Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mungathe Kukana Mayesero

Mungathe Kukana Mayesero

“Sindinkafuna kuonera zolaula. Koma nditatsegula Intaneti, mwadzidzidzi panabwera uthenga wa otsatsa malonda. Nditatsegula, ndinaona kuti pali zithunzi zolaula.”—CODY. *

“Mtsikana wina wokongola wa kuntchito kwathu anayamba kundikopa. Tsiku lina anandiuza kuti tipite kuhotelo ina tikasangalale. Ndinadziwa zoti akufuna kuti tikagonane.”—DYLAN.

“NDINGATHE kukana chilichonse kupatulapo mayesero.” Mawu amenewa akusonyeza mmene anthu ena amaonera mayesero. Iwo amaona kuti mayesero ndi chinthu chosangalatsa. Enanso amachita kulakalaka kuti aziyesedwa nthawi zonse n’cholinga choti azidzitama kuti amatha kugonjetsa mayesero. Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Tikakumana ndi mayesero, kodi tiyenera kulola kuti atigonjetse kapena ayi?

N’zoona kuti si mayesero onse amene angatibweretsere mavuto aakulu. Koma kuchita zinthu zina, makamaka zimene zingatipangitse kuchita chiwerewere, kukhoza kutibweretsera mavuto aakulu. Baibulo limachenjeza kuti: “Aliyense wochita chigololo . . . alibe nzeru mumtima mwake. Amene amachita zimenezi amawononga moyo wake.”—Miyambo 6:32, 33.

Kodi mungatani ngati mukuyesedwa kuti muchite zachiwerewere? Baibulo limanena kuti: “Mulungu akufuna kuti mukhale oyera mwa kupewa dama. Akufunanso kuti aliyense wa inu akhale woyera mwa kudziwa kulamulira thupi lake m’njira yoyera kuti mukhale olemekezeka pamaso pa Mulungu.” (1 Atesalonika 4:3, 4) Kodi mungatani kuti muzitha kukana kuchita zoipa? Ganizirani zinthu zitatu izi zimene zingakuthandizeni.

Chinthu Choyamba: Muzipewa Kuonera Zinthu Zolaula

Kuonera zolaula kungapangitse kuti muzilakalaka kuchita zoipa. Yesu anasonyeza kuti pali kugwirizana pakati pa kuona ndi kuganiza pamene ananena kuti: “Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka, wachita naye kale chigololo mumtima mwake. Tsopano ngati diso lako lakumanja limakuchimwitsa, ulikolowole ndi kulitaya.” (Mateyu 5:28, 29) Kodi pamenepa Yesu ankatanthauza chiyani? Kuti tithe kukana mayesero, tiyenera kuchita zinthu mwanzeru komanso kupewa kuonera zolaula zomwe zingatipangitse kuchita zachiwerewere.

Mukaona zolaula, yang’anani kumbali

Mwachitsanzo, tayerekezani kuti mwaona kuwala kothobwa m’maso komwe kumabwera anthu akamaotcherera  zitsulo. Kodi mungapitirizebe kuyang’ana kuwala kothobwa m’masoko? N’zokayikitsa kuti mungachite zimenezi. Mukhoza kuyang’ana kumbali kapena kutchinga maso anu ndi chinachake kuti maso anuwo asawonongeke. Mofanana ndi zimenezi, mukaona zolaula, kaya papepala, pa TV kapena munthu yemwe sanavale bwino, mungachite bwino kuyang’ana kumbali mwamsanga. Zimenezi zidzakuthandizani kuteteza maganizo anu kuti asawonongeke. Munthu wina amene anali ndi chizolowezi choonera zolaula, dzina lake Juan, anati: “Ndikaona mkazi wokongola, nthawi zambiri ndimafuna nditamuyang’ana kangapo. Koma ndimadzikakamiza kuti ndiyang’ane kumbali ndipo ndimadziuza kuti: ‘Pemphera kwa Yehova ndipo ukufunika kuchita zimenezi panopa.’ Ndikangopemphera, maganizo onse oipa amathera pompo.”—Mateyu 6:9, 13; 1 Akorinto 10:13.

Mungachitenso bwino kuganizira chitsanzo cha Yobu, amene anali munthu wokhulupirika. Iye anati: “Ndachita pangano ndi maso anga. Choncho ndingayang’anitsitse bwanji namwali?” (Yobu 31:1) Inunso mungachite chimodzimodzi.

Tayesani izi: Ngati mwaona zolaula, mwansanga yang’anani kumbali. Mungachite bwino kutengera chitsanzo cha munthu wina amene analemba nawo Baibulo. Iye anapemphera kuti: “Chititsani maso anga kuti asaone zinthu zopanda pake.”—Salimo 119:37.

Chinthu Chachiwiri: Musamaganizire Zinthu Zoipa

Chifukwa choti ndife opanda ungwiro, nthawi zina tikhoza kumaganiza zinthu zoipa. Baibulo limanena kuti: “Munthu aliyense amayesedwa mwa kukopedwa ndi kukodwa m’chilakolako chake. Ndiye chilakolako chikatenga pakati, chimabala tchimo.” (Yakobo 1:14, 15) Mukayamba kuganiza zinthu zoipa, kodi mungatani kuti musapitirize kuganiza zinthu zimenezo?

