Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 KUCHEZA NDI MUNTHU WINA

Kodi Ufumu wa Mulungu Unayamba Liti Kulamulira? (Gawo 1)

Kodi Ufumu wa Mulungu Unayamba Liti Kulamulira? (Gawo 1)

Nkhani ili m’munsiyi ikusonyeza mmene a Mboni za Yehova amachitira akamakambirana ndi anthu nkhani za m’Baibulo. Tiyerekeze kuti munthu wina wa Mboni, dzina lake Cameron, wafika pakhomo pa Bambo Jon.

MUZIFUFUZA KUTI MUDZIWE ZOONA

Cameron: Ndimasangalala kwambiri kuphunzira nanu Baibulo bambo. * Paja mlungu watha munafunsa funso lokhudza Ufumu wa Mulungu ndipo ndikukumbukira kuti funso lake linali lakuti, ‘N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova mumakhulupirira kuti ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira mu 1914?’

Jon: Ee, ndinawerenga m’buku lanu lina kuti Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira mu 1914. Zimenezi zinandidabwitsa kwambiri chifukwa paja inu mumanena kuti zonse zomwe mumakhulupirira zimachokera m’Baibulo.

Cameron: N’zoona, zimachokeradi m’Baibulo.

Jon: Koma ineyo ndinawerengapo Baibulo lonse koma sindinaone paliponse patalembedwa chaka cha 1914. Ndinafufuzanso m’Baibulo la pa Intaneti, koma chakachi sichinapezeke n’komwe.

Cameron: Ndikufuna kukuthokozani pa zifukwa ziwiri izi: Choyamba, chifukwa choti munawerengapo Baibulo lonse. Zimenezi zikusonyeza kuti mumakonda Mawu a Mulungu.

Jon: Zoona. Ndimaona kuti Baibulo ndi losiyana ndi mabuku ena onse.

Cameron: Ndi bukudi lapadera. Chifukwa chachiwiri, munachita bwino kufufuza m’Baibulo kuti mupeze yankho la funso lanu. Zimene munachitazi zikugwirizana ndi zimene Baibulo limanena. Limatilimbilikitsa kuti tikakhala ndi funso tizifufuza kuti tipeze yankho lake. * Khama lotereli limathandiza.

Jon: Zikomo kwambiri. Ndimachita zimenezi chifukwa ndikufuna kudziwa zambiri. Ndipotu ndinafufuzanso m’buku limene tikuphunzirali ndipo ndinapeza nkhani ina yonena za chaka chimenechi. Sindingathe kufotokoza bwinobwino, koma ananena za mfumu ina imene inalota mtengo waukulu womwe unadulidwa ndipo kenako unaphukiranso.

Cameron: Ndaidziwa nkhani imeneyi. Ndi ulosi wopezeka pa Danieli chaputala 4. Amene analota maloto amenewa ndi Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo.

Jon: Ndi yemweyodi. Nkhani imeneyi ndaiwerenga kangapo. Koma kunena zoona sindinamvetsebe kugwirizana pakati pa Ufumu wa Mulungu ndi chaka cha 1914.

Cameron: Nkhani imeneyi ndi yovutadi kumvetsa. Mneneri Danieli ndi amene anauziridwa kulemba nkhaniyi. Koma nayenso sanamvetse tanthauzo lake.

Jon: Oo.

Cameron: Ee. Taonani zimene iye analemba pa Danieli 12:8. “Tsopano ine ndinamva zimene ananenazo, koma sindinadziwe tanthauzo lake.”

Jon: Si ine ndekha eti. Zimenezi zandilimbitsa mtima.

Cameron: Mfundo ndi yakuti, Danieli sanamvetse tanthauzo la mawuwa chifukwa sinali nthawi imene Mulungu ankafuna kuti anthu adziwe tanthauzo lonse  la maulosi a m’buku la Danieli. Koma panopa tingathe kumvetsa tanthauzo la maulosi amenewa.

Jon: Oo. Chifukwa?

Cameron: Kuti tidziwe chifukwa chake, tiyeni tiwerengenso vesi lotsatira, vesi 9. Akuti: “Mawuwa asungidwa mwachinsinsi ndipo atsekedwa ndi kumatidwa kufikira nthawi yamapeto.” Choncho anthu akanamvetsa maulosi amenewa m’tsogolo, kapena kuti “nthawi yamapeto.” Ndipotu monga mmene tidzaphunzirire kutsogoloku, pali umboni wonse wosonyeza kuti nthawi ya mapetoyo ndi inoyo. *

Jon: Ndiye kodi mungandifotokozere bwinobwino tanthauzo la ulosi wa m’buku la Danieliwu?

Cameron: Sikuti ineyo ndikudziwa zonse, komabe ndiyesetsa kukufotokozerani zimene ndikudziwa.

