Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO | YOSEFE

“Tamverani Maloto Amene Ine Ndinalota”

“Tamverani Maloto Amene Ine Ndinalota”

YOSEFE ankati akayang’ana chakum’mawa, komwe kunkaoneka mapiri, ankangolakalaka atapeza mpata wothawa. Kuseri kwa mapiriwo kunali dera lotchedwa Heburoni ndipo ndiye kunali kwawo. Mwina pa nthawiyi n’kuti bambo ake, Yakobo atakhala pansi phee akupuma, osadziwa zimene zachitikira mwana wawo wokondedwayu. Nayenso Yosefe ankawakonda kwambiri bambo akewa. Koma pa nthawiyi ankangoona kuti basi sadzawaonanso. Yosefe anali ali pakati pa gulu la anthu amalonda omwe anali ndi ngamila, ndipo ankapita naye ku Iguputo. Anthuwa anali atam’gula ndipo ankaonetsetsa kuti asapeze mpata wothawa. Iwo ankaona kuti mnyamatayu ndi katundu wa mtengo wapatali woti akawapezetsa ndalama zankhaninkhani ku Iguputo.

Pa nthawiyi n’kuti Yosefe ali ndi zaka 17 zokha. Ndiye yerekezani kuti mukumuona akuyang’ana kumadzulo pamene dzuwa likulowa. Iye akuona kuti moyo wake wasinthiratu ndipo sakudziwa kuti chimuchitikire n’chiyani. Sakumvetsa kuti azichimwene ake enieni amafuna kumupha ndipo kenako amugulitsa ngati kapolo. N’kutheka kuti Yosefe akaganizira zimenezi ankagwetsa misozi ndipo sankadziwa kuti tsogolo lake likhala lotani.

Ngakhale kuti Yosefe anali kapolo, sanasiye kukhulupirira Mulungu

Koma kodi chinachititsa n’chiyani kuti akumane ndi mavuto amenewa? Ndipo tingaphunzire chiyani kwa mnyamatayu, amene anazunzidwa komanso kugulitsidwa ndi abale ake enieni?

BANJA LOMWE ANAKULIRA

Banja limene Yosefe anakulira linali lalikulu kwambiri koma linali losasangalala komanso losagwirizana. Zimene Baibulo limafotokoza zokhudza banja la Yakobo zimasonyezeratu kuti mitala imayambitsa mavuto ambiri. Komabe pa nthawiyi Mulungu ankalola anthu kukwatira mitala mpaka pamene Mwana wake anabwezeretsa zimene Mulunguyo anakhazikitsa poyamba, zoti munthu azikhala ndi mkazi mmodzi. (Mateyu 19:4-6) Yakobo anali ndi ana 14 koma anabereka anawa ndi akazi 4. Akaziwa anali Leya ndi Rakele komanso akapolo awo Zilipa ndi Biliha. Koma mkazi amene Yakobo anamukonda poyamba anali Rakele, yemwe anali wokongola kwambiri. Yakobo sankakonda kwambiri Leya, mchemwali wake wa Rakele. Iye anakwatira Leyayo, apongozi ake atam’pusitsa. Azimayi awiriwa ankadana koopsa ndipo zimenezi zinapangitsanso kuti ana awo azidana.—Genesis 29:16-35; 30:1, 8, 19, 20; 37:35.

Rakele anakhala wosabereka kwa nthawi yaitali koma kenako anabereka Yosefe. Izi zinachititsa kuti Yakobo azikonda kwambiri Yosefeyo popeza anabadwa Yakobo ali wachikulire. Mwachitsanzo, pamene banja la Yakobo linkapita kukakumana ndi Esau, yemwe mwina akanapha banja lonseli, Yakobo anaika Rakele  ndi mwana wake Yosefe kumbuyo kwa gulu lonselo kuti akhale otetezeka. N’kutheka kuti zimenezi zinachititsa kuti Yosefe azidziwa kuti bambo ake amam’konda kwambiri ndipo ankazikumbukirabe. Koma palinso zinthu zina zimene zinachitika pa nthawiyi zimene Yosefe ankazikumbukirabe. M’mawa wa tsikuli, anaona bambo ake akuyenda motsimphina. Iye ayenera kuti anadabwa kwambiri bambo akewo atamuuza kuti alimbana ndi mngelo wamphamvu usiku wonse ndipo zimenezi n’zimene zinapangitsa kuti azitsimphina. Yakobo anachita izi kuti Yehova amudalitse ndipo zotsatira zake Yehova anasintha dzina la Yakoboyo n’kukhala Isiraeli. Izi zinasonyeza kuti padzakhala mtundu umene uzidzadziwika ndi dzinali. (Genesis 32:22-31) Patapita nthawi, Yosefe anadziwa kuti ana a Yakobo ndi amene adzapange mtundu umenewu.