Maganizo oipa akakubwererani, siyani kuganizira zimenezo nthawi yomweyo ndipo pempherani

Ngati mukuganizira zinthu zoipa, dziwani kuti mungathe kusankha ngati mukufuna muziganizirabe zinthuzo kapena ayi. Yesetsani kulimbana ndi maganizo amenewa. Zichotseni mumtima mwanu ndipo musamaziganizirenso. Munthu wina dzina lake Troy, amene ankakonda kuonera zolaula pa Intaneti, ananena kuti: “Ndinkayesetsa kuchotsa maganizo alionse olakwika mumtima mwanga n’kumaganizira zinthu zabwino. Kuchita zimenezi sikunali kophweka moti nthawi  zina ndinkatha kuyambiranso kuganizira zinthu zimenezi. Koma m’kupita kwa nthawi, ndinagonjetsa vutoli.” Mayi wina dzina lake Elsa, yemwe ali mtsikana anali ndi vuto lofuna kuchita chiwerewere, ananena kuti: “Kuchita zinthu zosiyanasiyana komanso kupemphera kwa Yehova ndi kumene kunkandithandiza kuchotsa maganizo oipa.”

Tayesani izi: Mukayamba kuganizira zinthu zoipa, nthawi yomweyo yesetsani kusiya kuganizira zimenezo ndipo kenako pempherani. Yesetsani kuganizira “zinthu zilizonse zoona, zilizonse zofunika kwambiri, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zachikondi, zilizonse zoyamikirika, khalidwe labwino lililonse, ndi chilichonse chotamandika.”—Afilipi 4:8.

Chinthu Chachitatu: Muzipewa Kuchita Zinthu Zimene Zingakupangitseni Kuchita Zinthu Zoipa

Munthu amene amalakalaka kuchita zoipa, akayesedwa kuti achite zoipazo ndipo wapeza mpata woti angathe kuchita zoipa, akhoza kuchitadi zoipazo. (Miyambo 7:6-23) Kodi mungatani kuti zimenezi zisakuchitikireni?

“Ndimagwiritsa ntchito Intaneti ngati panyumba pali anthu ena”

Baibulo limachenjeza kuti: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala, koma anthu osadziwa zinthu amangopitabe ndipo amalangidwa.” (Miyambo 22:3) Choncho muyenera kupewa zinthu zimene zingakupangitseni kuti muchite zoipa. Muzikhala tcheru ndi zinthu zimene zingakubweretsereni mavuto, n’kumazipewa. (Miyambo 7:25) Bambo wina dzina lake Filipe, yemwe anagonjetsa vuto loonera zolaula, anati: “Ndimaika kompyuta pamalo oonekera kuti aliyense azitha kuona zimene ndikuchita komanso ndinaika pulogalamu ya pa kompyuta imene imakuuza kuti malo amene ukufuna kutsegula ali ndi zithunzi zolaula. Ndimagwiritsa ntchito Intaneti ngati panyumba pali anthu ena.” Troy, amene tamutchula koyambirira uja nayenso anati: “Ndimapewa kuonera filimu iliyonse imene ili ndi zolaula komanso ndimapewa kucheza ndi anthu amene amakonda kulankhula nkhani zokhudza kugonana. Sindifuna kuchita zinthu zimene zingandigwetse m’mavuto.”

Tayesani izi: Muzidzifufuza moona mtima ngati muli ndi vuto pa nkhani yoonera zolaula ndipo muzipewa kuchita zinthu zimene zingakupangitseni kuti muchite zolakwika.—Mateyu 6:13.

MUSATAYE MTIMA

Koma bwanji ngati mukuyesetsa kuthetsa vuto lanu, koma mukulephera? Musataye mtima n’kusiya kulimbana ndi vutolo. Baibulo limati: “Wolungama akhoza kugwa ngakhale nthawi 7 ndipo ndithu adzadzukanso.” (Miyambo 24:16) Atate wathu wakumwamba amatilimbikitsa kuti tikagwa ‘tizidzuka.’ Kodi mumafuna kuti Mulungu akuthandizeni? Ngati mumafuna kuti akuthandizeni, musasiye kupemphera kwa iye. Muzilimbitsa chikhulupiriro chanu pophunzira Mawu ake komanso kupita kumisonkhano ya Mboni za Yehova. Muzikhulupirira mawu a Mulungu akuti: “Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza.”—Yesaya 41:10.

Cody, amene tamutchula koyambirira uja, anati: “Ndinkafunika kuchita khama kwambiri kuti ndithetse chizolowezi changa choonera zolaula. Nthawi zina ndinkabwerezanso kuchita khalidweli koma Mulungu anandithandiza kulithetsa.” Dylan, yemwenso tamutchula koyambirira kwa nkhani ino, ananena kuti: “Ndinangotsala pang’ono kuchita zachiwerewere ndi munthu amene ndinkagwira naye ntchito. Koma ndinatsimikizira mkaziyo kuti sindikufuna kuchita naye zachiwerewere. Ndimasangalala chifukwa chokhala ndi chikumbumtima choyera. Komanso ndimasangalala chifukwa chodziwa kuti Yehova amandinyadira chifukwa cha khalidwe langa labwino.”

Ngati mutamayesetsa kupewa kuchita zoipa, nanunso Mulungu angamakunyadireni chifukwa cha khalidwe lanu labwino.—Miyambo 27:11.

^ ndime 2 Tasintha mayina m’nkhaniyi.