Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MULUNGU AMAKUONANI KUTI NDINU WOFUNIKA?

Kodi Mulungu Amakuganizirani?

Kodi Mulungu Amakuganizirani?

“Koma ine ndasautsika ndipo ndasauka. Yehova amandiwerengera.” *DAVIDE YEMWE ANKAKHALA KU ISIRAELI, M’ZAKA ZA M’MA 1000 B.C.E.

“Mitundu ya anthu ili ngati dontho la madzi lochokera mumtsuko.”—YESAYA 40:15

Kodi Davide ankanena zoona kuti Mulungu ankamuwerengera kapena kuti kumuganizira? Kodi inuyo mumaona kuti Mulungu amakuganizirani? Anthu ambiri zimawavuta kukhulupirira kuti Mulungu Wamphamvuyonse angamawaganizire. N’chifukwa chiyani?

Chifukwa amadziwa mfundo yoti Mulungu ndi wapamwamba kwambiri kuposa anthufe. Mulungu akakhala kumwamba n’kumayang’ana anthu padzikoli, amaona kuti mitundu yonse ya anthu “ili ngati dontho la madzi lochokera mumtsuko, ndipo kwa iye ili ngati fumbi pasikelo.” (Yesaya 40:15) Poganizira mfundo imeneyi munthu wina wolemba mbiri yakale ananena kuti: “Munthu amene amaganiza kuti Mulungu, yemwe ndi wapamwamba kwambiri, angamachite chidwi ndi zochita za iyeyo ndi wodzikuza kwambiri.”

Palinso anthu ena amene amaganiza kuti zochita zawo zimachititsa kuti Mulungu aziwaona kuti ndi osafunika. Mwachitsanzo, bambo wina dzina lake Jim, ananena kuti: “Nthawi zambiri ndinkapemphera kwa Mulungu kuti andithandize kuti ndiziugwira mtima komanso ndizikhala mwamtendere ndi anthu. Koma pakangopita nthawi ndinkayambiranso kupsa mtima. Zimenezi zinandipangitsa kuganiza kuti ndine wokanika ndipo Mulungu sangandithandize.”

Popeza Mulungu ndi wapamwamba kwambiri, kodi ndiye kuti sachita chidwi ndi anthu? Nanga kodi iye amamva bwanji anthu akamalephera kuchita bwino zinthu chifukwa choti si angwiro? Palibe munthu amene angathe kudziwa mayankho a mafunso amenewa popanda kuthandizidwa ndi Mulungu. Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu, limatitsimikizira kuti ngakhale kuti Mulungu ndi wapamwamba kwambiri, amachita chidwi ndi zimene zikuchitikira munthu aliyense payekha. Ndipotu Baibulo limati: “Iye sali kutali ndi aliyense wa ife.” (Machitidwe 17:27) M’nkhani zotsatirazi, tiona zimene Mulungu amatiuza zosonyeza kuti amachita chidwi ndi munthu aliyense payekha. Tionanso mmene anachitira zimenezi kwa anthu ena, zomwe zikusonyeza kuti amachitanso chidwi ndi inuyo.

^ ndime 3 Mawuwa achokera pa Salimo 40:17. Yehova ndi dzina la Mulungu.