Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MBIRI YA MOYO WANGA

Ndinasankha Kutumikira Yehova Moyo Wanga Wonse

Ndinasankha Kutumikira Yehova Moyo Wanga Wonse

Nditamaliza sukulu ku sekondale mu January 1937, ndinayamba kuphunzira pa yunivesite ina ku America. Koma ndinkafunikanso kugwira ntchito kuti ndizipeza ndalama zolipirira sukuluyi, ndipo izi zinkachititsa kuti ndizikhala wotanganidwa kwambiri. Kuyambira ndili mnyamata, ndinkafuna kuphunzira kamangidwe ka nyumba zitalizitali komanso milatho ikuluikulu.

Dziko la America linayamba kuchita nawo nkhondo yachiwiri ya padziko lonse chakumayambiriro kwa 1942. Pa nthawiyi n’kuti ndili m’chaka chomaliza cha maphunziro anga a zomangamanga ndipo kunali kutangotsala miyezi yowerengeka kuti ndilandire digirii. Ndinkakhala ndi anyamata ena awiri. Tsiku lina mmodzi mwa anyamatawa anandiuza kuti ndikumane ndi John O. (Johnny) Brehmer, yemwe ankakonda kucheza ndi anyamata ena omwe ankakhala m’chipinda china chapansi. John anali wa Mboni za Yehova ndipo ndinadabwa kuona mmene ankayankhira funso lililonse pogwiritsa ntchito Baibulo. Pochita chidwi ndi zimenezi ndinayamba kuphunzira naye Baibulo, ndipo kenako ndikapeza mpata ndinkatsagana naye akamapita kolalikira.

Bambo ake a John, a Otto, anakhala a Mboni za Yehova pa nthawi imene anali pulezidenti wa banki ina ku Walnut, Iowa. Abambo akewa anasiya ntchitoyi n’cholinga choti azikhala ndi nthawi yambiri yolalikira nthawi zonse. Patapita nthawi chitsanzo chawo komanso cha anthu a m’banja lawo chinandilimbikitsa kwambiri kuti nanenso ndiyambe kutumikira Yehova.

NDINAFUNIKA KUSANKHA ZOCHITA

Tsiku lina mkulu wina wa pa yunivesite yathu anandiuza kuti sindikuchitanso bwino m’kalasi ndipo zimenezi zilepheretsa kuti ndilandire digirii. Ndikukumbukira kuti atandiuza zimenezi, ndinapemphera kwa Yehova Mulungu kumupempha kuti andithandize kusankha zochita. Pasanapite nthawi yaitali, ndinaitanidwa kuti ndikakumane ndi pulofesa wina wa zomangamanga. Anandiuza kuti anali atalandira telegalamu yomupempha kuti apeze munthu wodziwa zomangamanga ndipo pulufesayo anali atayankha kuti ineyo ndingakagwire ntchito imeneyo. Ndinamuyamikira chifukwa chondiganizira, komabe ndinam’fotokozera kuti ndasankha kuti ntchito yanga ikhale kutumikira Yehova moyo wanga wonse. Pa June 17, 1942, ndinabatizidwa ndipo pasanapite nthawi ndinaikidwa kukhala mpainiya, dzina limene limapatsidwa kwa a Mboni za Yehova amene amalalikira nthawi zonse.

Kenako mu 1942, ndinalandira kalata yondiitana kuti ndikaphunzire zausilikali. Ndinafotokozera akuluakulu amene anandiitanawo kuti sindikanatha kupita kukaphunzira zimenezi chifukwa zinali zosiyana ndi zimene ndimaphunzira m’Baibulo. Ndinawapatsa zikalata zokhudza mbiri yanga yabwino zimene mapulofesa anandilembera ndiponso analembamo zoti ndili ndi luso pa ntchito ya zomangamanga. Koma zonsezi sizinathandize, ndipo pamapeto pake anandilipiritsa ndalama zokwana madola 10,000 a ku America komanso anandiuza kuti ndikakhale m’ndende kwa zaka 5.

 MOYO WA KUNDENDE

Achinyamata okwana 230 tinaikidwa m’ndendeyi, yomwe panopa imaoneka chonchi

Kundende imeneyi ndinapezako anyamata a Mboni okwana 230 omwe ankagwira ntchito pafamu ina ya ndendeyi. Pafamuyi m’pamene ankatipatsirapo ntchito yoti tigwire ndipo pankakhala asilikali ambiri amene ankatiyang’anira. Ambiri mwa asilikaliwa ankadziwa kuti a Mbonife sitichita nawo ndale ndipo ankalemekeza maganizo athu.

