Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Pali Amene Angadziwiretu za M’tsogolo?

Kodi Pali Amene Angadziwiretu za M’tsogolo?

Tonsefe timafuna kudziwa zomwe zidzachitike m’tsogolo. Timafuna kudziwa kuti zinthu zidzakhala bwanji kwa ifeyo, anzathu komanso anthu a m’banja lathu. Timadzifunsa kuti: ‘Kodi ana anga adzakhala ndi moyo wabwino? Kodi dzikoli lidzawonongedwa ndi masoka achilengedwe? Kodi pali zimene ndingachite kuti ndikhale ndi tsogolo labwino?’ Kukhala ndi maganizo amenewa n’kwachibadwa, chifukwa anthufe timalakalaka moyo wabwino komanso wotetezeka. Mutakhala kuti mukudziwiratu zomwe zidzachitike m’tsogolo, ndipo mukukhulupirira kuti zimenezo zidzachitikadi, zingakuthandizeni kudziwa zoyenera kuchita.

Ndiye kodi tsogolo lanu ndi lotani? Kodi pali aliyense amene angalidziwe? Anthu ena ayesetsa kuneneratu za m’tsogolo, koma nthawi zambiri zomwe amanena sizichitikadi. Koma Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu, limanena kuti Mulungu angathe kuneneratu molondola zinthu zomwe zidzachitike m’tsogolo. Limati: “Ndimanena za mapeto kuyambira pa chiyambi. Kuyambira kalekale, ndimanena za zinthu zimene sizinachitike.” (Yesaya 46:10) Kodi n’zoona kuti zonse zimene Mulungu wanena zimachitikadi?

KODI ZONSE ZIMENE MULUNGU AMANENA ZIMACHITIKADI?

N’chifukwa chiyani muyenera kudziwa ngati zimene Mulungu walosera zimachitikadi kapena ayi? Ngati pali munthu wina wazanyengo yemwe zimene wanena zimachitikadi, n’zosakayikitsa kuti mungayambe kumukhulupirira. Munthu wotereyu atanena zokhudza mmene nyengo idzakhalire mawa, simungakayikire. N’chimodzimodzinso ndi Mulungu. Mutadziwa kuti zonse zimene wakhala akulosera zimachitika ndendende, simungakayikirenso kuti zomwe walosera zokhudza m’tsogolo, zidzachitikadi. Taonani zitsanzo zotsatirazi.

Khoma lomwe linamangidwanso pamabwinja a mzinda wakale wa Nineve

KUWONONGEDWA KWA MZINDA WA NINEVE:

Munthu wina atalosera kutatsala zaka zambiri, kuti mzinda winawake wamphamvu udzawonongedwa, mzindawo n’kuwonongedwadi, mwina mungamutayire kamtengo. Zangati zimenezi n’zimene Mulungu anachita. Kudzera mwa  mneneri wake wina, analosera kuti mzinda wa Nineve udzawonongedwa. (Zefaniya 2:13-15) Kodi akatswiri a mbiri yakale amati bwanji pa nkhaniyi? M’zaka za m’ma 600 B.C.E., patadutsa zaka 15 kuchokera pamene Mulungu analosera za kuwonongedwa kwa mzinda wa Nineve, Ababulo ndi Amedi anaukira mzindawu, n’kuuwononga. Mulungu anatchulanso kuti mzinda wa Nineve udzakhala ‘bwinja, n’kukhala dziko lopanda madzi ngati chipululu.’ Kodi zimenezi zinachitikadi? Inde. Ngakhale kuti mzindawu unali waukulu komanso unali ndi matauni ambiri, anthu amene anaulanda, anangouwononga ndipo sunakhalidwenso ndi anthu. Kodi pali katswiri aliyense wandale amene anganeneretu zinthu molondola chonchi?

