Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MULUNGU AMAKUONANI KUTI NDINU WOFUNIKA?

Mulungu Akufuna Kuti Mukhale Naye pa Ubwenzi

Mulungu Akufuna Kuti Mukhale Naye pa Ubwenzi

“Palibe munthu angabwere kwa ine akapanda kukokedwa ndi Atate.” —YOHANE 6:44.

N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHU ENA AMAKAYIKIRA? Pali anthu ambiri amene amakhulupirira kuti kuli Mulungu, koma amaona kuti sali naye pa ubwenzi. Mwachitsanzo, mayi wina wa ku Ireland dzina lake Christina, ananena kuti: “Ndinkadziwa kuti Mulungu ndi amene analenga chilichonse. Komabe sindinkamudziwa bwinobwino komanso ndinkaona kuti iye si bwenzi langa lapamtima.”

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: Tikalakwa, Yehova satopa nafe ndipo amapitirizabe kutithandiza kuti tikhale naye pa ubwenzi. Yesu anapereka fanizo losonyeza mmene Mulungu amachitira zimenezi. Iye anati: “Ngati munthu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi mwa nkhosazo n’kusochera, kodi sangasiye nkhosa 99 zija m’phiri ndi kupita kukafunafuna yosocherayo? . . . Mofanana ndi zimenezi, Atate wanga wakumwamba sakufuna kuti mmodzi wa tianati akawonongeke.”—Mateyu 18:12-14.

Zimenezi zikutiphunzitsa kuti Mulungu amaona kuti munthu aliyense ndi wofunika. Ndiye kodi Mulungu ‘amafunafuna’ bwanji anthu amene ali ngati nkhosa zosochera? Lemba la Yohane 6:44 limanena kuti Yehova amakokera anthuwa kwa iye.

Kodi ndani masiku ano amene amapita kunyumba za anthu kapena m’malo osiyanasiyana n’kumauza anthu uthenga wa m’Baibulo wonena za Mulungu?

Tiyeni tione mmene Mulungu anachitira zimenezi m’mbuyomu. M’nthawi ya atumwi, Mulungu anatumiza Filipo, yemwe anali wophunzira wa Yesu, kukakumana ndi nduna ya ku Itiyopiya kuti akakambirane nayo tanthauzo la zimene ndunayi inkawerenga m’Malemba. (Machitidwe 8:26-39) Pa nthawi ina Mulungu anachititsa kuti mtumwi Petulo apite kunyumba kwa kapitawo wa gulu la asilikali a Roma, dzina lake Koneliyo, yemwe ankapemphera komanso kuyesetsa kulambira Mulungu. (Machitidwe 10:1-48) Pa nthawi inanso Mulungu anatsogolera mtumwi Paulo ndi anzake kuti apite m’mbali mwa mtsinje womwe unali kunja kwa mzinda wa Filipi. Kumeneko anapeza mayi wina dzina lake Lidiya, yemwe anali “wolambira Mulungu,” ndipo Mulungu “anatsegula kwambiri mtima wake kuti atchere khutu ku zimene Paulo anali kunena.”—Machitidwe 16:9-15.

Zitsanzo za anthu onsewa zikusonyeza kuti Yehova anaonetsetsa kuti anthu amene ankafunitsitsa kumudziwa, apeze mwayi wophunzira za iye. Kodi ndani masiku ano amene amapita kunyumba za anthu kapena m’malo osiyanasiyana n’kumauza anthu uthenga wa m’Baibulo wonena za Mulungu? Ambiri angayankhe kuti, “Ndi a Mboni za Yehova.” Ndiye dzifunseni kuti, ‘Kodi n’kutheka kuti Mulungu akugwiritsa ntchito anthu amenewa pofuna kundikokera kwa iye?’ Tikukulimbikitsani kuti mupemphere kwa Mulungu kuti akuthandizeni kuzindikira njira imene akugwiritsa ntchito kuti akukokereni kwa iye. *

^ ndime 8 Kuti mudziwe zambiri, onerani vidiyo yakuti, N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? pa webusaiti yathu ya www.jw.org/ny.