Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MULUNGU AMAKUONANI KUTI NDINU WOFUNIKA?

Mulungu Angakulimbikitseni ndi Kukuthandizani

Mulungu Angakulimbikitseni ndi Kukuthandizani

“Mulungu, amene amalimbikitsa osautsika mtima, anatilimbikitsa.” —2 AKORINTO 7:6.

“Mwana wa Mulungu . . . anandikonda ndi kudzipereka yekha chifukwa cha ine.” —AGALATIYA 2:20

N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHU ENA AMAKAYIKIRA? Anthu ena akakhala pa mavuto amaganiza kuti n’kudzikonda kupempha Mulungu kuti awathandize. Iwo amachita zimenezi ngakhale atasoweratu mtengo wogwira. Mwachitsanzo, mayi wina dzina lake Raquel, ananena kuti: “Ndikaganizira mavuto amene anthu ambiri padzikoli akukumana nawo, ndimaona kuti mavuto anga ndi ochepa kwambiri moti palibe chifukwa choti ndizipempha Mulungu kuti andithandize.”

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: Mulungu anapereka Mwana wake pofuna kutithandiza. Anthufe timabadwa ochimwa, ndipo zimenezi zimachititsa kuti tisamathe kuchita zonse zimene Mulungu amafuna popanda kulakwitsa. Komabe Mulungu “anatikonda ndi kutumiza Mwana wake [Yesu Khristu] monga nsembe yophimba machimo athu.” (1 Yohane 4:10) Kudzera mu nsembe ya Yesu, Mulungu amatikhululukira machimo, timakhala ndi chikumbumtima chabwino komanso timakhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha m’dziko latsopano lamtendere. * Komatu sikuti nsembe imeneyi imangosonyeza kuti Mulungu amakonda anthu onse monga gulu. Imasonyezanso kuti Mulungu amakukondani inuyo panokha.

Taganizirani zimene mtumwi Paulo ananena. Iye ankayamikira kwambiri nsembe ya Yesu moti analemba kuti: “Ndikukhala mokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene anandikonda ndi kudzipereka yekha chifukwa cha ine.” (Agalatiya 2:20) Ngakhale kuti Yesu anafa Paulo asanakhale Mkhristu, iye ankaona kuti nsembe ya Yesu ndi mphatso imene Mulungu anamupatsa iyeyo.

Inunso muziona kuti nsembe ya Yesu ndi mphatso imene Mulungu anakupatsani inuyo panokha. Mphatso imeneyi imasonyeza kuti Mulungu amakuonani kuti ndinu wofunika. Ingakupatseninso “chiyembekezo chabwino” ndipo zimenezi zingakuthandizeni kuti muzichita zinthu zabwino.—2 Atesalonika 2:16, 17.

Komatu Yesu anapereka nsembe moyo wake zaka pafupifupi 2,000 zapitazo. Ndiye kodi masiku ano pali umboni uliwonse wosonyeza kuti Mulungu akufuna kuti mukhale naye pa ubwenzi?

^ ndime 5 Kuti mudziwe zambiri zokhudza nsembe ya Yesu, werengani mutu 5 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.