KUWOTCHEDWA KWA MAFUPA A ANTHU:

Ndani angathe kuneneratu zinthu zimene zingachitike patatha zaka 300? Mwachitsanzo kutchuliratu kuti munthu winawake adzawotcha mafupa a anthu paguwa lansembe. N’kutchulanso dzina la munthuyo, agogo ake komanso tauni imene zimenezi zidzachitikire. Zimene munthu ameneyu wanena zitachitikadi, zingapangitse kuti atchuke kwambiri. Komatu zimenezi n’zimene Mulungu anachita. Mneneri wake analosera kuti: “Mwana wamwamuna adzabadwa m’nyumba ya Davide, dzina lake Yosiya” ndipo ananenanso kuti “iye adzawotcha mafupa a anthu” paguwa la nsembe m’tauni ya Beteli. (1 Mafumu 13:1, 2) Patatha zaka 300, munthu wina dzina lake Yosiya, anakhala mfumu ndipo anali wochokera kubanja la Davide. Dzina loti Yosiya silinali lofala pakati pa Aisiraeli. Zimene Mulungu analoserazi zinachitikadi ndendende, moti Yosiya ‘anatumiza anthu kuti akatenge mafupa m’manda, ndipo anawatentha paguwa lansembe.’ (2 Mafumu 23:14-16) Kodi pali amene angathe kulosera zinthu ngati zimenezi popanda kutsogoleredwa ndi Mulungu?

Ulosi wa m’Baibulo unaneneratu za kuwonongedwa kwa Babulo ndipo zonse zinakwaniritsidwa ndendende

KUTHA KWA UFUMU WA BABULO:

Zingakhale zodabwitsa kwambiri munthu wina atalosera molondola zoti kudzabadwa munthu wina kutsogolo, komanso kutchuliratu dzina lake. N’kuneneratu kuti munthuyo adzasonkhanitsa asilikali n’kugonjetsa ufumu wamphamvu kwambiri n’kutchuliratunso njira yachilendo imene adzagwiritse ntchito polanda ufumuwo. Komatu zimenezi n’zimene Mulungu anachita. Iye analosera kuti munthu wina dzina lake Koresi adzasonkhanitsa asilikali kuti alande ufumu wa Babulo. Mulungu analoseranso kuti Koresi adzamasula Ayuda, omwe anali akapolo ku Babuloko, ndipo adzathandiza pa ntchito yomanga kachisi wawo woyera. Kuwonjezera pamenepo, analoseranso kuti njira yomwe Koresi adzagwiritse ntchito idzaphatikizapo kuphwetsa mitsinje komanso kuti mageti adzakhala osatseka zimene  zidzachititse kuti asilikali alandedi mzindawo. (Yesaya 44:27–45:2) Kodi zonse zimene Mulungu analosera mu ulosiwu zinakwaniritsidwadi? Akatswiri a mbiri yakale amavomereza kuti Koresi analandadi mzindawu. Koresi ndi asilikali ake anapatutsa mtsinje wina wa ku Babulo ndipo zimenezi zinachititsa kuti mitsinje inanso isakhale ndi madzi ambiri. Komanso asilikali a Koresi analowa mumzindawo kudzera pamageti omwe anasiyidwa osatseka. Kenako Koresi anamasula Ayuda n’kuwalola kuti apite kwawo, akamange kachisi wa ku Yerusalemu. Zimenezi zinali zachilendo kwambiri, chifukwa Koresi sankalambira Mulungu wa Ayuda. (Ezara 1:1-3) Mulungu yekha ndi amene angalosere mwatsatanetsatane zinthu ngati zimenezi.

Tangotchula zitsanzo zitatu zokha zosonyeza kuti Mulungu akalosera, zinthuzo zimachitikadi. Koma pali zitsanzo zambiri zosonyeza mfundo imeneyi. Yoswa, yemwe anali mtsogoleri wa Ayuda ananena mfundo yomwenso Ayudawo ankaidziwa bwino, yakuti: “Inu mukudziwa bwino ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kuti pamawu onse abwino amene Yehova Mulungu wanu ananena kwa inu, palibe ngakhale amodzi omwe sanakwaniritsidwe. Onse akwaniritsidwa kwa inu. Palibe ngakhale mawu amodzi omwe sanakwaniritsidwe.” (Yoswa 23:1, 2, 14) Ayuda ankadziwa bwino kuti zonse zimene Mulungu walosera zimachitikadi. Koma kodi Mulungu amakwanitsa bwanji kuchita zimenezi? Chifukwa choti iye ndi wosiyana kwambiri ndi anthu. N’zofunika kuti mudziwe zomwe zimachititsa kuti Mulungu azikwaniritsa zimene wanena. Tikutero chifukwa pali zinthu zambiri zimene walosera zomwe zidzachitike m’tsogolo, ndipo zimenezi zikukhudzanso inuyo.