Asilikali ena ankatilola kuti tizichita misonkhano yathu m’ndendemo. Ankatithandizanso kupeza mabuku athu. Msilikali wina anafika mpaka polembetsa kuti azilandira magazini ya Consolation (yomwe pano imadziwika kuti Galamukani!).

NDINATULUTSIDWA N’KUYAMBA UMISHONALE

Nditakhala m’ndende kwa zaka zitatu, ndinatuluka pa February 16, 1946, patangopita miyezi yochepa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itatha. Pasanapite nthawi, ndinayambanso kugwira ntchito yolalikira nthawi zonse. Malo amene ndinauzidwa kuti ndizikalalikira anali dera limene kunali ndende ija. Ndinachita mantha kwambiri chifukwa kuderali anthu ambiri ankadana ndi Mboni za Yehova. Komanso kuderali ntchito zinali zosowa kwambiri ndiponso kupeza malo okhala kunali kovuta.

Ndikukumbukira kuti tsiku lina ndikulalikira, mlonda wa nyumba ina anandikalipira pondiuza kuti, “Choka pano!” Nditaona chibonga chimene chinali m’manja mwake, ndinachita mantha ndipo ndinachoka mwamsanga. Nditafika panyumba ina, mzimayi wina anandiuza kuti, “Tandidikirani pang’ono,” kenako anatseka chitseko. Ndinamuyembekeza kwa kanthawi koma kenako mzimayiyo anatsegula windo la chipinda cham’mwamba, n’kundikhuthulira madzi oti atsukira mbale. Ngakhale kuti ndinkakumana ndi mavuto onsewa, ndinkapeza madalitso ambiri pa ntchito yanga yolalikirayi. Patapita nthawi ndinamva kuti anthu ena amene ndinawapatsa mabuku athu anakhala a Mboni.

M’chaka cha 1943 ku New York, kunakhazikitsidwa sukulu ya amishonale. Kenako sukuluyi inayamba kudziwika kuti Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo. Ndinaitanidwa ku sukuluyi ndipo ndinamaliza maphunziro anga pa February 8, 1948. Nditamaliza maphunzirowa ananditumiza ku Gold Coast, lomwe pano ndi dziko la Ghana.

Nditafika ku Gold Coast, ntchito yanga inali yolalikira akuluakulu a boma komanso azungu. Loweruka ndi Lamlungu, ndinkalalikira limodzi ndi a Mboni za Yehova a mumpingo mwathu n’kumawathandiza kulalikira kunyumba ndi nyumba. Ndinkapitanso kumadera ena komwe kunali a Mboni ochepa, ndipo ndinkawaphunzitsa mmene angagwirire ntchito yolalikira. Komanso ndinayamba kuyendera mipingo yomwe inali pafupi ndi dziko la Ivory Coast, lomwe pano ndi Côte d’Ivoire.

Pamene ndinkatumikira m’madera amenewa ndinaphunzira kuchita zinthu ngati mmene anthu a ku Africa amachitira. Ndinkagona m’nyumba yozira, kudya ndi manja komanso kupita kutchire kukakumba ndikafuna  kudzithandiza ngati mmene Aisiraeli ankachitira. (Deuteronomo 23:12-14) Zimenezi zinachititsa kuti mbiri yanga komanso ya amishonale anzanga ikhale yabwino. Tinkaphunzira Baibulo ndi akazi a akuluakulu ena a boma. Izi zinathandiza pa nthawi imene anthu ena otsutsa ankafuna kuti boma lilande zikalata zathu zokhalira m’dzikomo. Akaziwa ankaumiriza amuna awo kuti asavomereze zimenezo.

Monga zimakhalira ndi amishonale ambiri a ku Africa, nanenso ndinadwala malungo kangapo konse. Ndikukumbukira kuti pa nthawi ina malungo atandipanikiza kwambiri ndinkafunika kugwira chibwano changa kuti chisamanjenjemere kwambiri. Komabe ndinapitirizabe kusangalala ndi ntchito yanga yolalikira.

