Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | MABODZA OMWE AMALEPHERETSA ANTHU KUKONDA MULUNGU

Zimene Zimapangitsa Anthu Ena Kuti Asamakonde Mulungu

Zimene Zimapangitsa Anthu Ena Kuti Asamakonde Mulungu

“‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.’ Limeneli ndilo lamulo lalikulu kwambiri komanso loyamba.”Ananena mawu amenewa ndi Yesu Khristu, mu 33 C.E. *

Anthu ena zimawavuta kukonda Mulungu chifukwa amaona kuti ndi wosamvetsetseka, wankhanza komanso sakhudzidwa ndi mavuto a anthu. Taonani zimene ena ananena:

  • “Ndinkapemphera kwa Mulungu kuti andithandize. Koma pa nthawi yomweyonso ndinkaona kuti iye sakhudzidwa ndi mavuto a anthu ndipo sangamve mapemphero anga. Ndinkaona kuti Mulungu si weniweni.”—Marco, Italy.

  • “Ndinkafuna kutumikira Mulungu, koma ndinkaona kuti saganizira n’komwe za ine. Ndinkaonanso kuti iye ndi Mulungu wankhanza amene amangofuna kutilanga basi. Ndinkaganiza kuti alibe chikondi.”—Rosa, Guatemala.

  • “Ndili mwana, ndinkakhulupirira kuti Mulungu amangofufuza zolakwa zathu n’cholinga choti atilange. Kenako ndinayamba kumuona kuti ndi wapamwamba kwambiri moti sindingakhale naye pa ubwenzi. Ndinkaona kuti Mulungu ali ngati pulezidenti amene amalowerera nkhani za anthu amene amawalamulira, koma alibe nawo chidwi chenicheni.”—Raymonde, Canada.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi Mulungu ndi wopanda chikondi? Akhristu akhala akudzifunsa funso limeneli kwa zaka zambirimbiri. Ndipotu m’zaka za m’ma 500 mpaka m’ma 1500 anthu ambiri a m’matchalitchi amene amati ndi achikhristu sankapemphera kwa Mulungu Wamphamvuyonse chifukwa ankachita naye mantha kwambiri. Wolemba mbiri wina, dzina lake Will Durant, analemba kuti: “Zingatheke bwanji kuti munthu wochimwa alimbe mtima kupemphera kwa Mulungu, yemwe ndi woopsa komanso ali kutali kwambiri ndi anthu?”

Koma kodi n’chiyani chinachititsa kuti anthu aziona kuti Mulungu ndi ‘woopsa komanso ali nawo kutali kwambiri?’ Kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani zokhudza Mulungu? Nanga kodi kuphunzira zoona zokhudza Mulungu kungakuthandizeni kuti muzimukonda kwambiri?