KUSIYANA KWA MAULOSI OCHOKERA KWA MULUNGU NDI A ANTHU

Zimene anthu amalosera zimakhala zongochokera pa mfundo za asayansi, zimene ena apeza, zimene owombeza amanena komanso pongotengera zomwe zimachitika kawirikawiri. Anthu akalosera, amangokhala n’kumadikira kuti zimene aloserazo zikwaniritsidwa bwanji.—Miyambo 27:1.

Koma Mulungu ndi wosiyana ndi anthu chifukwa iye amadziwa mfundo zonse. Amadziwa bwino mmene anthufe tilili choncho akafuna, amadziwiratu ndendende zimene munthu wina kapena mtundu wina wa anthu udzachite. Komansotu Mulungu angathe kuchita zoposa pamenepa. Akhoza kusintha zinthu zina, ngakhale zimene anthu anazolowera kuti zimachitika nthawi zonse, n’cholinga choti zimene walosera zichitikedi. Iye anati: “Mawu otuluka pakamwa panga sadzabwerera kwa ine popanda kukwaniritsa cholinga chake, koma adzachitadi zimene ine ndikufuna.” (Yesaya 55:11) Choncho tingati zinthu zina zimene Yehova amalosera zimakhala zoti akungotiuza zimene adzachite m’tsogolo, ndipo amaonetsetsa kuti zinthuzo, zachitikadi.

DZIWANI ZA TSOGOLO LANU

Kodi pali zilizonse zimene zinanenedweratu kuti zidzachitika m’tsogolo zomwe zikukhudza moyo wanu, wa anthu a m’banja lanu ndiponso wa anzanu? Mutakhala kuti mwadziwiratu kuti kukubwera chimphepo chamkuntho, n’zosakayikitsa kuti mungachite zomwe zingakuthandizeni kuti mupulumuke. Muyenera kuchitanso chimodzimodzi ndi maulosi a m’Baibulo. Mulungu waneneratu kuti posachedwapa zinthu padzikoli zisintha kwambiri. (Onani bokosi lakuti:  “Zomwe Mulungu Waneneratu Zokhudza Zimene Zidzachitike M’tsogolo.”) Zimene zidzachitikezo n’zosiyana kwambiri ndi zomwe anthu amene amati ndi akatswiri olosera za m’tsogolo, amanena.

Pa nkhani ya zomwe zidzachitike m’tsogoloyi tingati, tsogolo la dzikoli likudziwika kale. Tikutero chifukwa zonse zinalembedwa kale m’Baibulo, choncho mukhoza kudziwiratu zimene zidzachitike komanso mmene zidzathere. Mulungu ananena kuti: “Kuyambira pa chiyambi, . . . ndimanena za zinthu zimene sizinachitike. Ine ndiye amene ndimanena kuti, ‘Zolingalira zanga zidzachitikadi, ndipo ndidzachita chilichonse chimene ndikufuna.’” (Yesaya 46:10) Inuyo komanso anthu a m’banja lanu, mungakhale ndi tsogolo labwino. Pemphani a Mboni za Yehova kuti akambirane nanu zimene Baibulo limanena zokhudza zimene zidzachitike m’tsogolo. A Mboni si owombeza, sanena kuti amalankhula ndi Mulungu komanso sikuti ali ndi mphamvu zapadera zodziwira za m’tsogolo. Chimene chimawathandiza kudziwa zomwe zidzachitike m’tsogolo n’choti amaphunzira Baibulo mwakhama. Angakuthandizeninso inuyo kudziwa zinthu zabwino zomwe Mulungu wakonza kudzakuchitirani..