawa ndi akuti, Mulungu alibe nazo kanthu za mavuto a anthu komanso iye amafuna kuti tizivutika. Yesu ‘ankalalikira uthenga wabwino wa ufumu’ mofunitsitsa chifukwa ankadziwa kuti Ufumuwu udzayeretsa dzina la Atate wake. (Mateyu 4:23; 6:9, 10) Kodi udzachita bwanji zimenezi?
Yehova adzasintha zinthu padzikoli pogwiritsa ntchito Ufumuwu. Pa nkhani imeneyi, Baibulo limati: “Iye adzapukuta misozi yonse” m’maso mwa anthu okhulupirika. Mulungu adzachotsa zonse zimene zimapangitsa kuti anthu azilira ndipo “imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.” (Chivumbulutso 21:3, 4) Mulungu adzagwiritsa ntchito Ufumu wake kuchotsa mavuto onse amene anthu akukumana nawo. *
Ndiyetu m’pake kuti Yesu ankaphunzitsa anthu za Ufumu wa Mulungu mwakhama. Ankadziwa kuti Ufumuwu udzasonyeza kuti Atate wake ndi wamphamvu komanso wachifundo. (Yakobo 5:11) Yesu ankadziwanso kuti Ufumuwu udzathandizanso anthu okhulupirika.
UFUMUWU UDZABWERETSA MADALITSO AMBIRI KWA ANTHU OKHULUPIRIKA
Yesu asanabwere padziko lapansi, anakhala nthawi yaitali ndi Atate wake kumwamba. Mulungu anagwiritsa ntchito Mwana wakeyu polenga zinthu zonse zakumwamba ndi zapadziko lapansi. (Akolose 1:15, 16) Koma pa zonsezi, zimene Yesu ankasangalala nazo kwambiri “zinali zokhudzana ndi ana a anthu.”—Miyambo 8:31.
Ngakhalenso pamene ankachita utumiki wake padziko lapansi, Yesu ankakonda kwambiri anthu. Atangoyamba kumene utumiki wake ananena momveka bwino kuti anabwera padziko lapansi ‘kudzauza anthu osauka uthenga wabwino.’ (Luka 4:18) Koma sikuti Yesu ankangonena kuti anabwera kudzauza anthu uthenga wabwino. Nthawi zambiri ankachita zinthu zosonyeza kuti amakonda anthu. Mwachitsanzo, pa nthawi ina khamu la anthu litasonkhana kuti limvetsere ulaliki wake, “anawamvera chisoni, ndi kuwachiritsira anthu awo odwala.” (Mateyu 14:14) Pa nthawi inanso munthu wina wakhate, yemwe ankakhulupirira kuti Yesu akhoza kumuchiritsa atafuna, anamupempha kuti amuchiritse. Yesu anagwidwa chifundo ndipo anauza munthuyo kuti: “Ndikufuna. Khala woyera.” (Luka 5:12, 13) Komanso Yesu ataona Mariya akulira maliro a mchimwene wake Lazaro, “anadzuma povutika mumtima,” ‘anamva chisoni’ ndipo kenako “anagwetsa misozi.” (Yohane 11:32-36) Ndiyeno anachita zinthu zoti anthu sankayembekezera. Iye anaukitsa Lazaro ngakhale kuti panali patatha masiku 4 ali m’manda.—Yohane 11:38-44.
Komabe Yesu ankadziwa kuti zabwino zimene ankachitira anthu zinali zakanthawi chabe. Ankadziwa kuti pakapita nthawi, anthu amene anawachiritsawo akhoza kudwalanso komanso amene anawaukitsa akhoza kufanso. Iye ankadziwanso kuti Ufumu wa Mulungu ndi umene udzathetseretu mavuto onse a anthu. Choncho sankangochiritsa kapena kuukitsa anthu, koma ankalalikiranso mwakhama “uthenga wabwino wa ufumu.” (Mateyu 9:35) Zozizwitsa zimene Yesu anachita, zinali chitsanzo chochepa chabe cha zimene Ufumu wa Mulungu udzachite padziko lonse. Taonani malonjezo a m’Baibulo osonyeza mmene zinthu zidzakhalire pa nthawiyo.
Sikudzakhalanso matenda.
“Pa nthawi imeneyo, maso a anthu akhungu adzatsegulidwa, ndipo makutu a anthu ogontha adzayamba kumva. Pa nthawiyo, munthu wolumala adzakwera phiri ngati mmene imachitira mbawala yamphongo. Lilime la munthu wosalankhula lidzafuula mokondwa.” Komanso “palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”—Yesaya 33:24; 35:5, 6.
Anthu sazidzafanso.
“Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 37:29.
“Iye adzameza imfa kwamuyaya ndipo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzapukuta misozi pankhope zonse za anthu.”—Yesaya 25:8.
Anthu omwe anamwalira adzaukitsidwa.
“Onse ali m’manda achikumbutso adzamva mawu ake ndipo adzatuluka.”—Yohane 5:28, 29.
“Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.”—Machitidwe 24:15.
Aliyense adzakhala ndi nyumba komanso ntchito yabwino.
“Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake. Sadzamanga wina n’kukhalamo. Sadzabzala wina n’kudya. . . . Anthu anga osankhidwa mwapadera adzapindula mokwanira ndi ntchito ya manja awo.”—Yesaya 65:21, 22.
Sikudzakhalanso nkhondo.
“Akuletsa nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”—Salimo 46:9.
“Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake, ndipo anthuwo sadzaphunziranso nkhondo.”—Yesaya 2:4.
Kudzakhala chakudya cha mwanaalirenji.
“Dziko lapansi lidzapereka zipatso zake. Mulungu, ndithu Mulungu wathu, adzatidalitsa.”—Salimo 67:6.
“Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri. Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.”—Salimo 72:16.
Umphawi udzatha.
“Waumphawi sadzaiwalidwa nthawi zonse.”—Salimo 9:18.
“Pakuti adzalanditsa wosauka wofuulira thandizo, komanso wosautsika ndi aliyense wopanda womuthandiza. Adzamvera chisoni munthu wonyozeka ndi wosauka, ndipo adzapulumutsa miyoyo ya anthu osauka.”—Salimo 72:12, 13.
Mukaganizira zinthu zabwino zonsezi zimene Ufumu wa Mulungu udzachite, kodi mukuona chifukwa chake Yesu ankaona kuti Ufumu wa Mulungu ndi wofunika kwambiri? Iye ali padziko lapansi ankafunitsitsa kuuza munthu aliyense za Ufumu wa Mulungu. Ankachita izi chifukwa ankadziwa kuti Ufumuwu udzathetsa mavuto onse padzikoli.
Kodi inuyo mukulakalaka kudzasangalala ndi zinthu zabwino zimene Ufumu wa Mulungu udzachite? Kodi mukufuna kudziwa zambiri za Ufumuwu? Nanga mungatani kuti mudzakhalepo pa nthawi imene Ufumuwu udzabweretse madalitso osanenekawa padzikoli? Nkhani yotsatira ili ndi mayankho a mafunso amenewa.
^ ndime 8 Kuti mudziwe chifukwa chake Mulungu amalola kuti anthu azivutika, onani mutu 11 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.