Koma kenako, Yosefe anakumana ndi vuto lalikulu. Mayi ake, omwe ankawakonda kwambiri, anamwalira pobereka Benjamini. Bambo ake a Yosefe anali ndi chisoni kwambiri chifukwa cha imfayi. Yerekezani kuti mukuona Yakobo akutonthoza Yosefe kwinaku akum’pukuta misozi n’kumamuuza mfundo zolimbikitsa zomwe zinatonthozanso Abulahamu pa nthawi imene Sara anamwalira. Abulahamu anali agogo ake a Yakobo. Yosefe ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri atadziwa kuti Yehova adzaukitsa mayi akewo. N’kutheka kuti izi zinapangitsa kuti Yosefe azikonda kwambiri Yehova yemwe ndi “Mulungu wa anthu amoyo.” (Luka 20:38; Aheberi 11:17-19) Imfa ya Rakele, inapangitsa kuti Yakobo ayambe kukonda kwambiri Yosefe ndi Benjamini, ana amene mkazi wakeyu anamubereka.—Genesis 35:18-20; 37:3; 44:27-29.

Ana ena sakula ndi makhalidwe abwino makolo awo akamawakonda kuposa ana ena. Koma si mmene zinalili ndi Yosefe. Iye anaphunzira makhalidwe abwino kuchokera kwa makolo ake, anali ndi chikhulupiriro cholimba komanso ankatha kusiyanitsa zoyenera ndi zosayenera. Mmene ankakwanitsa zaka 17 n’kuti ali m’busa ndipo ankathandizana ndi azichimwene ake kuweta nkhosa za bambo awo. Tsiku lina anaona zinthu zolakwika zimene azichimwene ake ankachita. Yosefe akanatha kungoisunga nkhaniyo n’cholinga choti asadane ndi azichimwene akewo. Koma iye anaona kuti ndi bwino kuti akanene nkhaniyi kwa bambo ake ndipo anakanenadi. (Genesis 37:2) N’kutheka kuti zimenezi zinapangitsa kuti Yakobo azimudalira kwambiri mwana wakeyu. Apatu Yosefe anapereka chitsanzo chabwino kwa Akhristu achinyamata. Sayenera kubisa m’bale wawo kapena mnzawo akachita tchimo. M’malomwake, ayenera kutengera chitsanzo cha Yosefe poulula tchimolo kwa munthu woyenera n’cholinga choti wolakwayo athandizidwe.—Levitiko 5:1.

Tingaphunzirenso zambiri pa zimene zinkachitika m’banja limene Yosefe anakulira. Ngakhale kuti masiku ano Akhristu sakwatira mitala, pali mabanja ambiri omwe muli makolo ndi ana opeza. Zimene mabanja otere angaphunzire kuchokera ku banja la Yakobo ndi zoti, kuchita zinthu mokondera kungapangitse kuti m’banjamo anthu asamagwirizane. Makolo a  m’mabanja oterewa ayenera kuchita zinthu zomwe zingathandize kuti mwana aliyense aziona kuti amakondedwa komanso ndi wofunika m’banjamo.—Aroma 2:11.

ANAYAMBA KUMUCHITIRA NSANJE

Yakobo ankakonda kwambiri Yosefe chifukwa anali wokhulupirika komanso wachilungamo

Nthawi ina Yakobo anasoketsera Yosefe mkanjo wokongola kwambiri. Mwina iye anachita zimenezi chifukwa choti mwana wakeyu ankayesetsa kuchita zinthu zomukondweretsa. (Genesis 37:3) Mkanjowu unali wamanja aatali ndipo unkafika mpaka m’mapazi. Uyenera kuti unali chovala chapamwamba kwambiri chomwe ankavala anthu olemekezeka kapena ana a mafumu.

