Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MULUNGU AMAKUONANI KUTI NDINU WOFUNIKA?

Mulungu Amaona Zomwe Zikuchitika pa Moyo Wanu

Mulungu Amaona Zomwe Zikuchitika pa Moyo Wanu

“Pakuti maso ake amayang’anitsitsa njira za munthu, ndipo amaona mayendedwe ake onse.”—YOBU 34:21.

Mwana wamng’ono amafunika chisamaliro chapadera

N’CHIFUKWA CHIYANI ENA AMAKAYIKIRA? Zotsatira za kafukufuku amene anachitika posachedwapa zinasonyeza kuti mlalang’amba wathu wokhawu uli ndi mapulaneti okwana 100 biliyoni. Poganizira zimenezi ndiponso kukula kwa chilengedwe chonse, anthu ambiri amafunsa kuti, ‘Zingatheke bwanji kuti Mlengi wachilengedwe chonsechi azichita chidwi ndi anthu okhala padzikoli n’kumadziwa zomwe zikuchitika pa moyo wawo?’

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: Sikuti Mulungu anangotipatsa Baibulo n’kutisiya. M’malomwake Yehova amatitsimikizira kuti: “Ndidzakupatsa malangizo ndi kukuyang’anira.”—Salimo 32:8.

Taganizirani zimene zinachitikira Hagara, mayi wa ku Iguputo yemwe anakhalako m’zaka za m’ma 1900 B.C.E. Hagara anali wantchito wa Sarai ndipo atayamba kuchita mwano Sarai anayamba kumuzunza. Zitatere Hagarayo anathawira m’chipululu. Kodi Mulungu anamutaya Hagara chifukwa choti anachitira mwano Sarai? Ayi, chifukwa Baibulo limati: “Mngelo wa Yehova anakapeza Hagara m’chipululu.” Mngeloyo anauza Hagara kuti: “Yehova wamva kulira kwako.” Kenako Hagara anauza Yehova kuti: “Inu ndinu Mulungu amene amaona chilichonse.”—Genesis 16:4-13.

Dziwani kuti “Mulungu amene amaona chilichonse,” amaonanso zimene zikuchitika pa moyo wanu ndipo amakuderani nkhawa. Kuti timvetse mfundo imeneyi, tiyeni tiyerekeze ndi zimene mayi wachikondi amachita. Iye amaonetsetsa zimene zikuchitikira ana ake, makamaka aang’ono, chifukwa amadziwa kuti mwana wamng’ono amafunika chisamaliro chapadera. Mofanana ndi zimenezi, Mulungu amaonetsetsa zimene zikutichitikira, makamaka tikhala pa mavuto. Yehova ananena kuti: “Ndimakhala kumwamba pamalo oyera. Ndimakhalanso ndi munthu wopsinjika ndi wa mtima wodzichepetsa, kuti nditsitsimutse mtima wa anthu onyozeka ndiponso kuti nditsitsimutse mtima wa anthu opsinjika.” —Yesaya 57:15.

Komabe mwina mungafunse kuti: ‘Kodi Mulungu amaona chiyani mwa ine? Kodi amandiweruza pongotengera maonekedwe anga, kapena amaona zimene zili mumtima mwanga ndipo amandimvetsa?’