MALOTO A MFUMU NEBUKADINEZARA

Cameron: Ndiyamba ndi kufotokoza mwachidule zimene Nebukadinezara analota. Kenako tikambirana tanthauzo lake.

Jon: Chabwino.

Cameron: Mfumu Nebukadinezara inalota mtengo wautali kufika kumwamba. Kenako inamva mngelo akulamula kuti mtengowo udulidwe, koma chitsa chake achisiye. Anati pakatha “nthawi zokwanira 7” mtengowo udzaphukanso. * Ulosiwu unakwaniritsidwa koyamba pa Mfumu Nebukadinezara. Ngakhale kuti iye anali mfumu yotchuka ngati mtengo wofika kumwamba, anachotsedwa pa udindo kuti asakhalenso mfumu mpaka zitatha “nthawi zokwanira 7.” Kodi mukukumbukira zimene zinachitika?

Jon: Ayi. Sindikukumbukira kwenikweni.

Cameron: Musadandaule. Baibulo limanena kuti Nebukadinezara anachita misala kwa zaka 7 ndipo sankalamuliranso monga mfumu. Nthawi imeneyi itatha, Nebukadinezara anakhala bwinobwino ndipo anayambanso kulamulira. *

Jon: Ndamvetsa zimene mwafotokozazi. Komano zikugwirizana bwanji ndi nkhani yokhudza Ufumu wa Mulungu komanso chaka cha 1914?

Cameron: Mwachidule, tingati ulosiwu unakwaniritsidwa m’njira ziwiri. Unakwaniritsidwa koyamba pa nthawi imene Nebukadinezara anasiya kulamulira. Njira yachiwiri imene ulosiwu unakwaniritsidwira ndi pamene ulamuliro wa Mulungu unasokonekera. Koma kukwaniritsidwa kwachiwiriku n’kumene kukukhudzana ndi nkhani ya Ufumu wa Mulungu.

Jon: Mukudziwa bwanji kuti ulosiwu unakwaniritsidwa m’njira ziwiri, komanso kuti njira yachiwiriyo ndi yokhudzana ndi Ufumu wa Mulungu?

Cameron: Chinthu choyamba chimene tikudziwira zimenezi ndi zimene ulosiwu ukunena. Malinga ndi zimene lemba la Danieli 4:17 likunena, ulosiwu unaperekedwa “ndi cholinga chakuti anthu adziwe kuti Wam’mwambamwamba ndiye Wolamulira wa maufumu a anthu, ndiponso adziwe kuti iye akafuna kupereka ulamuliro kwa munthu aliyense, amamupatsa.” Kodi mwaona kuti vesili lanena kuti “Wolamulira wa maufumu a anthu?”

Jon: Ee, lanena kuti “Wam’mwambamwamba ndiye Wolamulira wa maufumu a anthu.”

Cameron: Zoona. Ndiye mukuganiza kuti “Wam’mwambamwamba” ameneyu ndi ndani?

Jon: Ayenera kuti ndi Mulungu.

Cameron: Mwalondola. Choncho, zimenezi zikutithandiza kudziwa kuti ulosiwu sikuti ukungonena za Nebukadinezara. Ukunenanso za “maufumu a anthu” kapena kuti ulamuliro wa Mulungu pa anthu. Zimenezi n’zomveka tikaganizira zimene nkhani yonse yokhudza ulosiwu imanena.

Jon: Mukutanthauza chiyani?

MFUNDO YAIKULU YA M’BUKU LA DANIELI

Cameron: Kawirikawiri nkhani za m’buku la Danieli, zimanena mfundo imodzi mobwerezabwereza. Zimanena za kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Mulungu womwe wolamulira wake ndi Yesu. Mwachitsanzo, tiyeni tione zimene lemba la Danieli 2:44 limanena. Mungaliwerenge?

Jon: Chabwino. Likuti: “M’masiku a mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse. Ufumuwo sudzaperekedwa kwa mtundu wina uliwonse wa anthu, koma udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo, ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.”

Cameron: Zikomo kwambiri. Kodi mukuganiza kuti vesili likunena za Ufumu wa Mulungu?

Jon: Aa. Mwina kapena.

 Cameron: Vesili lanena kuti Ufumuwu “udzakhalapo mpaka kalekale.” Ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene ungakhalepo mpaka kalekale. Nanga pali ufumu uliwonse wa anthu umene ungakhalepo mpaka kalekale?

Jon: Ayidi.