Yakobo anasoketsera Yosefe mkanjowu pongofuna kusonyeza kuti amamukonda, ndipo Yosefe ayenera kuti anasangalala kwambiri ndi zimenezi. Komabe mkanjowu unabweretsa mavuto ambiri kwa Yosefe. Musaiwale kuti mnyamatayu anali m’busa wa nkhosa. Ntchito imeneyi inali yovuta kwambiri. Yerekezerani kuti mukumuona Yosefe atavala mkanjowu n’kumadutsa m’malo momwe muli udzu wautali, kukwera m’miyala kapenanso kuchotsa kamwana ka nkhosa komwe kakodwa m’ziyangoyango. Komanso mkanjowu unautsa mapiri pachigwa. Kodi mukuganiza kuti azichimwene a Yosefe anamva bwanji ataona kuti abambo awo amusoketsera mkanjo wapamwamba posonyeza kuti amamukonda?

Baibulo limati: “Abale ake ataona kuti bambo awo anali kum’konda kwambiri Yosefe kuposa iwo onse, anayamba kudana naye, moti sankatha kulankhula naye mwamtendere.” * (Genesis 37:4) Ena angaone kuti m’pake kuti azichimwene ake a Yosefe anachita nsanje. Komabe iwo sanachite bwino kulola kuti nsanje imeneyi iwapangitse kuchita zoipa. (Miyambo 14:30; 27:4) Kodi inunso nthawi zina mumachita nsanje munthu wina akamakondedwa kapena akapatsidwa udindo woti inunso mumaufuna? Muzikumbukira zimene azichimwene ake a Yosefe anachita. Chifukwa cha nsanje, iwo anachita zinthu zimene pamapeto pake ananong’oneza nazo bondo. Nkhani yawoyi ndi phunziro kwa Akhristu kuti ndi bwino ‘kusangalala ndi anthu amene akusangalala.’—Aroma 12:15.

Yosefe ayenera kuti ankadziwa kuti azichimwene ake ankam’chitira nsanje. Kodi zimenezi zinachititsa kuti azibisa mkanjo uja azichimwene ake akakhalapo? N’kutheka kuti nthawi zina ankaganiza zoubisa kuti azichimwene ake asauone. Komatu paja Yakobo anamusokera mkanjowu posonyeza kuti amamukonda komanso kumudalira. Yosefe sanafune kukhumudwitsa bambo akewo choncho nthawi zonse ankavala mkanjowo. Tingaphunzire zambiri pa zimene anachitazi. N’zoona kuti Atate wathu wakumwamba alibe tsankho. Komabe nthawi zina amatha kuchitira zinthu zapadera atumiki ake ena okhulupirika. Ndipo amafuna kuti atumiki ake azichita zinthu mosiyana ndi anthu a m’dziko loipali. Chovala chapadera cha Yosefe chinkamupangitsa kuoneka mosiyana ndi azichimwene ake. Akhristunso amakhala osiyana  ndi anthu ena chifukwa cha khalidwe lawo labwino. Nthawi zina zimenezi zimapangitsa kuti anthu ena azidana nawo kapena kuwachitira nsanje. (1 Petulo 4:4) Ndiye kodi ndi bwino kuti Mkhristu azidzibisa kuti asadziwike kuti ndi mtumiki wa Mulungu? Ayi. Ayenera kutengera chitsanzo cha Yosefe.—Luka 11:33.

MALOTO A YOSEFE

Pasanapite nthawi yaitali, Yosefe analota maloto awiri odabwitsa. Maloto oyamba, analota ali ndi azichimwene ake, akumanga mitolo ya tirigu. Kenako mitolo ya azichimwene ake inadzuka n’kuzungulira mtolo wake ndipo inayamba kuuweramira. Maloto achiwiri, analota dzuwa, mwezi komanso nyenyezi 11 zikumugwadira. (Genesis 37:6, 7, 9) Kodi Yosefe anatani atalota maloto odabwitsawa?

Yehova Mulungu ndi amene anamulotetsa malotowa. Anali a ulosi ndipo Mulungu ankafuna kuti Yosefe auze abale ake uthenga wa malotowa. Yosefe ankafunika kuchita zofanana ndi zimene aneneri a Mulungu anachita patapita zaka. Iwo ankauza anthu osamvera, uthenga wochokera kwa Mulungu wonena za chiweruzo komanso zinthu zina.

