Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi aloye amene ankagwiritsidwa ntchito kale anali chiyani?

Mitengo imene matabwa ake ankapangira aloye

Baibulo limanena kuti aloye ankagwiritsidwa ntchito ngati mafuta onunkhiritsa zovala komanso pabedi. (Salimo 45:8; Miyambo 7:17; Nyimbo ya Solomo 4:14) Aloye wotchulidwa m’Baibulo ankapangidwa kuchokera ku matabwa a mtengo winawake. Matabwa a mtengowu akayamba kuwola, ankatulutsa utomoni ndi mafuta enaake. Matabwa oterewa ankawapera n’kukhala ngati ufa, womwe unkatchedwa kuti “aloye,” ndipo ankaugulitsa.

Baibulo limati malo okhala a Aisiraeli anali “ngati mitengo ya aloye imene Yehova anabzala.” (Numeri 24:5, 6) N’kutheka kuti apa akunena za mtengo umene ankapangira aloye womwe unkakhala wautali pafupifupi mamita 30 ndipo unkakhala ndi nthambi zambirimbiri zopita m’mbali. Ngakhale kuti mitengoyi siipezekanso ku Israel masiku ano, buku lina linanena kuti “n’zosakayikitsa kuti mitengo imeneyi komanso ina yomwe panopa kulibe kuderali, inkapezeka yambiri mphepete mwa mtsinje wa Yorodano.”—A Dictionary of the Bible.

Kodi ndi nsembe zotani zimene zinali zovomerezeka pakachisi ku Yerusalemu?

Kanthu kadongo kamene kanapezeka kukachisi wa ku Yerusalemu, kanapangidwa zaka 2,000 zapitazo

Chilamulo cha Mulungu chinkati nsembe zonse zoperekedwa pakachisi zizikhala zabwino kwambiri. Mulungu sankalandira nsembe za nyama zachilema kapena zodwala. (Ekisodo 23:19; Levitiko 22:21-24) Wolemba mabuku wina wachiyuda wa m’nthawi ya atumwi, dzina lake Philo, ananena kuti ansembe ankaiyang’ana nyama iliyonse “kuchokera kuphazi mpaka kumutu,” pofuna kutsimikiza kuti nyamayo “ilibe chilema chilichonse komanso siikudwala.”

Katswiri wina, dzina lake E. P. Sanders, ananena kuti n’kutheka kuti akuluakulu a pakachisi “ankachita kusankha anthu oti azigulitsa nyama zoperekedwa nsembe, ndipo nyama zake zinkakhala zokhazo zimene ansembe azivomereza. Ogulitsa nyamawo ankapereka kwa wogula, kanthu kenakake kopangidwa ndi dongo kooneka ngati ndalama yachitsulo, monga umboni wosonyeza kuti nyamayo ndi yovomerezeka.”

Mu 2011, akatswiri ofukula zinthu zakale, anapeza kanthu kopangidwa ndi dongo kameneka, pafupi ndi kachisi. Kanthu kameneka kakusonyeza kuti ndi kakale kwambiri, isanafike 70  C.E. Kanthuka kankakhala ndi mawu achiaramu amene akatswiri ena anawamasula kuti “Yoyenera Kuperekedwa kwa Mulungu.” Anthu ena amanena kuti akuluakulu a pakachisi ankakoleka tizinthu timeneti ku zinthu zogwiritsidwa ntchito pa miyambo inayake kapena ku nyama zokaperekedwa nsembe.