Pa zaka zinayi zoyambirira zomwe ndinali ku Africa, ndinkalemberana makalata ndi mtsikana wina, dzina lake Eva Hallquist, amene ndinakumana naye ndisanachoke ku America. Eva anandiuza kuti akumaliza maphunziro a kalasi ya nambala 21 ya Sukulu ya Giliyadi pa July 19, 1953 pamsonkhano womwe unachitikira ku New York, pasitediyamu ya Yankee. Ndinakambirana ndi mkulu woyendetsa sitima yopita ku America kuti ndikwere nawo sitima yawo ndipo ndizigwira ntchito m’sitimayo n’cholinga choti asandilipiritse pa ulendowu.

Ulendowu unatenga masiku 22 ndipo unali wovuta. Kenako ndinafika ku likulu la Mboni za Yehova ku Brooklyn komwe ndinakumana ndi Eva. Tili pamalo ena ofikira sitima zapamadzi mumzinda wa New York, ndinafunsa Eva ngati angavomere kuti tidzakwatirane. Kenako tinakwatiranadi, ndipo tonse tinayamba kukhala ku Gold Coast.

KUSAMALIRA MAKOLO KOMANSO MKAZI WANGA

Titatumikira ku Africa kwa zaka zambiri, ndinalandira kalata kuchokera kwa mayi anga yondidziwitsa kuti bambo akudwala khansa. Tinapempha ku ofesi ya Mboni za Yehova ya m’dzikoli kuti ine ndi Eva tikasamalire bambowo. Matendawa anakula kwambiri ndipo pasanapite nthawi yaitali bambowo anamwalira.

Tinakumana ndi mfumu ina ku Gold Coast, komwe panopa ndi ku Ghana

Tinabwereranso ku Ghana ndipo patangotha zaka pafupifupi 4, tinamvanso kuti amayi akudwala kwambiri. Anzathu ena anatiuza kuti zingakhale bwino titabwerera ku America kuti tikasamalire amayi, ngakhale kuti kuchita zimenezi kunali kovuta kwambiri. Panali patatha zaka 15 ndikuchita utumiki waumishonale, ndipo zaka 11 pa zaka zimenezi ndinachita limodzi ndi mkazi wanga.

Kwa zaka zambiri, tinkasinthana kusamalira mayi ndipo tinkawathandiza kupita ku misonkhano yathu akakhala kuti angakwanitse. Mayi anamwalira pa January 17, 1976 ali ndi zaka 86. Koma patatha zaka 9 tinakumananso ndi vuto lina lalikulu. Eva anapezekanso ndi matenda a khansa. Tinayesetsa kulimbana ndi matendawa koma sizinaphule kanthu moti pa June 4, 1985, Eva anamwalira ali ndi zaka 70.

ZOCHITIKA ZINA ZOSANGALATSA

Mu 1988, ndinaitanidwa kuti ndikakhale nawo pamwambo wotsegulira ofesi ya Mboni za Yehova ku Ghana. Unali mwambo wosangalatsa kwambiri. Zaka 40 m’mbuyomo pamene ndinafika ku Ghana nditangochoka kusukulu ya Giliyadi, kunali Mboni za Yehova zosakwana 1,000. Koma pomafika mu 1988, m’dzikoli munali a Mboni okwana 34,000, ndipo panopa muli a Mboni okwana 114,000.

Patatha zaka ziwiri kuchokera pamene ndinapita ku Ghana, pa August 6, 1990 ndinakwatira Betty Miller, yemwe anali mnzake kwambiri wa Eva. Ine ndi mkazi wangayu timaonabe kuti kutumikira Yehova ndiye ntchito yathu yaikulu. Tikuyembekezera kudzakumana ndi agogo, makolo athu komanso Eva akadzaukitsidwa m’Paradaiso.—Machitidwe 24:15.

Ndimasangalala kwambiri ndikaganiza mwayi umene ndakhala nawo wogwiritsidwa ntchito ndi Yehova kwa zaka zoposa 70. Ndimamuthokoza chifukwa chondilola kumutumikira kwa moyo wanga wonse. Ngakhale kuti panopa ndili ndi zaka zoposa 90, Yehova, yemwe ndi katswiri pa zomangamanga, akupitirizabe kundipatsa mphamvu komanso kundilimbikitsa kuti ndizimutumikirabe.