Yosefe anauza azichimwene ake mwaulemu kuti: “Tamverani maloto amene ine ndinalota.” Yosefe atafotokozera azichimwene ake malotowa, iwo anadziwa tanthauzo lake ndipo zinawanyansa kwambiri. Anamuyankha kuti: “Kodi iweyo ndithu ukuganiza kuti ungadzakhale mfumu yathu? Moti ukuona kuti ungadzatilamulire ife?” Nkhaniyi imapitiriza kuti: “Maloto amenewa ndi mawu akewa anakhala chifukwa chinanso chomudera.” Yosefe atauza bambo ake komanso azichimwene ake maloto achiwiri aja, zinthu zinangoipiraipira. Baibulo limati: “Bambo ake anam’dzudzula kuti: ‘Kodi maloto walotawa akutanthauza chiyani? Kodi ineyo ndithu ndi mayi akowa, komanso abale akowa tidzagwada pansi pamaso pa iwe?’” Komabe Yakobo ankaganizirabe malotowa ndipo anaona kuti mwina Yehova ndi amene wamulotetsa.—Genesis 37:6, 8, 10, 11.

Yosefe sanali mtumiki wa Yehova woyamba kapena womaliza kuuzidwa ndi Yehova kuti anene uthenga wosasangalatsa kwa anthu komanso umene ungachititse kuti azunzidwe. Nayenso Yesu nthawi zina ankalengeza uthenga umene unkakwiyitsa anthu. Ndipo anauza ophunzira ake kuti: “Ngati anazunza ine, inunso adzakuzunzani.” (Yohane 15:20) Akhristu onse, ana ndi akulu omwe, angaphunzire zambiri pa chikhulupiriro komanso kulimba mtima kwa Yosefe.

CHIDANI CHINAFIKA POSAUZANA

Pasanapite nthawi kuchokera pamene Yosefe ananena maloto ake, Yakobo anamutuma kuti apite komwe azichimwene ake ankadyetsa nkhosa. Iwo ankadyetsa nkhosazo chakumpoto, kufupi ndi Sekemu. Kumeneku kunali adani awo chifukwa anali atakangana ndi anthu a kuderali. Monga kholo, Yakobo ankadera nkhawa ana akewa n’chifukwa chake anatuma Yosefe kuti akaone ngati ali bwino. Kodi mukuganiza kuti Yosefe anamva bwanji? Iye ankadziwa kuti azichimwene akewo ankadana naye kwambiri. Kodi azichimwene ake akatani akakaona kuti bambo ake amutuma iyeyo? Komabe Yosefe anamvera bambo ake, ndipo anapita.—Genesis 34:25-30; 37:12-14.

Komatu ulendowu unali wautali chifukwa ankafunika kuyenda wapansi masiku 4 kapena 5. Dera la Sekemu linali pa mtunda wamakilomita 80 kuchokera ku Heburoni. Koma Yosefe atafika ku Sekemu, anamva kuti azichimwene akewo apita ku Dotani, womwe unali mtunda wa makilomita enanso oposa 22. Choncho Yosefe anauyambanso ulendo wopita ku Dotani ndipo atafika, azichimwene akewo anamuonera patali. Nthawi yomweyo mkwiyo unayamba kuyaka mumtima mwawo. Nkhaniyi imati: “Anauzana kuti: ‘Tamuonani wolota uja. Uyo akubwera apoyo! Tiyeni timuphe, timuponye m’chitsime chopanda madzi, ndipo tikanene kuti chilombo cholusa chamudya. Tidzaone kuti chidzachitike n’chiyani ndi maloto ake aja.’” Komabe Rubeni ananyengerera azibale akewo kuti asamuphe koma amuponyere m’chitsime chopanda madzi. Iye anachita zimenezi n’cholinga choti nthawi ina amutulutsemo.—Genesis 37:19-22.