Cameron: Tiyeni tionenso ulosi wina umene umanena za Ufumu wa Mulungu. Ulosiwu ukupezeka pa Danieli 7:13, 14. Ponena za mfumu ya Ufumuwu, ulosiwu umati: “Anamupatsa ulamuliro, ulemerero, ndi ufumu kuti anthu a mitundu yosiyanasiyana, olankhula zinenero zosiyanasiyana azimutumikira. Ulamuliro wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo sudzatha. Ufumu wake sudzawonongedwa.” Kodi ndi mawu ati mu ulosiwu amene akufanana ndi amene ali mu vesi tinawerenga lija?

Jon: Lembali lanenanso za ufumu.

Cameron: Mwalondola. Ndipotu si ufumu wamba. Mwina mwaona kuti lembali likunena kuti Ufumuwu udzalamulira ‘anthu a mitundu yosiyanasiyana komanso olankhula zinenero zosiyanasiyana.’ M’mawu ena tingati, Ufumuwu udzalamulira dziko lonse lapansi.

Jon: Sindimadziwa kuti lembali likutanthauza zimenezi. Koma ndikuona kuti n’zomveka.

Cameron: Ulosiwu ukunenanso kuti: “Ulamuliro wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo sudzatha. Ufumu wake sudzawonongedwa.” Zimene ulosiwu ukunena zikugwirizana ndi zimene tawerenga pa Danieli 2:44 paja, si choncho?

Jon: Zikugwirizanadi.

Cameron: Zoona zimenezo. Tsopano tiyeni tikumbutsane mwachidule zimene takambirana. Taona kuti ulosi wa m’buku la Danieli chaputala 4 unalembedwa n’cholinga choti anthu adziwe kuti “Wam’mwambamwamba ndiye Wolamulira wa maufumu a anthu.” Zimenezi zikusonyeza kuti ulosiwu unakwaniritsidwa m’njira ina yofunika kwambiri kuposa mmene unakwaniritsidwira kwa Mfumu Nebukadinezara. Komanso taona kuti m’buku la Danieli muli maulosi ambiri onena za kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Mulungu, womwe wolamulira wake ndi Yesu. Ndiye kodi inuyo simukuona kuti m’pomveka kunena kuti ulosi wa m’buku la Danieli chaputala 4 umanenanso za Ufumu wa Mulungu?

Jon: Ndikuganiza kuti n’zomvekadi. Komabe sindikuona kugwirizana kwa zimenezi ndi chaka cha 1914.

“PADUTSE NTHAWI ZOKWANIRA 7”

Cameron: Tiyeni tikambiranenso nkhani ya Mfumu Nebukadinezara. Mwina mwakumbukira kuti mfumuyi inkaimiridwa ndi mtengo mu ulosi takambirana koyamba uja. Ulamuliro wake unasokonekera pa nthawi imene mtengowo unadulidwa n’kukhala nthawi zokwanira 7 usanaphukirenso. Nthawi imeneyi ndi imene Nebukadinezara anachita misala. Nthawi zokwanira 7 zimenezi zinatha pamene anachira n’kuyambanso kulamulira. Pa kukwaniritsidwa kwachiwiri kwa ulosiwu, ulamuliro wa Mulungu unasokonekera kwa nthawi ndithu koma osati chifukwa choti Mulungu analephera kulamulira.

Jon: Mukutanthauza chiyani pamenepa?

Cameron: Kale, mafumu a ku Isiraeli omwe ankalamulira ku Yerusalemu ankaonedwa kuti akhala “pampando wachifumu wa Yehova.” * Mafumuwa ankaimira Mulungu polamulira Aisiraeli. Choncho akamalamulira, ankakhala ngati akhala pampando wachifumu wa Yehova. Koma patapita nthawi, mafumuwa anasiya kumvera Mulungu ndipo Aisiraeli ambiri anatengeranso chitsanzo chawochi. Chifukwa cha kusamvera kwawoku, Mulungu analola kuti agonjetsedwe ndi a Babulo mu 607 B.C.E. Kuchokera nthawi imeneyi panalibenso mfumu imene inkaimira  Yehova ku Yerusalemu. Apa tinganene kuti ulamuliro wa Mulungu unasokonekera. Tili limodzi?

Jon: Ee. Tili limodzi.

Cameron: Choncho, nthawi zokwanira 7, kapena kuti nthawi imene ulamuliro wa Mulungu unasokonekera, zinayambira mu 607 B.C.E. Ulosi uja unanena kuti pamapeto pa nthawi zokwanira 7 zimenezi, Mulungu anayenera kudzaika mfumu yatsopano yochokera kumwamba, imene ikanaimira Mulunguyo. Pa nthawi imeneyi ndi pamenenso maulosi ena a m’buku la Danieli ankayenera kukwaniritsidwa. Ndiye funso lofunika ndi lakuti: Kodi nthawi zokwanira 7 zimenezi zinatha liti? Tikapeza yankho la funso limeneli, tidziwanso nthawi imene Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira.

