Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI KUPEMPHERA N’KOTHANDIZADI?

N’chifukwa Chiyani Anthu Amapemphera kwa Mulungu?

N’chifukwa Chiyani Anthu Amapemphera kwa Mulungu?

Kodi inuyo mumakonda kupemphera? Anthu ambiri amakonda kupemphera, ngakhalenso amene amati kulibe Mulungu. Koma kodi n’chifukwa chiyani anthu amapemphera? Kafukufuku amene anachitika ku France anasonyeza kuti mofanana ndi anthu ambiri a ku Ulaya, hafu ya anthu a m’dzikoli nthawi zina amapemphera kapena kusinkhasinkha koma osati n’cholinga chofuna kulambira Mulungu. Iwo amapemphera “n’cholinga chongofuna kuchepetsako nkhawa” kapena chifukwa choganiza kuti “pemphero liwathandiza kuti mtima wawo ukhale m’malo.” Koma palinso anthu ena amene amangopemphera kwa Mulungu zinthu zikawathina ndipo amayembekezera kuti Mulungu awathetsera mavuto awowo nthawi yomweyo.—Yesaya 26:16.

Kodi inuyo mumaiona bwanji nkhani ya pemphero? Kodi mumaganiza kuti pemphero limangomuthandiza munthu kuti ayambe kuona zinthu moyenera? Ngati mumakhulupirira Mulungu, kodi mumaona kuti kupemphera kumakuthandizani, kapena mumaona kuti mapemphero anu sayankhidwa? Baibulo lingakuthandizeni kudziwa kuti pemphero si njira yongochepetsera nkhawa, koma ndi njira yapadera yokuthandizani kuyandikira Mulungu.