Yosefe sanadziwe kuti azichimwene akewo amukonzera chiwembu, moti ankaganiza kuti asangalala kumuona ndipo amulandira ndi manja awiri. Koma atangofika, azichimwene akewo anamugwira, kumung’ambira mkanjo wake uja, ndipo anamududuluza n’kukamuponyera m’chitsime chopanda madzi. Yosefe anayesetsa kuti atuluke m’chitsimemo koma analephera. Akayang’ana kumwamba ankangoona mitambo ndipo mawu a azichimwene ake aja ankamvekera chapatali kusonyeza kuti akupita. Yosefe anayesetsa kukuwa kuwapempha kuti adzamutulutse, koma iwo sanabwerere. Kenako azichimwene  akewa anapita pamalo ena ndipo anayamba kudya chakudya, osada nkhawa ngakhale pang’ono za mng’ono wawoyo. Rubeni atachoka, anyamatawa anayambanso kuganiza zopha Yosefe, koma Yuda anawanyengerera kuti asamuphe, m’malomwake angomugulitsa kwa amalonda. Dera la Dotani linali pafupi ndi msewu wopita ku Iguputo womwe amalonda ankadutsa. Pasanapite nthawi, panadutsadi gulu la anthu amalonda ndipo anali Aisimaeli ndi Amidiyani. Azichimwene a Yosefe anamugulitsa kwa anthuwa moti pamene Rubeni ankabwera, anapeza atamugulitsa kale. Anamugulitsa ngati kapolo pa mtengo wa ndalama zasiliva 20. *Genesis 37:23-28; 42:21.

Yosefe ankayesetsa kuchita zinthu zoyenera, koma azichimwene ake ankadana naye

Zimene tafotokoza kumayambiriro kwa nkhani ino zija, zinachitika pa nthawi imeneyi. Amalondawa anatenga Yosefe n’kumapita naye ku Iguputo ndipo Yosefeyo ankangoona kuti zake zada. Anali atasiyana ndi anthu onse a m’banja lake. Sanadziwe kuti Rubeni anatani atamva kuti azichimwene ake ena aja anamugulitsa. Sanadziwenso zimene bambo ake anachita atanamizidwa kuti iye wafa. Yosefe sanamvenso chilichonse chokhudza agogo ake, a Isaki, omwe pa nthawiyi anali adakali moyo. Komanso kwa nthawi yaitali sankadziwa kuti mng’ono wake Benjamini, yemwe ankamukonda kwambiri, zinthu zinkamuyendera bwanji. Komatu pali chinthu chinachake chimene chinathandiza kwambiri Yosefe.—Genesis 37:29-35.

Yosefe anali ndi chikhulupiriro cholimba, chomwe azichimwene ake sakanatha kumulanda. Iye ankadziwa zambiri zokhudza Yehova Mulungu ndipo zinthu monga kusiyana ndi bambo ake, mavuto amene anakumana nawo pa ulendo wopita ku Iguputo komanso kugulitsidwa ngati kapolo, sizinamuchititse kuti asiye kudziwa zimenezi. (Genesis 37:36) Mavuto onsewa anangothandiza Yosefe kuti azikhulupirira komanso kukonda kwambiri Yehova. M’nkhani zina zokhudza Yosefe zimene zidzatuluke m’tsogolomu, tidzaona mmene chikhulupiriro chake chinamuthandizira kuti Mulungu athe kumugwiritsa ntchito. Tidzaonanso mmene chikhulupirirochi chinamuthandizira kuti athandize anthu a m’banja lake pa nthawi ya mavuto. Tonsefe tingachite bwino kutsanzira chikhulupiriro cha Yosefe.

^ ndime 15 Akatswiri ena amati azichimwene ake a Yosefe anaona kuti bambo awo anapatsa Yosefe mkanjo chifukwa ankafuna kuti Yosefeyo adzatenge madalitso amene ankaperekedwa kwa mwana woyamba kubadwa. Ankadziwanso kuti Yosefe anali mwana woyamba wa Rakele, mkazi amene Yakobo ankamukonda kwambiri. Komanso Rubeni, mwana woyamba wa Yakobo, anali atagona ndi Biliha, mkazi wamng’ono wa bambo ake. Uku kunali kunyoza bambo akewo komanso kupeputsa udindo wake monga mwana woyamba.—Genesis 35:22; 49:3, 4.

^ ndime 25 Pa nkhani imeneyinso, Baibulo limasonyeza kuti ndi lolondola. Zolemba za m’nthawi imeneyi zimasonyeza kuti ku Iguputo mtengo wovomerezeka wogulitsira kapolo unali ndalama 20 zasiliva.