Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi ndi ndani kwenikweni amene akulamulira dziko lapansili?

Zikanakhala kuti Mulungu ndiye akulamulira dziko, kodi bwenzi padzikoli pali mavuto ambiri chonchi?

Anthu ambiri amakhulupirira kuti Mulungu ndi amene akulamulira dziko lapansili. Ngati ndi choncho, n’chifukwa chiyani padzikoli pali mavuto ambiri chonchi? (Deuteronomo 32:4, 5) Baibulo limanena kuti dzikoli lili m’manja mwa winawake yemwe ndi woipa.—Werengani 1 Yohane 5:19.

Kodi zinatheka bwanji kuti woipayu azilamulira dzikoli? Anthu atangolengedwa, mngelo wina anapandukira Mulungu ndipo ananyengereranso mwamuna ndi mkazi oyamba kuti nawonso apandukire Mulungu. (Genesis 3:1-6) Anthu oyambirirawa anamvera Satana, zimene zinachititsa kuti akhale wolamulira wawo. Mulungu Wamphamvuyonse ndiye woyenera kulamulira. Komabe iye amafuna kuti anthu azisankha okha kulamulidwa ndi iyeyo chifukwa choti amamukonda. (Deuteronomo 6:6; 30:16, 19) Koma n’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri amapusitsidwanso ngati mmene anthu oyambirira anachitira, potsatira zimene Satana ananena.—Werengani Chivumbulutso 12:9.

Kodi ndani adzathetse mavuto a anthu?

Kodi Mulungu alola kuti Satana azilamulirabe dzikoli mpaka kalekale? Ayi. Mulungu adzagwiritsa ntchito Yesu kuchotsa zoipa zonse zimene Satana akubweretsa padzikoli.—Werengani 1 Yohane 3:8.

Yesu adzawononga Satana pogwiritsa ntchito mphamvu zimene Mulungu anamupatsa. (Aroma 16:20) Kenako, Mulungu adzayambanso kulamulira dziko lonse n’kupangitsa kuti anthu azikhala mwamtendere komanso mosangalala ngati mmene ankafunira poyamba.—Werengani Chivumbulutso 21:3-5.