Jon: Oo ndamvetsa tsopano. Ndikuganiza kuti nthawi zokwanira 7 zimenezi zinatha mu 1914. Ndalondola?

Cameron: Ee mwalondola.

Jon: Koma tingatsimikize bwanji kuti nthawizi zinathadi mu 1914?

Cameron: Yesu ali padziko lapansi anasonyeza kuti pa nthawi imeneyo, nthawi zokwanira 7 zija zinali zisanathe. * Choncho, nthawi imeneyi inali yaitali ndithu. Nthawi zokwanira 7 zimenezi zinayamba zaka zambiri Yesu asanabwere padziko lapansi ndipo zinapitirirabe mpaka patadutsa nthawi yaitali Yesu atabwerera kumwamba. Kumbukiraninso kuti lemba lija linasonyeza kuti tanthauzo la maulosi a m’buku la Danieli linayenera kudzadziwika bwinobwino “nthawi yamapeto.” * N’zochititsa chidwi kuti chakumapeto kwa zaka za m’ma 1800, Ophunzira Baibulo anafufuza mosamala kwambiri ulosiwu komanso maulosi ena kuti adziwe tanthauzo lake. Iwo anazindikira kuti nthawi zokwanira 7 zinkayenera kuthera mu 1914. Zimene zakhala zikuchitika kuyambira mu 1914 zikusonyezadi kuti Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira kumwamba m’chaka chimenechi. M’chakachi, ndi pamenenso masiku otsiriza kapena kuti nthawi ya mapeto inayamba. Takambiranatu zambiri, ndipo ndikudziwa kuti n’zovuta kumvetsa zonse. . . .

Jon: Ee. N’zovutadi kumvetsa. Ndiwerenganso nkhani imeneyi kuti ndiimvetse bwino.

Cameron: Musadandaule. Inenso zinanditengera nthawi kuti ndimvetse bwinobwino maulosiwa komanso mmene anakwaniritsidwira. Koma pa zimene takambiranazi, ndikukhulupirira kuti mwaona kuti zimene a Mboni za Yehova amakhulupirira zokhudza Ufumu wa Mulungu, n’zochokera m’Baibulo.

Jon: Ee ndaonadi choncho. Ndimachita chidwi ndi mmene mumagwiritsira ntchito Baibulo pofotokoza zomwe mumakhulupirira.

Cameron: Ndikuona kuti inunso mumadalira kwambiri Baibulo. Koma monga ndanenera, simungamvetse zonsezi bwinobwino nthawi imodzi. N’kutheka kuti mulinso ndi mafunso ena. Mwachitsanzo, takambirana kuti ulosi wa nthawi zokwanira 7 umanenanso za Ufumu wa Mulungu ndipo nthawi zimenezi zinayamba mu 607 B.C.E. Koma kodi a Mboni za Yehova anawerengetsera bwanji kuti adziwe kuti nthawi zokwanira 7 zimenezi zinathadi mu 1914? *

Jon: Funso limeneli ndi lozunguzadi.

Cameron: Baibulo lingatithandize kudziwa kutalika kwa nthawi zokwanira 7 zimenezi. Kodi mungakonde kuti tidzakambirane nkhani imeneyi ndikadzabweranso? *

Jon: Mudzabweredi kuti tidzakambirane.

Kodi pali nkhani inayake ya m’Baibulo imene simumaimvetsa? Kapena mumafuna mutadziwa zimene a Mboni za Yehova amakhulupirira? Ngati ndi choncho, funsani a Mboni za Yehova ndipo adzasangalala kwambiri kukambirana nanu.

^ ndime 5 Pali njira imene a Mboni za Yehova amagwiritsa ntchito pophunzira Baibulo kwaulere ndi anthu. Iwo amaphunzira ndi anthu kunyumba kwawo nkhani zosiyanasiyana za m’Baibulo.

^ ndime 63 Yesu analosera zimene zidzachitike m’masiku otsiriza kuti: “Anthu a mitundu ina adzapondaponda Yerusalemu [amene akuimira ulamuliro wa Mulungu], kufikira nthawi zoikidwiratu za anthu a mitundu inawo zitakwanira.” (Luka 21:24) Choncho, pa nthawi imene Yesu anali padziko lapansili, ulamuliro wa Mulungu unali udakali wosokonekera mpaka nthawi ya mapeto.

^ ndime 67 Kuti mudziwe zambiri, werengani za kumapeto pa mutu wakuti ”1914 ndi Chaka Chofunika Kwambiri M’maulosi a Baibulo” m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?

^ ndime 69 Nkhani yotsatira idzafotokoza mavesi a m’Baibulo amene angatithandize kudziwa kutalika kwa nthawi zokwanira 7 zimenezi.