Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE OWERENGA AMAFUNSA . . .

Kodi Ndani Analenga Mulungu?

Kodi Ndani Analenga Mulungu?

Tiyerekeze kuti bambo akucheza ndi mwana wake wamwamuna wazaka 7. Bamboyo akuuza mwana wakeyo kuti: “Kale kwambiri, Mulungu anapanga dziko lapansi ndi zinthu zonse zimene zili padzikoli. Anapanganso dzuwa, mwezi komanso nyenyezi.” Mwanayo akuganizira zimene bambo akewo amuuza, kenako akuwafunsa kuti, “Adadi, ndiye Mulunguyo anam’panga ndani?”

Ndiyeno bamboyo akuyankha kuti: “Palibe anapanga Mulungu. Iye anakhalapo kuyambira kalekale.” Mwanayu akuona kuti yankho limeneli ndi lomveka. Komabe, pamene akukula, funsoli likuyambiranso kumuzunguza maganizo. Zikumuvutabe kumvetsa kuti pali winawake amene sanachite kulengedwa. Iye akuona kuti ngakhale zinthu zakumwamba zili ndi chiyambi. Zimenezi zikumupangitsa kudzifunsa kuti: ‘Ndiye Mulungu anachokera kuti?’

Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhaniyi? Limanena zofanana ndi zimene bamboyu anauza mwana wake m’chitsanzochi. Mose analemba kuti: “Inu Yehova, . . . mapiri asanabadwe, kapena musanakhazikitse dziko lapansi ndi malo okhalapo anthu, inu ndinu Mulungu kuyambira kalekale mpaka kalekale.” (Salimo 90:1, 2) Nayenso mneneri Yesaya ananena kuti: “Kodi iwe sukudziwa kapena kodi sunamve? Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi,ndiye mulungu mpaka kalekale.” (Yesaya 40:28) Komanso lemba la Yuda 25 limati Mulungu wakhala alipo “kuchokera kalekale.”

Malemba amenewa akusonyeza kuti Mulungu ndi “Mfumu yamuyaya.” (1 Timoteyo 1:17) Zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu alibe chiyambi, ndipo ngakhale titati tifufuze, sitingapeze kuti anayambira apa. Komanso iye adzakhalapo mpaka kalekale. (Chivumbulutso 1:8) Choncho, zimenezi zimam’pangitsa kuti akhale Wamphamvuyonse.

N’chifukwa chiyani mfundo imeneyi imativuta kumvetsa? Chifukwa choti timakhala ndi moyo kwa nthawi yochepa. Zimenezi zimapangitsa kuti tiziona nthawi mosiyana ndi mmene Mulungu amaionera. Popeza Mulungu ndi wamuyaya, zaka 1,000 zili ngati tsiku limodzi kwa iye. (2 Petulo 3:8) Mwachitsanzo, ziwala zimakhala ndi moyo kwa masiku 50 okha. Ndiye kodi ziwala zingamvetse kutalika kwa zaka 70 kapena 80, zimene anthufe timakhala ndi moyo? N’zosatheka. Ndiyetu Baibulo limanena kuti anthufe tili ngati ziwala poyerekeza ndi Mlengi wathu. Ngakhale kaganizidwe kathu n’kochepa kwambiri poyerekeza ndi ka Mulungu. (Yesaya 40:22; 55:8, 9) Choncho, n’zosadabwitsa kuti pali zinthu zina zokhudza Yehova zimene sitingazimvetse bwinobwino.

Ngakhale kuti mfundo yakuti Mulungu alibe chiyambi ndi yovuta kumvetsa, tikaganizira zimene Baibulo limanena zokhudza nkhaniyi, tikhoza kuona kuti ndi zoona. Ngati pali winawake amene analenga Mulungu, ndiye kuti munthu ameneyo ndi Mlengi. Komatu Baibulo limanena kuti Yehova ndi amene ‘analenga zinthu zonse.’ (Chivumbulutso 4:11) Izi zikusonyeza kuti nthawi inayake zinthuzi kunalibe. (Genesis 1:1, 2) Ndiye kodi zinachokera kuti? Mosakayikira amene anazilenga, anafunika kukhalapo izozo zisanakhalepo. Mulungu analipo kale asanalenge Mwana wake komanso angelo. (Yobu 38:4, 7; Akolose 1:15) Apa n’zoonekeratu kuti poyamba Mulungu analipo yekha. Iye sanachite kulengedwa chifukwa pa nthawiyi, panalibe aliyense amene akanamulenga.

Anthufe ndiponso chilengedwe chonsechi, ndi umboni woti kuli Mulungu. Komanso popeza zinthu za m’chilengedwechi nthawi zonse zimayenda motsatira malamulo, ndi umboni wakuti Mulungu amene anazilenga, wakhala alipo kwa nthawi zonse.—Yobu 33:4.