Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE OWERENGA AMAFUNSA . . .

N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Osauka Aziponderezedwa?

N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Osauka Aziponderezedwa?

M’Baibulo muli nkhani zingapo zonena za anthu amphamvu omwe ankapondereza anthu wamba. Chitsanzo cha nkhani zoterezi ndi nkhani ya Naboti. * Ahabu, yemwe anali mfumu ya Isiraeli cha m’ma 900 B.C.E., analola kuti mkazi wake, Yezebeli, akonze chiwembu chopha Naboti ndi ana ake. Yezebeli anachita zimenezi n’cholinga choti Ahabu atenge munda wa mpesa wa Naboti. (1 Mafumu 21:1-16; 2 Mafumu 9:26) N’chifukwa chiyani Mulungu analola kuti zimenezi zichitike, komwe kunali kugwiritsa ntchito mphamvu molakwa?

“Mulungu . . . sanganame.”—Tito 1:2

Chifukwa choyamba n’chakuti: Mulungu sanganame. (Tito 1:2) Kodi mfundo imeneyi ikugwirizana bwanji ndi zimene Mulungu amachita polola kuti anthu osauka aziponderezedwa? Dziwani kuti pa chiyambi penipeni, Mulungu anachenjeza anthu kuti akapanda kumvera malamulo ake, zotsatira zake zidzakhala imfa. Kungoyambira pamene anthu oyamba anapandukira Mulungu m’munda mwa Edeni, anthu akhala akuvutika ndi imfa ndipo izi zikusonyeza kuti zimene Mulungu ananena zinachitikadi. Munthu woyamba kufa anali Abele, ndipotu Kaini, mkulu wake, ndi amene anamupha.—Genesis 2:16, 17; 4:8.

Ponena za zimene zakhala zikuchitika m’mbiri yonse ya anthu kuyambira nthawi imeneyi, Mawu a Mulungu amati: “Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.” (Mlaliki 8:9) Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti nthawi zambiri anthu ena amapondereza anzawo? Mulungu anachenjeza Aisiraeli kuti mafumu awo azidzawapondereza ndipo iwo azidzalirira Yehova kuti awapulumutse. (1 Samueli 8:11-18) Nayonso Mfumu Solomo inkapondereza anthu ake powalipiritsa msonkho wokwera kwambiri. (1 Mafumu 11:43; 12:3, 4) Koma panalinso mafumu ena a Isiraeli, monga Ahabu, amene ankapondereza anthu kuposa pamenepa. Komano taganizirani izi: Mulungu akanati aziletsa zinthu zimenezi kuti zisamachitike, kodi sizikanapangitsa kuti mawu ake aja akhale abodza?

“Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.”—Mlaliki 8:9

Kumbukiraninso kuti Satana ananena kuti anthu amatumikira Mulungu chifukwa chongofuna kuti Mulunguyo aziwathandiza. (Yobu 1:9, 10; 2:4) Mulungu akanati aziteteza atumiki ake ku mavuto onse amene amakumana nawo, kodi zimene Satana ananenazi sizikanaoneka ngati zoona? Komanso Mulungu akanati aziteteza aliyense kuti asaponderezedwe, anthu ambiri akanaganiza kuti anthu akhoza kumadzilamulira okha bwinobwino popanda Mulungu. Komatu Mawu a Mulungu amasonyeza kuti zimenezi sizingatheke chifukwa anthu sangathe kumalamulirana, zinthu zonse n’kumayenda bwinobwino. (Yeremiya 10:23) Pakufunika kuti Ufumu wa Mulungu uyambe kulamulira dzikoli chifukwa ndi umene ungathetse kupanda chilungamo.

Kodi zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu sachita chilichonse anthu akamaponderezedwa? Ayi. Taganizirani zinthu ziwiri izi zimene amachita: Choyamba, amaulula zinthu zopanda chilungamo zimene anthu oipa amachita. Mwachitsanzo, Mawu ake, Baibulo, amafotokoza za chiwembu chonse chimene Yezebeli anakonzera Naboti. Baibulo limatiuzanso kuti pali wina wamphamvu amene amachititsa kuti zinthu zopanda chilungamo ngati zimenezi zizichitika, koma amafuna kuti anthu asamuzindikire. (Yohane 14:30; 2 Akorinto 11:14) Baibulo limanena kuti iye ndi Satana Mdyerekezi. Kudziwa zimenezi kumatithandiza kuti tizipewa kuchita zinthu zopanda chilungamo kapena zopondereza ena. Choncho tingati Mulungu amatithandiza kuti tizipewa kuchita zinthu zoipa kuti tidzapeze moyo wosatha.

Chachiwiri, Mulungu amatilonjeza kuti adzathetsa kuponderezana. Zimene anachita poulula chiwembu cha Ahabu ndi Yezebeli, komanso chilango chimene anawapatsa iwowo ndiponso anthu ena oipa, zimatithandiza kukhulupirira kuti adzakwaniritsadi lonjezo lake lowononga anthu oipa. (Salimo 52:1-5) Mulungu amalonjezanso kuti adzakonza mavuto onse amene akhalapo chifukwa cha zinthu zopanda chilungamo zimene anthu amachita. * Choncho Naboti, yemwe anali wokhulupirika, komanso ana ake, adzaukitsidwa ndipo adzakhala ndi moyo wosangalala m’dziko lapansi la paradaiso mmene simudzakhalanso zinthu zopanda chilungamo.—Salimo 37:34.

^ ndime 3 Onani nkhani yakuti, “Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo,” patsamba 12 mpaka 15.